bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 22
2 Chronicles 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 23 →
1
Anthu okhala mu Yerusalemu adalonga ufumu Ahaziya, mzime wa Yehoramu uja, m'malo mwa bambo wakeyo, pakuti gulu lankhondo limene lidadza pamodzi ndi Arabu kuzithandoko, linali litapha ana onse akuluakulu aamuna. Motero Ahaziya, mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda, ndiye amene adaloŵa ufumu.
2
Ahaziyayo anali wa zaka 42 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira chaka chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Ataliya, mdzukulu wake wa Omuri.
3
Iyeyonso ankatsata chitsanzo cha banja la Ahabu, poti mai wake ndiye ankamupatsa uphungu woipa.
4
Adachita zoipa pamaso pa Chauta, monga momwe linkachitira banja la Ahabu. Pakuti atafa bambo wake uja, anthuwo ndiwo amene ankamupatsa uphungu pa ntchito zake zoipa.
5
Iyeyo adatsatanso uphungu wao, ndipo adapita pamodzi ndi Yoramu, mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israele, kuti akamenyane nkhondo ndi Hazaele, mfumu ya ku Siriya, ku Ramoti ku Giliyadi. Kumeneko Asiriya adamlasa Yoramu.
6
Tsono iye adabwerera napita ku Yezireele kuti akamchiritse mabala amene adaamlasa ku Rama, pamene ankamenyana ndi Hazaele mfumu ya ku Siriya. Motero Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda adapita ku Yezireele kukazonda Yoramu, mwana wa Ahabu, chifukwa chakuti ankadwala.
7
Koma Mulungu adazikonzeratu kuti Ahaziya aonongedwe pokacheza kwa Yoramuyo. Atafika kumeneko, adapita pamodzi ndi Yoramu kuti akakumane ndi Yehu, mwana wa Nimisi, amene Chauta adaamsankha kuti aononge banja la Ahabu.
8
Pamene Yehu ankalanga banja la Ahabu lija, adakumana ndi atsogoleri a ku Yuda ndiponso ana aamuna a abale ake a Ahaziya, amene ankatumikira Ahaziya, iye nkuŵapha onsewo.
9
Adafunafuna Ahaziya, ndipo adamgwira pamene ankabisala ku Samariya. Adabwera naye kwa Yehu, namupha. Anthuwo adamuika m'manda, poti ankati, “Ameneyu ndi mdzukulu wa Yehosafati uja amene ankatumikira Chauta ndi mtima wake wonse.” Choncho banja la Ahaziya linalibe munthu woti nkukhala mfumu yomalamulira.
10
Tsono Ataliya, mai wake wa Ahaziya, ataona kuti mwana wake wafa, adanyamuka nakaononga onse a pa banja laufumu la Yuda.
11
Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu, adatenga Yowasi mwana wa Ahaziya. Adachita momuba, kumuchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene ankati aŵaphewo. Adamuika m'chipinda china chogona cha m'Nyumba ya Chauta pamodzi ndi mlezi wake. Motero Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wake wa wansembe Yehoyada, poti anali mlongo wake wa Ahaziya, adambisa mwanayo, kotero kuti Ataliya sadamuphe.
12
Mwanayo adakhala ndi iwowo zaka zisanu ndi chimodzi, akubisala m'Nyumba ya Chauta, pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36