bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 28
Deuteronomy 28
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 29 →
1
Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi.
2
Mverani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalandira madalitso onse aŵa:
3
Chauta adzadalitsa mizinda yanu ndi minda yanu.
4
Chauta adzadalitsa ana anu ndi zokolola zanu, ndi ana a zoŵeta zanu, ndipo adzakupatsani ng'ombe ndi zoŵeta zina zambiri.
5
Chauta adzadalitsa mbeu zanu ndi chakudya chimene muchikonza kuchokera ku mbeuzo, kuti zichuluke.
6
Chauta adzadalitsa zochita zanu zonse.
7
Chauta adzakuthandizani kuti mugonjetse adani anu pamene akuukirani. Pokuukirani adzatulukira njira imodzi, koma pothaŵa adzathaŵira m'zikuŵa zisanu ndi ziŵiri.
8
Chauta adzadalitsa ntchito zanu, ndipo nkhokwe zanu zidzadzaza. Adzakudalitsani m'dziko limene akukupatsanilo.
9
Chauta adzakusandutsani anthu opatulikira Iye monga adalonjezera, malinga mukachita zonse zimene akukulamulani ndi kuyenda m'njira yake.
10
Tsono anthu onse a pa dziko lonse lapansi adzaona kuti Chauta, Mulungu wanu, wakusankhani inu kuti mukhale anthu akeake, ndipo azidzakuwopani.
11
Chauta adzakudalitsani pokupatsani ana ambiri, zoŵeta zambiri ndiponso zokolola zambiri. Zonsezi adzakupatsani m'dziko limene Iye adalonjeza kwa makolo anu kuti adzakupatsani.
12
Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense.
13
Mulungu wanu adzakusandutsani atsogoleri pakati pa mitundu ya anthu, osati otsata pambuyo. Mukamamvera malamulo ake amene ndikukupatsani lero ndi kuŵatsatadi mosamala, mudzakhala okwera nthaŵi zonse, osati otsika.
14
Choncho pa mau ndikukuuzani leroŵa, musapatuke kumanja kapena kumanzere, pakutsata milungu ina ndi kumaitumikira.
15
Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa:
16
Chauta adzatemberera mizinda yanu ndi minda yanu.
17
Chauta adzatemberera zokolola zanu ndiponso zokandiramo ufa wanu.
18
Chauta adzakutembererani pokupatsani ana oŵerengeka, zokolola zochepa, ndiponso ng'ombe ndi zoŵeta zina pang'ono chabe.
19
Chauta adzatemberera ntchito zanu zonse.
20
Mukamachita zoipa ndi kumkana Mulungu, Iye adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndiponso zokuvutani pa ntchito zanu zonse, mpaka mutaonongeka ndi kufa nonsenu pa kamphindi kochepa.
21
Adzakutumizirani matenda otsatanatsatana, mpaka mutatha nonse kuti psiti m'dziko limene muli kukakhalamolo.
22
Chauta adzakukanthani ndi nthenda zopatsana, zotupatupa ndi zamalungo. Adzakutumiziraninso kutentha koopsa ndi chilala ndiponso chinsikwi ndi chinoni zoononga mbeu zanu. Masoka amenewo adzakhala pa inu mpaka kukufetsani.
23
Mvula sidzakugwerani ndipo nthaka yanu idzauma kuti gwa ngati chitsulo.
24
M'malo mwa mvula, Chauta adzakugwetserani fumbi ndi mchenga, mpaka mutaonongeka nonse.
25
Chauta adzalola kuti adani anu akugonjetseni. Pokalimbana nawo mudzadzera njira imodzi, koma poŵathaŵa mudzapanga zikuŵa zisanu ndi ziŵiri. Ndipo mafumu onse a pa dziko lapansi adzaopsedwa poona zokuchitikiranizo.
26
Mutafa, mbalame pamodzi ndi nyama zakuthengo zidzadya mitembo yanu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzazipirikitse.
27
Chauta adzakulangani ndi zithupsa zonga za ku Ejipito zija. Mudzakhala ndi zilonda, mphere, ndi kunyerenyesa, zonsezo zosamva mankhwala. Thupi lanu lidzakhala la mphere zokhazokha, ndipo muzidzangokandakanda, koma osachira.
28
Chauta adzakuchititsani misala, ndipo adzakusandutsani akhungu ndi osokonezeka.
