bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 30
Deuteronomy 30
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 31 →
1
Pamene adzakufikirani madalitso ndi matemberero amene ndatchula aja, mudzaŵakumbukira muli pakati pa mitundu ina kumaiko kumene Chauta, Mulungu wanu, adakumwazirani.
2
Tsono inuyo ndi zidzukulu zanu mudzabwerera kwa Chauta, ndipo mau ake amene ndikukupatsani leroŵa mudzaŵamvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
3
Pamenepo Chauta, Mulungu wanu, adzakukhazikaninso pabwino ndi kukuchitirani chifundo. Adzakusokolotsani kukuchotsani ku mitundu ina ya anthu, kumene adakumwaziraniko, ndipo adzakusandutsaninso olemera.
4
Ngakhale mutamwazikira ku malekezero a dziko lapansi, Chauta, Mulungu wanu, adzakusonkhanitsani komweko nadzakutengani kuchokera kumeneko.
5
Adzakuperekezani ku dziko limene makolo anu anali nalo kale, kuti mukakhazikikeko ndinu. Ndipo adzakupezetsani bwino ndi kukuchulukitsani kopambana m'mene adaaliri makolo anu.
6
Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani inu ndi zidzukulu zanu mtima womvera, kotero kuti muzidzamkonda ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse. Motero mudzakhalabe ndi moyo m'dziko limenelo.
7
Koma Chauta, Mulungu wanu, adzagwetsa matemberero onse aja pa adani anu amene adakuzunzani.
8
Inuyo mudzamveranso ndi kumatsata malamulo amene ndikukupatsani leroŵa.
9
Chauta adzakupezetsani bwino pa zochita zanu zonse. Mudzakhala ndi ana ambiri, zoŵeta zambiri, ndipo minda yanu idzakubalirani zokolola zambiri. Adzakondwera nanu kuti mwakhoza chotere, monga momwe adakondwera ndi makolo anu pamene anali okhoza.
10
Komatu muzidzamvera Chauta, Mulungu wanu, ndi kusunga malamulo ndi malangizo ake onse amene ali m'buku lino la malamulo ake. Mutembenukire kwa Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
11
Lamulo ndikukupatsani leroli si lovuta kulimvetsa ndipo si lapatali.
12
Silili kumwamba, kuti muzichita kudzifunsa kuti, “Kodi amene akwere kumwamba kukatitsitsira lamulo kuti tilimve, ndani?”
13
Komanso silili pa tsidya la nyanja, kuti muthe kufunsa kuti, “Kodi amene aoloke nyanja kukatitengera lamulo kuti tilimve, ndani?”
14
Muli nalo pompano. Mukulidziŵa, mumalitchula ndipo mungathe kulitsata.
15
Ndikukupatsani mpata lero woti musankhe, kapena moyo ndi zabwino, kapena imfa ndi zoipa.
16
Mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, mukamamkonda Chauta, Mulungu wanu ndi kutsata mau ake onse, pamenepo mudzakhala pabwino ndipo mudzakhala mtundu wa anthu ochuluka. Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani m'dziko mukukakhalamolo.
17
Koma mukapanda kumvera, mukamakana kumva, m'malo mwake nkumatengeka kuti mupembedze milungu ina,
18
ndikuchenjezeranitu tsopano kuti mudzaonongeka. Dziko ili la patsidya pa Yordani limene mukupita kukakhalamolo, simudzakhalitsamo.
19
Tsopano ndikukupatsani mpata woti musankhe, kapena moyo kapena imfa, madalitso a Mulungu kapena matemberero ake. Zonse zakumwamba ndi zapansi zikhale mboni za zimene ndakuuzani lerozi. Tsono sankhani moyo,
20
mukonde Chauta, Mulungu wanu, muzimvera mau ake ndi kukhala okhulupirika kwa Iye, kuti inu ndi zidzukulu zanu mudzakhalitsemo m'dziko limene adalonjeza kuti adzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
← Chapter 29
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 31 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34