bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 23
Deuteronomy 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 24 →
1
Mwamuna aliyense wofulidwa, kapena woduka chiwalo chaumuna, asaloŵe mu msonkhano wa anthu a Chauta.
2
Mwana wam'chigololo asaloŵe mu msonkhano wa anthu a Chauta, ngakhale zidzukulu zake mpaka mbadwo wachikhumi.
3
Mwamoni kapena Mmowabu asaloŵe msonkhano wa anthu a Chauta. Ngakhale mdzukulu wao aliyense mpaka mbadwo wachikhumi, asaloledwe kuloŵa mu msonkhano wa anthu a Chauta.
4
Iwoŵa sadakupatseniko chakudya kapena madzi pa ulendo wanu uja wochoka ku Ejipito. Ndipo adalemba ntchito Balamu, mwana wa Beori, wa m'mudzi mwa Petori ku Mesopotamiya, kuti akutemberereni.
5
Koma Chauta, Mulungu wanu, sadamumvere Balamuyo. Matembererowo adaŵasandutsa madalitso pa inu, popeza kuti adakukondani inu.
6
Pa masiku onse a moyo wanu musachite kanthu kalikonse kothandiza anthu a mitundu imeneyi, kuti apeze mtendere kapena ubwino.
7
Musaŵanyoze Aedomu. Amene aja ndi abale anu. Musaŵanyoze Aejipito, popeza kuti kale mudaakhala m'dziko mwao.
8
Kuyambira pa mbadwo wachitatu mpaka muyaya, zidzukulu zao zingathe kuloŵa nao mu msonkhano wa anthu a Chauta.
9
Mukakhala m'zithando pa nthaŵi yankhondo, muzilewa zonse zimene zingathe kukulakwitsani.
10
Ngati mwamana aliyense pakati panu waipitsidwa chifukwa chakuti wadzilotera usiku, atuluke m'zithando ndipo akhale kunja kwa zithandozo.
11
Madzulo asambe ndithu, ndipo pomaloŵa dzuŵa, abwerere ku zithando.
12
Kunja kwa zithando, mukonze malo kumene mungathe kumapitako kukadzithandiza.
13
Mwa zida zanu muzitenga chokumbira, kuti muthe kukumba kadzenje komadzithandizirapo, tsono mutatha, mufotsere.
14
Zithando zanuzo zizikhala zaukhondo, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, amayenda pakati pa zithando zanu, kuti akutchinjirizeni ndi kukupambanitsani kwa adani anu. Choncho m'zithando zanu mukhale mwabwino, kuti Chauta asaone kanthu kalikonse konyansa ndi kukufulatirani.
15
Kapolo akathaŵa kwa mbuye wake, nkubwera kwa inu kuti mumsunge, musambweze kwa mbuyakeyo.
16
Angathe kukhala pakati pa inu mu mzinda wanu uliwonse umene angasankhe ndiponso kumene kungamkomere, musamvute ai.
17
Pakati pa ana a Aisraele pasakhale akazi kapena amuna okhala mahule a ku Nyumba ya Mulungu.
18
Ndalama zozipeza mwa njira yadama yotereyi, yochitika ndi mkazi kapena mwamuna, musabwere nazo ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu, kuti mukwaniritsire malonjezo anu, poti zimenezi Chauta, Mulungu wanu, amadana nazo.
19
Mukakongoza mbale wanu ndalama, kapena chakudya kapena kanthu kena kalikonse, musamulipitse chiwongoladzanja pobweza.
20
Mlendo yekha mungathe kumlipitsa chiwongoladzanja, koma osati mbale wanu. Lamulo limeneli mulimvere ndithu, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzadalitsa ntchito zanu zonse m'dziko limene mukukakhalamolo.
21
Ukachita lonjezo kwa Chauta, Mulungu wako, usazengereze kuchita chimene walonjezacho. Chauta adzakuumiriza kuti uchichite, ndipo kuzengereza nkuchimwa.
22
Koma ngati simulonjeza, apo palibe kulakwa ai.
23
Choncho muzisunga mau amene adatuluka m'kamwa mwanu, chifukwa mudalonjeza mwaufulu kwa Chauta kuti mudzachitadi zimene mudalonjeza.
24
Mukamayenda m'njira yodzera m'munda wamphesa wa mnzanu wokhala naye pafupi, mungathe kudyako mphesa zimene mungafune, koma musatengereko m'dengu pochoka.
25
Mukayenda m'njira yodzera m'munda watirigu, mungathe kudyako ngala za tirigu mobudula ndi manja, koma musadule tirigu ndi chikwakwa m'munda mwa mnzanuyo.
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34