bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 22
Deuteronomy 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 23 →
1
Mukaona ng'ombe kapena nkhosa ya Mwisraele mnzanu ikusokera, musailekerere. Itengeni, mukampatse mwiniwake.
2
Koma ngati mwiniwake kwao nkutali, kapena simumdziŵa, itengeni mupite nayo kwanu, muisunge komweko. Koma mwiniwake akabwera kudzaifunafuna, mumpatse.
3
Mukapeza bulu, chovala kapena kanthu kena kalikonse kamene Mwisraele mnzanu wataya, chitani chimodzimodzi, musakalekerere ai.
4
Bulu wa Mwisraele mnzanu akagona mu mseu, muutseni. Muchitenso chimodzimodzi ndi ng'ombe yake, musailekerere. Mthandizeni mnzanu kuti adzutse choŵetacho.
5
Akazi asamavale zovala za amuna, chimodzimodzi amuna asamavale zovala za akazi. Chauta, Mulungu wanu, amanyansidwa nawo anthu ochita zotere.
6
Ngati mupeza chisa cha mbalame mu mtengo kapena pansi, make ali pa mazira, kapena ali ndi tiana take, musaitenge mbalameyo pamodzi ndi tiana take.
7
Tianato mungathe kutenga, koma makeyo mloleni apite, kuti mukakhale ndi moyo wabwino ndi wautali.
8
Pamene mukumanga nyumba, muwonedi kuti mwamanga kampanda pamwamba kuzungulira mbali zonse zadenga. Apo inuyo simudzazengedwa mlandu wa kukhetsa magazi ngati wina agwa kuchokera pa denga, naphedwa.
9
M'munda wamphesa musabzalemo mbeu ina iliyonse. Ngati mutero, zonse zidzakhala zoletsedwa, mphesazo ndi mbeu zina zomwe.
10
Musamange ng'ombe ndi bulu kuti zilimire pamodzi.
11
Musamavale nsalu yoombedwa ndi ubweya pamodzi ndi thonje.
12
Sokani mphonje pa ngodya zinai za miinjiro yanu imene mumavala.
13
Mwina munthu angathe kukwatira mtsikana, namakhala naye ndithu, pambuyo pake nkunena kuti mkaziyo sakumfuna.
14
Tsono ayamba kumnenera zabodza zochititsa manyazi ndi kuipitsa mbiri yake ponena kuti, “Mkazi ameneyu sadaoneke ngati namwali wosadziŵa mwamuna pa nthaŵi yomukwatira.”
15
Zitatero, makolo a mkaziyo atenge zizindikiro zotsimikizira akuluakulu abwalo am'mudzimo kuti mwana waoyo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ndithu.
16
Pamenepo bambo wake wa mtsikanayo aŵauze abwalowo kuti, “Ndidalola mwana wanga wamkazi kuti akwatiwe ndi munthu uyu, koma tsopano akuti sakumufuna.
17
Wamnamizira momchititsa manyazi kuti ati sadali namwali wosadziŵa mwamuna pomkwatira. Koma pano tili ndi umboni wotsimikizira kuti mwana wangayu adaali namwali wangwiro ndithu. Onani, zizindikiro zake ndi izi.” Apo adzaonetse chovala cha mkaziyo kwa akuluakuluwo.
18
Tsono akuluakulu am'mudzimo amtenge mwamunayo ndi kumkwapula.
19
Pambuyo pake amlipitsenso masekeli asiliva makumi khumi, ndipo azipereke kwa bambo wa mtsikanayo. Alipe ndithu chifukwa choti adanyozetsa mnamwali Wachiisraele amene sadamdziŵeko mwamuna. Komanso adzakhalabe mkazi wake ndithu, ndipo pa moyo wake wonse sadzathanso kumsudzula.
20
Koma ngati zomunenerazo ndi zoona, ndipo umboni wakuti mtsikanayo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ukusoŵa,
21
pamenepo apite naye pakhomo pa bambo wake. Pomwepo amuna amumzindamo amuphe pakumponya miyala. Mtsikanayo wachita chinthu chochititsa manyazi pakati pa mtundu wathu wa Israele pochita zadama m'nyumba ya bambo wake. Motero mudzachotsa choipa pakati pa inu.
22
Munthu akagwidwa akuchita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, aphedwe onsewo, mwamuna ndi mkazi yemwe. Choncho mudzachotsa choipa pakati pa inu.
23
Tiyese kuti mwagwira munthu mumzinda momwemo akuchita chigololo ndi mnamwali wofunsidwa mbeta, amene sadamdziŵeko mwamuna.
24
Muŵatenge onsewo, mupite nawo kunja kwa mzinda, ndipo muŵaphe poŵaponya miyala. Mtsikanayo aphedwe chifukwa ngakhale anali m'mudzi, sadakuwe kuti anthu adzamthandize. Mwamunayo aphedwe chifukwa wachimwa ndi mtsikana wofunsidwa mbeta ndi mnzake. Motero mudzachotsa choipa pakati panu.
25
Mwina munthu, kuthengo koteroko, achita kugwirira mtsikana wofunsidwa mbeta nachita naye chigololo momkakamiza. Zikatero, munthu wamwamuna yekhayo ndiye aphedwe.
26
Mtsikanayo musamchite kanthu chifukwa choti sadachite tchimo loyenera kufa nalo. Mlandu umenewu ukufanafana ndi wakuti munthu aputa mnzake, namupha.
27
Munthuyo wachita kumgwira mtsikanayo nkuchita naye chigololo kuthengo. Ndipo ngakhale adaakuwa, panalibe amene akadampulumutsa.
28
Mwina munthu agwidwa akugwirira mnamwali wosafunsidwa mbeta, amene sadamdziweko mwamuna, nachita naye chigololo momkakamiza.
29
Munthuyo alipe bambo wake wa mtsikanayo mtengo wofunsira mbeta, ndiye kuti masekeli asiliva makumi asanu, ndipo amtenge kuti akhale mkazi wake chifukwa choti adamkakamiza kuchita naye chigololo. Tsono pa moyo wake wonse sangathenso kumsudzula.
30
Munthu asakwatire mkazi wa bambo wake, kapena kuchita chipongwe chomuvula.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34