bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 31
2 Chronicles 31
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 32 →
1
Zonsezi zitatha, Aisraele onse amene analipo adapita ku mizinda ya Yuda, nakaphwanyaphwanya zipilala, kugwetsa mafano, ndi kuwononga akachisi ndiponso maguwa ku dziko lonse la Yuda, Benjamini, Efuremu ndi Manase, mpaka kuwonongeratu zonse. Pambuyo pake Aisraele onse adabwereranso kumapita kumizinda kwao, aliyense ku dziko lake.
2
Hezekiya adakhazikitsanso magulu a ansembe ndi a Alevi, gulu lililonse kutsata ntchito yake. Ansembe ndi Aleviwo ena adaŵaika kuti azipereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, ena kumatumikira ku zipata za bwalo la Chauta, ena kumathokoza ndi kutamanda.
3
Mfumu idapatula chigawo cha chuma chake, kuti zipezeke nsembe zopsereza izi: zam'maŵa, zamadzulo, za masiku a Sabata, za pachiyambi pa mwezi ndiponso za masiku a chikondwerero okhazikitsidwa, monga momwe zidalembedwera m'malamulo a Chauta.
4
Ndipo adalamula anthu a ku Yerusalemu kuti azipereka chigawo choyenera ansembe ndi Alevi, kuti pakutero ansembe ndi Aleviwo azidzipereka ku malamulo a Chauta.
5
Tsono lamulo limenelo atangolilengeza, pomwepo Aisraele adayamba kupereka kwambiri zipatso zoyamba kucha za tirigu, vinyo, mafuta, uchi ndi zonse zam'minda. Adabweranso ndi zachikhumi zambirimbiri za zinthu zonse.
6
Aisraele ndi Ayuda amene ankakhala ku mizinda ya Yuda, ankabwera ndi zigawo zachikhumi za ng'ombe ndi nkhosa, ndiponso zinthu zopatulika zimene anali atazipereka kwa Chauta, Mulungu wao, namaziika zonsezo m'milum'milu.
7
Adayamba kumaunjika milu pa mwezi wachitatu natsiriza pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri.
8
Tsono Hezekiya ndi nduna zake atabwera naona miluyo, adatamanda Chauta pamodzi ndi Aisraele anthu ao.
9
Hezekiyayo adafunsa ansembe ndi Alevi za milu ija.
10
Azariya mkulu wa ansembe amene anali wa m'banja la Zadoki, adamuyankha kuti, “Chiyambire chake cha kupereka zopereka zao ku Nyumba ya Chauta, takhala ndi zinthu zambiri zakudya, ndipo zotsalanso nzambiri. Pakutitu Chauta wadalitsa anthuwo, kotero kuti tili nazo zambirimbiri zotsalazi.”
11
Tsono Hezekiya adaŵalamula anthuwo kuti akonze zipinda za ku Nyumba ya Chauta. Iwo adakonzadi zipindazo.
12
Pambuyo pake adabwera nazo zoperekazo mokhulupirika, zigawo zachikhumi ndiponso zinthu zopatulika. Tsono kapitao wamkulu woŵayang'anira anali Konaniya Mlevi, pamodzi ndi Simei mbale wake, amene anali wachiŵiri.
13
Yehiyele, Azariya, Nahati, Asahele, Yerimoti, Yozabadi, Eliyele, Isiimakiya, Mahati, ndi Benaya, ndiwo amene anali akapitao othandiza Konaniya ndi Simei mbale wake. Mfumu Hezekiya ndiye amene adaŵasankha, pamodzi ndi Azariya amene anali kapitao wamkulu wa ku Nyumba ya Chauta.
14
Ndipo Kore, mwana wa Imina Mlevi, amene ankalonda pa chipata chakuvuma ndiye ankayang'anira nsembe zaulere zopereka kwa Mulungu. Ankapatula chigawo cha zopereka choyenera Chauta ndiponso zopereka zoyera kopambana.
15
Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya ndi Sekaniya, ndiwo amene ankamthandiza mokhulupirika ku mizinda ya ansembe, popereka magawo a zopereka kwa abale ao, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe, molingana ndi magulu ao.
16
Komanso ankapereka kwa anthu olembedwa potsata mabanja a anthu, ndiye kuti amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka kupitirirapo, amene ankaloŵa m'Nyumba ya Chauta kuti azigwira ntchito yofunika pa tsiku lake, malinga ndi nthaŵi yao ndi magulu ao.
17
Ansembe ankaŵalemba potsata mabanja a makolo ao. Alevi ankaŵalemba kuyambira anthu a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, potsata mtundu wa ntchito yao ndi magulu ao.
18
Ansembe adalembedwa pamodzi ndi ana ao onse akhanda, akazi ao, ana ao aamuna ndi aakazi, kungoti onse a m'banja mwao, chifukwa anali oyenera kudziyeretsa mokhulupirika.
19
Kunena za ansembe, ana a Aaroni amene ankakhala ku madera okhala ndi mabusa a mizinda yao, panali amuna ena m'mizinda yoŵerengeka, amene adaauzidwa pakuŵatchula maina, kuti azipereka magawo a chakudya kwa munthu wamwamuna aliyense pakati pa ansembewo, ndiponso kwa aliyense pakati pa Alevi amene adalembedwa.
20
Hezekiya adachita zimenezi ku dziko lonse la Yuda. Motero adachita zabwino, zolungama ndi zokhulupirika pamaso pa Chauta, Mulungu wake.
21
Ntchito iliyonse imene ankachita potumikira ku Nyumba ya Chauta potsata malangizo ndi malamulo, ndi pofunafuna Mulungu wake, ankachita zimenezo ndi mtima wake wonse ndipo ankapeza mwai.
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 32 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36