bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 4
Deuteronomy 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 5 →
1
Tsopano inu Aisraele, muzimvera malamulo ndi malangizo onse amene ndikukuphunzitsani, kuti mukhale ndi moyo. Ndipo mudzaloŵa ndi kukhazikika m'dziko limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, akukupatsani.
2
Musaonjezerepo kanthu kena pa zimene ndakulamulani, ndipo musachotsepo kanthu. Muzimvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndakupatsani.
3
Inu mudaona zimene Chauta adachita ku Baala-Peori. Kumeneko Chauta, Mulungu wanu, adaonongeratu onse amene ankapembedza Baala wa ku Peori,
4
koma nonsenu amene mudakangamira Chauta, Mulungu wanu, muli ndi moyo lero lino.
5
Ndakuphunzitsani malamulo ndi malangizo onse, monga momwe Chauta, Mulungu wanga, adandilamulira. M'dziko limene mudzaloŵa ndi kukhalamolo, muzikamvera malamulo ameneŵa.
6
Mukaŵasunge ndi kuŵatsata, ndipo chimenechi chidzaonetsa anthu a mitundu ina kuti ndinu anthu anzeru ndi omvetsa zinthu bwino. Akadzamva malamulo onseŵa, iwowo adzati, “Mtundu umenewu ndi waukulu, wanzeru ndi womvetsa zinthu bwino.”
7
Palibe mtundu wina uliwonse, kaya ndi waukulu chotani, umene uli ndi Mulungu wokhala pafupi nawo, monga m'mene Mulungu wathu amakhalira ndi ife. Nthaŵi zonse tikamuitana, amatiyankha.
8
Palibe mtundu wina uliwonse kaya ndi waukulu chotani, umene uli ndi malamulo ndi malangizo achilungamo onga aŵa amene ndakupatsani leroŵa.
9
Mukhale tcheru, ndipo musadzaiŵale zonse zimene mudaziwona. Zimenezo zisachoke m'mitima mwanu pa moyo wanu wonse. Muzizifotokoza kwa ana anu ndi kwa zidzukulu zanu zomwe.
10
Muziŵauza za tsiku lija pamene mudaima pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, ku phiri la Horebu kuja. Kumeneko Chauta adandiwuza kuti, “Asonkhanitseni anthu. Ndifuna kuti iwo amve zimene ndilankhule, kuti aphunzire kundiwopa nthaŵi zonse adzakhale ndi moyo pa dziko lapansi, kenaka azidzaphunzitsanso ana ao kundimvera.”
11
Inu mudadza, mudaima patsinde pa phiri. Phirilo linkayaka moto mokwera mpaka ku thambo, ndipo linali lophimbidwa ndi chiwutsi chabii ndi chimdima.
12
Chauta adalankhula nanu ali m'motomo, ndipo munkamumva akulankhula, koma osamuwona.
13
Chauta adakuuzani zimene muyenera kuchita, kuti musunge chipangano chimene adapangana ndi inu, ndicho malamulo khumi amene adaŵalemba pa miyala iŵiri.
14
Chauta adandilamula nthaŵi imeneyo kuti ndikuphunzitseni malamulo amene muyenera kumaŵasunga m'dziko limene mukaloŵe ndi kukakhalamolo.
15
Pamene Chauta adalankhula nanu ali m'moto pa phiri la Horebu lija, inu simudaone kanthu kalikonse. Nchifukwa chake muchenjere.
16
Samalani kuti musachimwe pakudzipangira fano la mtundu uliwonse, kaya fanolo likhale longa mwamuna kaya mkazi,
17
fano la nyama iliyonse ya pa dziko lapansi, fano la mbalame iliyonse yamumlengalenga,
18
fano la chilichonse chokwaŵa pa nthaka, ndi fano la nsomba iliyonse yam'madzi pansi pa dziko.
19
Musamale kuti mukapenya ku thambo nkuwona dzuŵa, mwezi, nyenyezi ndi zonse zakuthamboko, mtima wanu usakopeke nkuyamba kupembedza ndi kutumikira zinthu zimene Mulungu wanu wapatsa anthu ena onse a pa dziko lapansi.
20
Koma inu ndinu anthu amene Mulungu adakutulutsani ku dziko la Ejipito, ng'anjo yotentha ija. Adakutulutsanimo kuti mukhale anthu akeake monga m'mene muliri leromu.
21
Chauta, Mulungu wathu, adandikwiyira ine chifukwa cha inu. Ndipo adalumbira kuti ine sindiwoloka mtsinje wa Yordani kukaloŵa m'dziko lokoma limene akukupatsanilo ngati choloŵa chanu.
22
Ndidzafera m'dziko lomwe lino osaoloka mtsinjewo. Koma inu, muli pafupifupi kuwoloka ndi kukhala m'dziko lokomalo.
23
Samalani bwino, musaiŵale chipangano chimene Chauta, Mulungu wanu, adachita nanu, ndipo musapange fano lofanizira chinthu chilichonse chimene Chauta, Mulungu wanu, adakuletsani.
24
Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wansanje, salola kuti wina apikisane naye. Ali ngati moto waukali.
25
Ngakhale mutakhala m'dzikomo nthaŵi yaitali, ndi kubereka ana ndi zidzukulu, musadzachimwe pakudzipangira fano la maonekedwe ena aliwonse. Pamaso pa Chauta ndi zoipa zimenezi, ndipo adzapsa nazo mtima.
