bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 23
2 Chronicles 23
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 24 →
1
Koma pa chaka chachisanu ndi chiŵiri, wansembe Yehoyada adalimba mtima, naitana anthu aŵa, amene anali atsogoleri a anthu mazana: Azariya, mwana wa Yerohamu, Ismaele mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseiya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri.
2
Iwoŵa adayendera dziko la Yuda, nasonkhanitsa Alevi onse a ku mizinda yonse ya ku Yuda ndi atsogoleri a mabanja a Aisraele, nabwera onse ku Yerusalemu.
3
Msonkhano wonsewo udachita chipangano ndi mfumu m'Nyumba ya Mulungu. Yehoyada adaŵauza anthuwo kuti, “Nayu mwana wa mfumu. Iyeyu akhale mfumu monga Chauta adanenera za ana a Davide.
4
Zimene mudzachite ndi izi: mwa inu ansembe ndi Alevi amene mukudzatumikira pa sabata, mugaŵikane patatu: gulu limodzi lidzalonde pa makomo.
5
Gulu lachiŵiri lidzalonde ku nyumba ya mfumu, gulu lachitatu lidzalonde pa khomo lakuchipata. Ndipo anthu onse adzakhale m'mabwalo a Nyumba ya Chauta.
6
Musalole aliyense kuti aloŵe m'Nyumba ya Chauta, koma ansembe ndi Alevi okha amene amatumikira. Iwo angathe kuloŵa poti ngoyeretsedwa. Anthu onse azimvera lamulo la Chauta.
7
Alevi akhale moizungulira mfumu, aliyense atatenga zida m'manja. Wina aliyense amene ati aloŵe m'Nyumbamo aphedwe. Muzikhala nayo mfumu kulikonse kumene iziyenda.”
8
Alevi ndi anthu onse a ku Yuda adachitadi zonse monga m'mene wansembe Yehoyada adaŵalamulira. Aliyense adabwera ndi anthu ake amene ankadzayamba ntchito yao yotumikira pa sabata, pamodzinso ndi anthu amene ankasiya ntchito yao yotumikira pa sabata. Pakuti wansembe Yehoyada sadaŵaloleze kuchokapo.
9
Tsono Yehoyadayo adapatsa atsogoleri aja mikondo ndi zishango zazikulu ndi zazing'ono, zimene zidaali za mfumu Davide. Zimenezi zinkasungidwa mu Nyumba ya Chauta.
10
Adandanditsa anthu onsewo kuti aziteteza mfumu, aliyense ali ndi mkondo m'manja, kuyambira kumwera kwa Nyumbayo mpaka kumpoto kwake, pafupi ndi guwa mpaka pa khomo la Nyumba kuti azizungulira mfumu.
11
Kenaka adaŵatulutsira mwana wa mfumu, namuveka chisoti chaufumu, nkumupatsa buku la malamulo, ndipo adamlonga ufumu. Tsono Yehoyada pamodzi ndi ana ake adamdzoza, anthu nafuula kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali.”
12
Tsono Ataliya atamva phokoso la anthu othamangira komweko akutamanda mfumu, adapita ku Nyumba ya Chauta kukaŵapeza anthuwo.
13
Atayang'ana, adaona mfumu itaima pa nsanja yake pa khomo, atsogoleri ndi anthu oimba malipenga ali pafupi ndi mfumuyo. Anthu onse am'deralo ankakondwa, namaimba malipenga. Anthu oimba nyimbo ali ndi zipangizo zao zoimbira, ndiwo amene ankatsogolera chikondwererocho. Pamenepo Ataliyayo adang'amba zovala zake ndipo mofuula adati, “Akundiwukira! Akundiwukira!”
14
Tsono wansembe Yehoyada adabwera nawo atsogoleri a gulu lankhondo aja naŵauza kuti, “Mtulutseni ameneyu pakati pa mizere mwandandayo. Ndipo aliyense amene amtsate, mumuphe ndi lupanga.” Wansembeyo adaanenadi kuti, “Musamphere m'Nyumba ya Chauta ai.”
15
Choncho anthuwo adamgwira Ataliya uja, ndipo atafika naye ku nyumba ya mfumu, pa khomo lotchedwa la Akavalo, adamuphera pamenepo.
16
Tsono Yehoyada adachititsa chipangano pakati pa iye mwini, ndi anthu onse ndi mfumunso, kuti iwowo akhale anthu akeake a Chauta.
17
Choncho anthu onsewo adapita ku nyumba ya Baala, nakaigwetsa. Maguwa ake ndi mafano ake adaŵaphwanyaphwanya. Kenaka anthuwo adaphanso Matani, wansembe wa Baala, patsogolo pa maguwawo pomwepo.
18
Tsono Yehoyada adaika ansembe a fuko la Levi kuti azilonda Nyumba ya Chauta. Paja Aleviwo Davide adaaŵaika kuti aziyang'anira Nyumba ya Chauta, ndi kumapereka nsembe zopsereza kwa Chauta, monga zidalembedwa m'malamulo a Mose kuti azipereka akukondwa ndipo akumaimba, potsata lamulo la Davide.
19
Iyeyo adaika alonda pa makomo a Nyumba ya Chauta, kuti wina aliyense woipitsidwa pa zachipembedzo asaloŵe.
20
Pambuyo pake adandanditsa atsogoleri, nduna, akazembe a anthu ndi anthu onse am'dzikomo. Onsewo adaperekeza mfumu kuchokera ku Nyumba ya Chauta, nakalowa m'nyumba ya mfumu podzera pa khomo lake lapamwamba; ndipo kumeneko adaikhazika mfumuyo pa mpando waufumu.
21
Motero anthu onse am'dzikomo adakondwa. Ndipo mumzindamo mudakhala bata, Ataliya ataphedwa ndi lupanga.
← Chapter 22
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 24 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36