bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 21
Deuteronomy 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 22 →
1
M'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani kuti likhale lanulanu mwina mwake mungathe kupeza munthu wakufa m'munda, inu osadziŵa amene wamupha.
2
Akuluakulu anu ndi aweruzi anu apiteko, ndipo akayese kutalika kwake kuchokera pamalo pamene pali munthu wakufayo mpaka ku mizinda yoyandikana ndi malowo.
3
Pamenepo akuluakulu a mudzi woyandikana kwambiri ndi pamene pali mtembopo, asankhe ng'ombe imene sidagwirepo ntchito, ndipo sidakokepo galeta.
4
Ng'ombeyo apite nayo kudambo kumene kuli madzi oyenda. Malowo akhale akuti munthu sadalimepo nkale lonse kapena kubzalapo kanthu. Kumeneko akaithyole khosi ng'ombeyo.
5
Ansembe Achilevi apitekonso kumeneko, chifukwa ndiwo amene ayenera kumaweruza milandu yonse ya ndeu ndi ya kupha. Chauta, Mulungu wanu, wasankha iwowo kuti akhale atumiki ake, ndiponso kuti azidalitsa m'dzina lake.
6
Tsono atsogoleri onse ochokera ku mudzi wa pafupi ndi pamene panali munthu wophedwayo, asambe m'manja pamwamba pa ng'ombe ija imene adaithyola khosi m'dambo muja.
7
Ndipo anene kuti, “Sindife tidamupha munthuyu, ndipo amene adamupha sitidamuwone.
8
Inu Chauta, khululukirani anthu anu Aisraele amene mudaŵaombola. Tikhululukireni ndipo musaike pa ife tchimo la kupha munthu wosalakwayu.”
9
Mukachita zimene Chauta afuna, Iyeyo sadzakuzengani mlandu woti mwapha munthu wosalakwa.
10
Chauta, Mulungu wanu, akakupambanitsani pa nkhondo, mungathe kugwirapo akapolo kunkhondoko.
11
Mwina pakati pa akapolowo inu nkuwona mkazi wokongola amene mwamkonda, ndipo mufuna kumkwatira.
12
Pita nayeni kwanu, ndipo mkaziyo amete kumutu, ndi kutseteka makadabo ake,
13
ndipo asinthe zovala. Akhale m'mudzi mwanu mwezi wathunthu, ndipo alire maliro kulira makolo ake. Tsono atatha zimenezi, mumkwatire.
14
Pambuyo pake mutaona kuti simukumfunanso, mumleke, apite mwaufulu kumene akufuna. Simungathe kumuyesanso kapolo kapena kumgulitsa, chifukwa mudakhala naye malo amodzi.
15
Tiyese kuti munthu ali ndi akazi aŵiri, wina wokondedwa kwambiri wina pang'ono, onsewo nkubala ana aamuna, mwana woyamba kubadwa nakhala wa mkazi amene amamkonda pang'ono.
16
Munthuyo akatsimikiza zoti agaŵire ana akewo chuma chake, asakondere mwana wa mkazi wokondedwa koposayo, pakumpatsa gawo la mwana woyamba.
17
Mwana wake woyamba kubadwa uja ampatse moŵirikiza, ngakhale kuti ndi mwana amene mai wake ndi wokondedwa pang'ono. Munthu ayenera kuvomera mwana wake woyamba, ndi kumpatsa gawo limene lili lake potsata lamulo.
18
Tiyese kuti wina ali ndi mwana wokanika ndiponso wachipongwe, mwana woti bambo ndi mai ake saŵamvera konse, ngakhale amlange chotani.
19
Makolo ake a mwanayo amgwire ndi kupita naye kwa akuluakulu amumzinda ku chipata cha mzindawo.
20
Makolowo auze akuluakuluwo kuti, “Mwana wathu ndi wokanika ndipo ndi wachipongwe safuna kutimvera, ndi wadyera ndiponso chidakwa.
21
Pamenepo anthu amumzindawo amuphe pakumponya miyala, motero mudzachotsa choipa pakati panu. Anthu onse a mu Israele muno akadzamva zimene zachitikazi, adzakhala ndi mantha.”
22
Munthu akaphedwa chifukwa cha mlandu, ndipo mtembo wake ndi wopachikidwa pa mtengo,
23
mtembowo usagonere pamtengopo. Uikidwe tsiku lomwelo, chifukwa kuti mtembo ugonerere pamtengo ndi chinthu chobweretsa matemberero a Mulungu. Kwirirani mtembowo, kuwopa kuti mungaipitse dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34