bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Deuteronomy 31
Deuteronomy 31
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 32 →
1
Mose adapitirira kulankhula ndi Aisraele aja kuti:
2
Tsopano ndili ndi zaka 120, ndipo sindingathenso kukhala mtsogoleri wanu. China nchakuti Chauta adandiwuza kuti Yordaniyu sindimuwoloka.
3
Mwini wake Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzakuperekezeni ndi kuwononga mitundu ina yonseyi, kuti inu mukhale m'dziko mwao. Yoswa adzakhala mtsogoleri wanu, monga momwe Chauta wanenera.
4
Chauta adzaŵaononga anthu ameneŵa monga momwe adaonongera Sihoni ndi Ogi, mafumu a Aamori, pamodzi ndi dziko lao.
5
Chauta adzakupambanitsani, ndipo adaniwo muzikaŵachita zomwe ndakulamulanizi.
6
Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.
7
Pomwepo Mose adaitana Yoswa pamaso pa Aisraele onse ndipo adamuuza kuti, “Khala wamphamvu ndipo ulimbe mtima. Ndi iweyo amene udzatsogolere anthu aŵa ku dziko limene Chauta adalonjeza makolo ao. Ndiwe amene udzakhazikitsa anthu m'dzikomo.
8
Chauta mwini wake adzakutsogolera, ndipo adzakhala nawe. Sadzalola kuti ulephere, ndipo sadzakusiya. Motero usachite mantha kapena kutaya mtima.”
9
Pamenepo Mose adalemba malamulo a Mulungu ndi kuŵapatsa ansembe, ana a Levi, amene ankanyamula Bokosi lachipangano la Chauta. Adaŵapatsanso atsogoleri a Aisraele.
10
Adaŵalamula onsewo kuti, “Kamodzi pa zaka zisanu ndi ziŵiri zilizonse, pamene chaka cha kumasulidwa chafika, muŵerenge malamuloŵa pa chikondwerero cha misasa.
11
Muŵaŵerenge kwa Aisraele onse, pamene adzabwere kudzapembedza Chauta pa malo oŵasankha Iyeyo.
12
Mudzaitane amuna onse, akazi, ana ndi alendo amene ali m'mizinda mwanu, kuti aliyense adzimvere yekha, ndipo aphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wanu, ndi kumamvera mau ake mosamala.
13
Mwa njira imeneyi zidzukulu zanu zimene sizidamve malamulo a Chauta nkale lomwe, zidzamva, ndipo zidzaphunzira kuwopa Chauta nthaŵi yonse imene zidzakhale m'dziko limene mukukakhalamolo patsidya pa Yordani.”
14
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Nthaŵi ya moyo wako yatsala yochepa. Itana Yoswa, ubwere naye ku chihema chamsonkhano kuti ndimulangize.” Mose pamodzi ndi Yoswa adapita ku chihema chamsonkhano,
15
ndipo Chauta adaŵaonekera iwowo mu mtambo wonga chipilala umene udaaima pakhomo pa chihemacho.
16
Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Patsala pang'ono kuti iwe umwalire. Ndiye iwe ukapita, anthuŵa adzaphwanya chipangano chomwe ndidachita nawo. Adzandisiya Ine, nkumapembedza milungu ya dziko limene akukakhalamolo.
17
Zikadzangotero, ndidzaŵakwiyira ndi kuŵasiya, ndipo adzatheratu. Masoka ndi zoipa zina zambiri zidzaŵagwera. Tsono masiku amenewo azidzanena kuti, ‘Kodi zoipazi sizikutigwera chifukwa chakuti Chauta, Mulungu wathu, sali nafenso?’
18
Ndithudi pa nthaŵi imeneyo ndidzaŵafulatira chifukwa cha machimo onse amene iwo adachita popembedza milungu ina.
19
“Tsopano talemba nyimbo iyi. Uŵaphunzitse ndi kuŵalimbitsa Aisraele kuti idzakhale mboni yanga yoŵatsutsa.
20
Ndidzaŵaloŵetsa m'dziko lamwanaalirenji, monga momwe ndidalonjezera makolo ao. Kumeneko adzapeza chakudya chonse chomwe angachifune, ndipo adzakhala mosangalala. Komabe adzatembenukira ku milungu ina ndi kumaipembedza. Adzandikana Ine, ndipo adzaphwanya chipangano changa.
21
Choncho masoka oopsa adzaŵagwera. Nyimbo imeneyi idzakhala mboni yanga yoŵatsutsa, chifukwa zidzukulu zao zizidzaiimba. Ngakhale tsopano lino ndisanaŵaloŵetse m'dziko limene ndidalumbira kuti ndidzaŵapatsa, ndikudziŵa zimene iwo akulingalira.”
22
Tsiku lomwelo Mose adalemba nyimbo naphunzitsa Aisraele.
23
Tsono Chauta adauza Yoswa, mwana wa Nuni, kuti, “Khala wamphamvu ndipo ulimbe mtima. Udzaŵatsogolera Aisraele kukaloŵa m'dziko lomwe ndidaŵalonjeza. Ndipo ndidzakhala nawe.”
24
Tsono Mose adalemba malamulo a Mulungu m'buku, osasiya kanthu.
25
Atamaliza, adauza Alevi amene ankanyamula Bokosi lachipangano kuti,
26
“Tengani buku ili la malamulo a Mulungu, ndipo muliike pambali pa Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wanu, kuti likhale kumeneko ngati mboni yokutsutsani.
27
Ndikudziŵa kukanika kwanu ndiponso uchigaŵenga wanu. Ngati mugalukira Chauta, ndikadali moyo, nanji ndikadzafa, ndiye mudzaposa kugaluka kwake.
28
Mundisonkhanitsire atsogoleri onse a mafuko pamodzi ndi akuluakulu omwe, kuti ndiŵauze zimenezi. Kumwamba ndi dziko lapansi ndizo zidzakhale mboni zoŵatsutsa.
29
Ndikudziŵa kuti ine ndikadzafa, nonse mudzaipa ndipo mudzakana zimene ndakuuzanizi. Koma pambuyo pake kutsogoloko, mudzakomana ndi masoka, chifukwa chochita zoipa pamaso pa Chauta ndi kuputa mkwiyo wake pakuchulukitsa machimo anu. Mwakwiyitsa Chauta pochita zimene Iyeyo amakana.”
30
Tsono Mose adanena mau a nyimbo yonseyi, kuyambira poyamba mpaka potsiriza, Aisraele onse alikumva:
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 32 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34