26
Mukachita zimenezi, ndikukuuzani lero, kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni, kuti simudzakhalitsa pa dziko. Mudzaonongeka m'dziko ili la patsidya pa Yordani, limene mukukakhalamolo. Mudzaonongeka nonsenu.
27
Chauta adzakumwazani pakati pa mitundu ina, ndipo oŵerengeka okha mwa inu ndiwo adzatsala pakati pa mitundu ina kumene Chauta adzakupirikitsirani.
28
Kumeneko muzidzatumikira milungu yopanga ndi manja, monga yamtengo ndi yamwala, milungu imene singathe kupenya kapena kumva, kudya kapenanso kununkhiza.
29
Kumeneko inu mudzafunafuna Chauta, Mulungu wathu, ndipo ngati mudzamfunafuna ndi mtima wonse ndi moyo wanu wonse, mudzampeza.
30
Mukadzakhala pa mavuto, ndipo zinthu zonsezi nkukuchitikirani, pamenepo mudzabwerera kwa Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzamvera mau ake.
31
Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wachifundo. Sadzakulekererani kapena kukuwonongani. Chipangano chimene Iye adachita molumbira ndi makolo anu, sadzachiiŵala.
32
Tafufuzani zakale, inu musanabadwe, kuyambira pa tsiku lija limene Mulungu adalenga munthu pa dziko lapansi. Tafufuzani pa dziko lonse lapansi. Kodi chachikulu chonga chimenechi chidachitikapo ndi kale lonse? Kodi alipo wina amene adamvapo zotere?
33
Kodi alipo anthu ena amene adakhalabe ndi moyo, atamva mau a Mulungu ali m'moto, monga m'mene mudamvera inu?
34
Kodi alipo mulungu wina aliyense amene adaapita kukadzitengera anthu kuŵachotsa pakati pa fuko lina, naŵasandutsa anthu akeake, monga muja Chauta, Mulungu wanu, adakuchitirani inu ku Ejipito kuja? Iye adachita zimenezo ndi mphamvu zake zazikulu, inu mukupenya. Adadzetsa miliri pamodzi ndi nkhondo, adachita zozizwitsa ndi zodabwitsa.
35
Chauta adakuwonetsani zimenezi, kuti inu mudziŵe kuti Chauta yekha ndiye Mulungu, ndipo kuti palibenso wina.
36
Chauta adalola kuti mumve mau ake kuchokera kumwamba, kuti pakutero akuphunzitseni. Pa dziko lapansi pano Chauta adakuwonetsani moto waukulu, ndipo mudamva akulankhula nanu kuchokera m'motomo.
37
Popeza kuti Chauta adakonda makolo anu, adasankha inu zidzukulu zao nakutulutsani ku Ejipito pakuwonetsa ulemu ndi mphamvu zake zazikulu.
38
Pamene munkayenda, Iye adapirikitsira kutali mitundu ikuluikulu kupambana inu, kuti akuloŵetseni ndi kukupatsani dziko laolo, kumene muli lero lino.
39
Choncho dziŵani ndipo musamaiŵala kuti Chauta ndiye Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, palibe wina ai.
40
Muzimvera malangizo ndi malamulo ake onse amene ndakupatsani leroŵa. Mukatero, zinthu zidzakuyenderani bwino inuyo ndi zidzukulu zanu, ndipo mudzakhalitsa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani kuti likhale lanu mpaka muyaya.
41
Pamenepo Mose adapatula mizinda itatu kuvuma kwa Yordani
42
kumene munthu wopha mnzake mwangozi, osati mwachidani, ankatha kuthaŵirako ndi kupulumutsa moyo wake.
43
A fuko la Rubeni, mzinda wao unali Bezeri umene unali m'chipululu, m'dziko lamapiri. A fuko la Gadi, mzinda wao unali Ramoti umene unali m'dziko la Giliyadi. Ndipo a fuko la Manase mzinda wao unali Golani umene unali m'dziko la Basani.
44
Aŵa ndi malamulo amene Mose adapatsa Aisraele.
45
Ameneŵa ndi malamulo ndi mau ndiponso malangizo amene Mose adauza Aisraele, atatuluka ku Ejipito.
46
Aisraelewo anali m'chigwa kuvuma kwa mtsinje wa Yordani, kuyang'anana ndi mudzi wa Betepeori. Kumeneko ndi dziko la Sihoni, mfumu ya Aamori, amene ankalamula mzinda wa Hesiboni, ndipo Mose ndi Aisraelewo atatuluka m'dziko la Ejipito, adamgonjetsa Sihoniyo.
47
Aisraele aja adakakhala m'dziko lake ndi m'dziko la mfumu Ogi wa ku Basani. Ameneŵa anali mafumu aŵiri a Aamori amene ankakhala kuvuma kwa Yordani.
48
Dziko limene adalandalo lidayambira ku mudzi wa Aroere pamphepete pa mtsinje wa Arinoni, mpaka kukafika ku phiri la Sirioni (ndiye kuti phiri la Heremoni),
49
ndi dziko lonse la Araba la kuvuma kwa mtsinje wa Yordani, mpaka kukafika ku Nyanja ya Araba, patsinde pa phiri la Pisiga.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34