bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 17
Deuteronomy 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 18 →
1
Musadzapereke ng'ombe kapena nkhosa yachilema ngati nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu. Musadzapereke nyama iliyonse yopunduka, chifukwa Mulungu wanu amadana nazo zimenezi.
2
Mwina padzapezeka kuti mu mzinda wina umene Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani, muli munthu wina wamwamuna kapena wamkazi amene wachimwira Chauta, Mulungu wanu,
3
naphwanya chipangano chake, popembedza ndi kutumikira milungu ina, monga dzuŵa, mwezi kapena nyenyezi, zimene ndidaletsa kuti asazipembedze.
4
Mukamva kuti chinthu chotere chachitika, mufufuze bwino nkhani imeneyo, ndipo mukapeza kuti choipa choterechi chachitikadi mu Israele,
5
mumgwire mwamunayo kapena mkaziyo ndi kupita naye ku zipata za mzinda wanu ndipo mumphere kunja kwa mzinda pakumponya miyala.
6
Munthuyo aphedwe pokhapokha patapezeka mboni ziŵiri kapena zitatu. Asaphedwe chifukwa cha umboni wa munthu mmodzi yekha.
7
Ziyambe ndi mbonizo kuponya miyala. Pambuyo pake anthu onse amponye miyala munthuyo. Motero chinthu choipacho mudzachichotsa pakati panu.
8
Milandu yophana, yolimbirana zinthu, kapena yopwetekana m'mizinda mwanu, ikaŵavuta aweruzi anu, mupite ku malo achipembedzo aja osankhidwa ndi Chauta, Mulungu wanu,
9
ndipo mupereke mlandu wanuwo kwa ansembe Achilevi ndi kwa muweruzi amene ali pa ntchito pa nthaŵi imeneyo. Ndipo iwowo agamule mlanduwo.
10
Iwowo atagamula, inu muyenera kungochita zomwe akuuzani ku malo osankhidwa ndi Chauta.
11
Muvomere chiweruzo chao, ndipo mutsate malangizo ao onse, osapotokera kumanja kapena kumanzere.
12
Aliyense wosamvera wansembe amene akutumikira Chauta, Mulungu wanu, kapena wosamvera muweruzi, aphedwe. Mwa njira imeneyi mudzachotsa choipa pakati pa Aisraele.
13
Tsono aliyense amene adzamve zimenezi adzakhala ndi mantha, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzafune kuchitanso zotere.
14
Mutaloŵa ndi kukhazikika m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsenilo, ndipo mukadzafuna kuti mukhale ndi mfumu monga ili nayo mitundu ina yozungulira,
15
mfumu imeneyo idzakhale munthu wosankhidwa ndi Chauta, Mulungu wanu. Adzakhale munthu wa mtundu wanu. Musadzasankhe mlendo kuti akhale mfumu yanu, ameneyo si mbale wanu.
16
Mfumuyo isadzakhale ndi akavalo ambiri ndipo isadzatume anthu ku Ejipito kukagula akavalo, popeza kuti Chauta adakuuzani kuti, “Musadzabwererenso kumeneko.”
17
Mfumu isadzakhale ndi akazi ambiri kuti mtima wake ungadzapotoke. Ndipo isadzadzikundikire siliva ndi golide wambiri.
18
Munthuyo ataloŵa mu ufumu wakewo, adzalembe m'buku lakelake malamulo a Mulunguŵa ochokera mu buku la malamulo limene lili m'manja mwa ansembe Achilevi.
19
Buku limeneli adzalisunge ndipo azidzaŵerengamo pa moyo wake wonse, kuti adzaphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wake, pakutsata mokhulupirika zonse zolembedwa m'bukumo.
20
Zimenezi zidzamthandiza kudziŵa kuti iyeyo saposa Aisraele anzake, ndiponso kuti sayenera kukhala wonyozera malamulo a Chauta mpang'ono pomwe. Motero iyeyo, pamodzi ndi zidzukulu zake zomwe, adzalamulira nthaŵi yaitali mu Israele.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34