bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 1
2 Chronicles 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 2 →
1
Solomoni mwana wa Davide adakhazikika molimbika mu ufumu wake, ndipo Chauta, Mulungu wake, anali naye, namkweza kwambiri.
2
Solomoni adalankhula ndi Aisraele onse, atsogoleri a anthu zikwi ndiponso atsogoleri a anthu mazana, aweruzi, atsogoleri a Aisraele onse, ndiponso akulu a mabanja.
3
Solomoni pamodzi ndi anthu onse amene adasonkhana nawo, adapita ku kachisi wa ku Gibiyoni. Paja chihema chamsonkhano cha Mulungu chimene Mose, mtumiki wa Chauta, adaamanga ku chipululu chinali kumeneko.
4
(Davide anali atabwera nalo bokosi lachipangano la Chauta kuchokera ku Kiriyati-Yearimu, ndi kulikhazika ku malo amene iye adaakonza, poti adaalimangira hema ku Yerusalemu.)
5
Kuwonjezera pamenepo, guwa lamkuŵa limene adaapanga Bazalele mwana wa Uri, mwana wa Huri, linali komweko kumaso kwa chihema cha Chauta. Ndipo Solomoni adakapembedza kumeneko pamodzi ndi msonkhano wonse.
6
Solomoni adakwera komweko ku guwa lamkuŵa lopembedzerapo Chauta, limene linali ku chihema chamsonkhano, naperekapo nsembe zopsereza zokwanira 1,000.
7
Usiku umenewo Mulungu adamuwonekera Solomoni namuuza kuti, “Upemphe chilichonse chimene ufuna kuti ndikupatse.”
8
Solomoni adati, “Inu Mulungu, mudaonetsa chikondi chanu chachikulu ndi chosasinthika kwa bambo wanga Davide, ndipo tsono mwandiika ine kuti ndikhale mfumu m'malo mwake.
9
Inu Chauta, zimene mudalonjeza kwa bambo wanga Davide zichitikedi, pakuti mwandiika kuti ndikhale mfumu yolamulira anthu ochuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi.
10
Tsono mundipatse nzeru ndi luntha, kuti ndiŵatsogolere bwino anthu anuŵa. Nanga popanda nzeruzo ndani angathe kulamulira mtundu waukulu wa anthu anu?”
11
Mulungu adamuyankha kuti, “Chifukwa chakuti waganiza zimenezi mumtima mwako, ndipo sudapemphe katundu, chuma, ulemu, kapena imfa ya adani ako, sudadzipempherenso moyo wautali, koma wapempha nzeru ndi luntha, kuti uzilamulira anthu anga amene ndakulongera ufumu, chabwino
12
nzeruzo ndi luntha ndikupatsa. Ndidzakupatsanso chuma, katundu ndi ulemu, zinthu zoti panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali nazo mwa mafumu amene analipo iwe usanabadwe, ndipo sipadzaonekanso wokhala nazo iweyo utafa.”
13
Motero Solomoni adachoka ku kachisi wa ku Gibiyoni pafupi ndi chihema chamsonkhano, nabwera ku Yerusalemu. Ndipo adalamulira Aisraele onse.
14
Adasonkhanitsa magaleta ndiponso anthu okwera pa akavalo. Magaletawo anali nawo 1,400, anthu okwera pa akavalo analipo 12,000. Adaŵakhazika ena ku mizinda yokhalako ankhondo ena pafupi ndi mfumu ku Yerusalemu.
15
Tsono mu Yerusalemumo mfumu idasandutsa siliva ndi golide kukhala wambiri ngati miyala wamba. Adasandutsanso mkungudza kukhala wochuluka ngati mikuyu ya m'zigwa.
16
Solomoni ankagula akavalo ku Ejipito ndi ku Kuwe. Anthu amalonda a mfumu ankalandira akavalowo ku Kuwe, atapereka ndalama.
17
Anthuwo ankagula galeta ku Ejipito pa mtengo wa masekeli asiliva 600 ndipo kavalo pa mtengo wa ndalama zasiliva 150. Momwemonso mafumu onse a Ahiti ndi a ku Siriya nawonso ankagula zinthu kudzera mwa anthu amalonda omwewo.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36