29
Ngakhale dzuŵa lili nye, muzidzachita kufufuza njira ngati anthu akhungu. Kalikonse kamene mudzachite simudzalemera nako. Kaŵirikaŵiri azidzakupsinjani ndi kumakuberani, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzakuthandizeni.
30
Mudzafunsira mbeta mtsikana, koma ndi wina amene adzakwatirane naye. Kumanga nyumba mudzamanga ndithu, koma simudzagonamo. Munda wamphesa mudzabzala, koma mphesa zake simudzadyako.
31
Ng'ombe zanu azidzakupherani mukupenya, koma nyama yake simudzadyako. Abulu anu azikaŵalanda mwamphamvu ndi kupita nawo kwina, inu mukupenya, ndipo sadzakubwezerani. Nkhosa zanu adzazipereka kwa adani anu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzakuthandizeni.
32
Ana anu aamuna ndi aakazi adzatengedwa ukapolo ndi alendo, inu mukupenya. Tsiku ndi tsiku maso anu adzakhala ali psuu kuyang'anira ngati ana anuwo abwere, koma simudzaphulapo kanthu.
33
Mtundu wachilendo udzakulandani zakumunda zanu zonse zimene mudathyoka nazo msana polima, ndipo mudzapsinjidwa ndi kuzunzika mosalekeza.
34
Zimene mudzaziwona ndi maso zidzakupengetsani.
35
Chauta adzabweretsa zilonda zoŵaŵa ndi zosachizika pa maondo ndi pamisongolo panu, ndipo anamkalimbwi azidzakutulukani thupi lonse, kuyambira kuphazi mpaka kumutu.
36
Chauta adzaipirikitsira ku dziko lachilendo mfumu yanu, pamodzi ndi inu nomwe, kumene inuyo ndi makolo anu simudakhaleko nkale lonse. Kumeneko muzikatumikira milungu ina yopanga ndi mitengo ndi miyala.
37
Ku mitundu yonse kumene Chauta adzakumwazireniko, anthu adzadabwa nanu, adzakusekani, adzakupekani nthano yokunyodolani.
38
Mudzabzala zambiri, koma mudzakolola pang'ono chabe, chifukwa dzombe lidzadya zolima zanuzo.
39
Minda yamphesa mudzalimadi, mpaka kuisamala bwino, koma mphesa zake simudzathyola kapena kumwako vinyo wake, chifukwa tizilombo ndito tidzadye mphesazo.
40
Mitengo ya olivi izidzamera paliponse m'dziko mwanumo, koma mafuta a olivi simudzakhala nawo, chifukwa zipatso za olivizo zidzayoyoka.
41
Mudzabereka ana aamuna ndi aakazi ndithu, koma sadzakhala anu, chifukwa adzatengedwa ukapolo.
42
Mitengo yanu yonse ndi dzinthu dzanu dzam'munda zidzatha ndi tizilombo.
43
Alendo okhala m'dziko mwanu ndiwo amene azidzakwererakwerera, koma inu muzidzatsikiratsikira.
44
Iwowo azidzakukongozani ndalama, koma inu simudzakhala nazo ndi pang'ono pomwe zoŵakongoza, ndipo potsiriza adzakulamulirani.
45
Masoka onseŵa adzakugwerani. Adzakhala pa inu mpaka mutaonongeka, chifukwa choti simudamvere Chauta, Mulungu wanu, ndipo simudatsate malamulo ndi malangizo onse amene Iye adakupatsani.
46
Masoka onseŵa adzakhala mboni yapadera ya chilango cha Mulungu pa inu ndi pa zidzukulu zanu mpaka muyaya.
47
Paja Chauta adakudalitsani pa zonse, komabe inu simudamtumikire mokondwa ndi mitima yachimwemwe.
48
Motero mudzatumikira adani odzalimbana nanu amene Chauta adzakutumizireni. Mudzamva njala ndi ludzu. Zinthu zonse zidzakusoŵani pamodzi ndi zovala zomwe. Chauta adzakuzunzani mwankhanza, mpaka mutaonongeka.
49
Chauta adzaitanitsa mtundu wa anthu ochokera ku malekezero a dziko lapansi, kuti adzamenyane nanu. Anthu a mtundu umenewo amene inu simudziŵa chilankhulo chao, adzakuterani ngati mphungu.
50
Anthuwo adzakhala aukali, ndipo sadzachita chifundo ndi aliyense, ngakhale akhale mwana kapena nkhalamba.
