bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 10
2 Chronicles 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 11 →
1
Tsono Rehobowamu adapita ku Sekemu. Apo nkuti Aisraele onse atapita kale ku Sekemuko, kuti akamulonge ufumu.
2
Nthaŵi imeneyo nkuti Yerobowamu, mwana wa Nebati, ali ku Ejipito, momwe adaathaŵira mfumu Solomoni muja. Tsono atamva zaufumuzo, adachokako ku Ejipito.
3
Anthu adakamuitana. Choncho Yerobowamu pamodzi ndi Aisraele onse, adadza kwa Rehobowamu namuuza kuti,
4
“Bambo wanu ankatisenzetsa goli lolemetsa kwambiri. Ndiye ife tikuti inu tsopano mudzatipeputsireko goli lolemetsalo ndi ntchito zoŵaŵa zimene bambo wanu adatisenzetsa, apo ife tidzakutumikirani.”
5
Rehobowamu adaŵauza kuti, “Mukabwerenso kuno patapita masiku atatu.” Choncho anthuwo adachoka.
6
Tsono mfumu Rehobowamu adapempha nzeru kwa madoda amene ankakhala ndi bambo wake Solomoni ndi kumamlangiza akali moyo. Adaŵafunsa kuti, “Inu mungandilangize zotani kuti ndiŵayankhe anthu ameneŵa?”
7
Madodawo adamuuza kuti, “Mukaŵachitira chifundo anthu ameneŵa ndi kumaŵasangalatsa, mukalankhula nawo mau abwino, iwowo adzakutumikirani mpaka muyaya.”
8
Koma Rehobowamu adanyozera zimene madoda aja adaamlangiza nakapempha nzeru kwa achinyamata anzake amene adaakula naye pamodzi namamtumikira.
9
Adaŵafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani kuti tiŵayankhe anthu ameneŵa amene andipempha kuti, ‘Tipeputsireniko goli limene bambo wanu adatisenzetsa?’ ”
10
Achinyamata anzakewo adamuuza kuti, “Anthuwo akupemphani kuti, ‘Bambo wanu adatisenzetsa goli lolemera, koma inu mutipeputsireko.’ Inu tsono mukaŵauze kuti, ‘Chala changa chakaninse nchachikulu kupambana chiwuno cha bambo wanga!
11
Ndiye kuti bambo wanga ankakusenzetsani goli lolemetsa, kuyambira pano ine ndidzaonjezerapo. Bambo wanga ankakukwapulani ndi zikoti wamba, koma ine ndidzakukwapulani ndi mikwapulo yachitsulo.’ ”
12
Tsono Yerobowamu ndi anthu onse adabwera kwa Rehobowamu mkucha wake, monga momwe mfumu idaanenera kuti, “Mubwerenso kuno mkucha.”
13
Ndiye mfumuyo idaŵayankha mwankhanza. Idanyonzera malangizo a madoda aja,
14
nilankhula potsata malangizo a anyamata anzake, nkunena kuti, “Bambo wanga ankakusenzetsani goli lolemetsa, koma ine ndidzaonjezerapo. Bambo wanga ankakukwapulani ndi zikoti wamba, koma ine ndidzakukwapulani ndi mikwapulo yachitsulo.”
15
Choncho mfumuyo sidamvere pempho la anthuwo, pakuti Mulungu anali atazikonzeratu zinthuzo kuti zichitikedi zimene Chauta adaalankhula ndi Yerobowamu, mwana wa Nebati, kudzera mwa Ahiya wa ku Silo.
16
Tsono Aisraele onsewo ataona kuti mfumu sidamvere zimene ankapemphazo, adayankha kuti, “Kodi ife tili ndi gawo lanjinso m'banja la Davide? Sitingayembekeze choloŵa chilichonse m'banja la mwana wa Yese. Ndiye inu Aisraele, bwererani kumahema kwanu. Tsopano iwe mwana wa Davide, udziwonere wekha pa banja lako.” Choncho Aisraele onsewo adachoka napita ku nyumba zao.
17
Koma Rehobowamu adakhala akulamulirabe Aisraele enawo okhala m'mizinda ya ku Yuda.
18
Tsono mfumu Rehobowamu adatuma Adoramu amene ankayang'anira ntchito yathangata, koma anthu a ku Israele adamponya miyala mpaka kumupha. Pamenepo, mfumu Rehobowamu adakwera msangamsanga pa galeta lake nathaŵira ku Yerusalemu.
19
Motero Aisraele akumpoto adakhala akupandukira banja la Davide mpaka lero lino.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36