bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 27
Deuteronomy 27
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 28 →
1
Pambuyo pake Mose, ali pamodzi ndi akuluakulu a Aisraele adauza anthu kuti, Muzimvera malamulo onse omwe ndikukupatsani leroŵa.
2
Pa tsiku limene muzaoloke mtsinje wa Yordani ndi kuloŵa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani, mudzaimiritse miyala yaitali, ndipo mudzaikulungize.
3
Mutatero, mudzalembepo mau onse a malamulo ameneŵa, mukakaloŵa m'dziko lamwanaalirenjilo, limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, adakulonjezani.
4
Mutaoloka Yordani, mudzaimiritse miyala imeneyi pa phiri la Ebala, monga momwe ndakulamulirani lero, ndipo mukaikulungize.
5
Kumeneko mukamangeko guwa la Chauta, Mulungu wanu, guwa la miyala yosasema ndi chitsulo chilichonse.
6
Guwalo likhale la miyala yosasema. Muzikapereka pamenepo nsembe zopsereza kwa Chauta, Mulungu wanu.
7
Ndipo muzikaphera ndi kudyera nsembe zachiyanjano komwekonso, ndi kumakhala okondwa pamaso pa Chauta, Mulungu wanu.
8
Pamiyalapo mudzalembepo mau onse a malamulo ameneŵa mooneka bwino.
9
Pamenepo Mose pamodzi ndi ansembe Achilevi adauza Aisraele kuti: Mverani inu Aisraele, ndipo tcherani khutu. Lero mwasanduka anthu ake a Chauta, Mulungu wanu.
10
Tsono mumvereni, ndipo musunge malamulo ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsani leroŵa.
11
Tsiku lomwelo Mose adauza Aisraele kuti,
12
Mukangooloka Yordani, mafuko amene adzaima pa phiri la Gerizimu, pamene madalitso adzatchulidwa pa Aisraele, ndi aŵa: Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini.
13
Koma mafuko ena amene adzaimirire pa phiri la Ebala, pamene matemberero adzatchulidwe pa Aisraele, ndi aŵa: Rubeni, Gadi, Asare, Zebuloni, Dani ndi Nafutali.
14
Ndipo Alevi azidzanena mau aŵa mokweza kuti,
15
“Atembereredwe aliyense wopanga fano losema kapena loumba, namalipembedza mobisa. Chauta amanyansidwa nacho chinthu chopanga mmisiricho.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
16
“Atembereredwe aliyense wosalemekeza atate ndi amai ake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
17
“Atembereredwe aliyense wosuntha malire a mnansi wake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
18
“Atembereredwe aliyense wosokeza munthu wakhungu.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
19
“Atembereredwe aliyense woweruza mopotoza milandu ya alendo, ya ana amasiye, ndi ya akazi amasiye.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
20
“Atembereredwe aliyense wogona ndi mkazi wa bambo wake, chifukwa wavula mkazi wa bambo wake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
21
“Atembereredwe aliyense wogona ndi nyama.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
22
“Atembereredwe aliyense wogona ndi mlongo wake, kapena mlongo wake wa mimba ina.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
23
“Atembereredwe aliyense wogona ndi mpongozi wake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
24
“Atembereredwe aliyense wopha mnzake mwachinsinsi.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
25
“Atembereredwe onse olandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
26
“Atembereredwe aliyense wosavomereza ndi wosatsata malamulo amene tatchulaŵa.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34