51
Adzakudyerani ng'ombe zanu pamodzi ndi zakumunda zanu zomwe, mpaka mudzafa ndi njala. Sadzakusiyiraniko mpang'ono pomwe tirigu, vinyo, mafuta aolivi, ng'ombe kapena nkhosa, ndipo mudzafadi.
52
Adzathira nkhondo mzinda uliwonse, m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo. Ndipo malinga ataliatali amene mukuŵakhulupirirawo adzagwa ponseponse. Adzakuzingani m'mizinda yonse ya m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsanilo.
53
Nthaŵi imene adani anu adzazinga mizinda yanu ndi kukusautsani koopsa, mudzasoŵa chakudya kotheratu, kotero kuti muzidzadya ana anu omwe aamuna ndi aakazi, amene Chauta adakupatsani.
54
Ngakhale munthu amene ali woleredwa bwino ndi wofatsa mtima kwambiri mwa inu, adzamana chakudya mbale wake, mkazi wake wapamtima ndi ana ake omutsalira,
55
mwakuti sadzapatsako ndi mmodzi yemwe nyama ya ana ake amene akuŵadya, chifukwa adzakhala alibiretu chakudya pa nthaŵi imene adani anu azidzakuzingani ndi kukusautsani koopsa.
56
Ngakhale mkazi woleredwa bwino ndi wolobodoka kotero kuti sangayese nkomwe kupondetsa pansi phazi lake, adzamana mwamuna wake wapamtima ndi ana ake onse
57
nyama ya ana ake ongobadwa kumene, pamodzi ndi za matenda ake zomwe zochokera m'mimba mwake, popeza kuti azidzadya zimenezi yekha mobisa, chifukwa cha kusoŵeratu chakudya, nthaŵi imene adani anu adzazinga mizinda yanu ndi kukusautsani kwambiri.
58
Muzimvera mau onse a malamulo aŵa a m'buku muno, ndipo dzina ili lodabwitsa ndi lochititsa mantha la Chauta, Mulungu wanu, muzilitamanda.
59
Mukapanda kutero, inuyo ndi zidzukulu zanu, Chauta adzakugwetserani masautso apadera, mavuto aakulu okhalitsa ndiponso nthenda zoopsa zosamva mankhwala.
60
Nthenda zonse zoopsa zimene mudaopsedwa nazo muli ku Ejipito kuja, Chauta adzakugwetserani zimenezo, ndipo simudzachira.
61
Adzakugwetseraninso nthenda zonse zamitundumitundu pamodzi ndi miliri yomwe, zimene sizidatchulidwepo m'buku la malamulo a Mulungu, ndipo mudzaonongeka.
62
Ngakhale mudaachuluka ngati nyenyezi zakuthambo, koma amoyo mudzakhala ochepa, chifukwa choti simudamvere Chauta, Mulungu wanu.
63
Monga momwe kudakomera Chauta kukudalitsani ndi kukuchulukitsani kuti mukhale ambiri, momwemo kudzamkomeranso kuti akuwonongeni kotheratu. Adzakuchotsani m'dziko limene mukuliloŵa kukakhalamolo.
64
Ndipo Chauta adzakumwazani pakati pa mitundu yonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko mpaka ku malekezero ake enanso. Kumeneko muzidzapembedza milungu yamitengo ndi yamiyala, imene inu ndi makolo anu simudaidziŵe nkale lonse.
65
Simudzapeza mtendere kwina kulikonse ndipo malo anuanu simudzaŵapeza. Mudzakhala ankhaŵa, osoŵa thandizo ndi otaya mtima, ndipo Chauta ndiye adzagwetse zimenezi pa inu.
66
Nthaŵi zonse, moyo wanu udzakhala wopenekapeneka. Muzidzakhala amantha, usiku ndi masana womwe, ndipo muzidzangokhalira kuwopa imfa.
67
Mitima yanu idzakhala yamantha poona kalikonse. M'maŵa mulimonse muzidzangofuna kuti kude. Madzulo aliwonse muzidzafuna kuti kuche.
68
Ndipo Chauta adzakutumizaninso ku Ejipito m'zombo zapanyanja, ngakhale kuti ndidaalonjeza kuti simudzapitakonso. Kumeneko mudzayesayesa kudzigulitsa ngati akapolo kwa adani anu, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene adzafune kukugulani.
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 29 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34