bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 24
2 Chronicles 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 25 →
1
Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziŵiri pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 40 ku Yerusalemu. Mai wake anali Zibiya wa ku Beereseba.
2
Tsono Yowasiyo adachita zolungama pamaso pa Chauta nthaŵi yonse ya moyo wa wansembe Yehoyada.
3
Yehoyada adaipezera mfumuyo akazi aŵiri, ndipo idabereka ana aamuna ndi ana aakazi.
4
Pambuyo pake Yowasi adatsimikiza zokonzanso Nyumba ya Mulungu.
5
Adasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, naŵauza kuti, “Pitani ku mizinda ya Yuda, mukasonkhetse ndalama pakati pa Aisraele onse, kuti muzikonzera Nyumba ya Chauta wanu chaka ndi chaka. Muwone kuti zimenezi zichitike mwachangu.” Koma Alevi sadachite zimenezo mofulumira.
6
Motero mfumu idaitana Yehoyada mkulu wa ansembe nimfunsa kuti, “Kodi chifukwa chiyani sudaŵauze Alevi kuti asonkhetse ndalama ku Yuda ndi ku Yerusalemu, ndalama zimene adalamula Mose mtumiki wa Chauta ku mpingo wonse wa Aisraele, ndalama zokonzera hema lamsonkhano?”
7
Paja anthu ake a Ataliya, mkazi woipa uja, adaaonongapo Nyumba ya Mulungu, ndiponso adaatenga zinthu zonse zopatulika za ku Nyumba ya Chautayo, nazipereka kwa Abaala.
8
Motero mfumu idalamula kuti apange bokosi, aliike panja pa khomo la Nyumba ya Chauta.
9
Ndipo adalengeza kwa anthu onse a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu, kuti adzapereke kwa Chauta ndalama zimene Mose mtumiki wa Mulungu adaalamula kuchipululu kuja kuti Aisraele onse azipereka.
10
Tsono akalonga onse, pamodzi ndi anthu onse adakondwa, nabwera ndi ndalama zao. Ankaponya ndalamazo m'bokosimo mpaka lidadzaza lonse.
11
Nthaŵi zonse Alevi ankabwera nalo bokosilo kwa nduna zake za mfumu, akaona kuti muli ndalama zambiri. Tsono mlembi wa mfumu pamodzi ndi nduna ya mkulu wa ansembe, ankadzakhuthula ndalamazo, kenaka ankalitenga bokosilo nkulibweza pamalo pake. Umu ndimo m'mene ankachitira tsiku ndi tsiku, mwakuti adasonkha ndalama zambirimbiri.
12
Ndipo mfumu pamodzi ndi Yehoyada ankazipereka kwa akapitao oyang'anira ntchito ya ku Nyumba ya Chauta. Tsono adalemba amisiri omanga ndi miyala ndi amisiri a matabwa, kuti akonzenso Nyumba ya Chauta. Adalembanso amisiri ogwira ntchito ndi chitsulo ndi mkuŵa, kuti akonze Nyumba ya Chauta.
13
Anthu amene adalembedwawo ankagwiradi ntchito, ndipo ntchito yokonzayo idapita m'tsogolo akuigwira ndi manja ao. Choncho anthuwo Nyumba ya Chauta ija adaisandutsanso monga momwe idaaliri kale, ndipo adailimbitsa.
14
Ataimaliza, ndalama zotsala adabwera nazo kwa mfumu ndi kwa Yehoyada. Iwo adapanga ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta ndi ndalamazo, ziŵiya zogwirira ntchito ndiponso za nsembe zopsereza. Adapanganso mbale za lubani ndiponso ziŵiya zagolide ndi zasiliva. Anthu ankapereka nsembe zopsereza ku Nyumba ya Chauta kosalekeza, pa nthaŵi yonse ya Yehoyada.
15
Koma Yehoyada adakalamba kwambiri, masiku ake adachuluka, ndipo adamwalira ali wa zaka 130.
16
Adamuika m'manda ku mzinda wa Davide pamodzi ndi mafumu, chifukwa chakuti adaachita zabwino m'dziko la Israele ndipo ankatumikira Mulungu ndi Nyumba yake.
17
Yehoyada atamwalira, akalonga a ku Yuda adabwera kudzalambira mfumu, ndipo mfumu idaŵamvera.
18
Anthu adasiya Nyumba ya Chauta, Mulungu wa makolo ao, namatumikira mafano. Tsono mkwiyo wa Mulungu udagwera anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu, chifukwa cha tchimo laoli.
19
Komabe Mulungu adatuma aneneri pakati pao kuti anthuwo aŵabweze kwa Chauta. Koma aneneriwo ataŵadzudzula, anthuwo sadasamaleko ai.
20
Tsono mzimu wa Mulungu udaloŵa mwa Zekariya, mwana wa wansembe Yehoyada. Iye adaimirira pakati pa anthu naŵauza kuti, “Chauta akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukuchimwira malamulo a Chauta? Ndithu simudzapindula kanthu?’ ”
21
Koma anthuwo adamchita chiwembu, ndipo mfumu italamula, adamponya miyala m'bwalo la Nyumba ya Chauta.
22
Motero mfumu Yowasi sadakumbukire zabwino zimene Yehoyada bambo wake wa Zekariya adamchitira, koma adapha mwana wake. Ndipo pamene ankafa, mwanayo adati, “Chauta apenye, ndipo abwezere chilango.”
23
Pa kutha kwa chaka, gulu lankhondo la ku Siriya lidadzamenyana ndi Yowasi. Adabwera ku Yuda ndi ku Yerusalemu, napha akazembe onse a anthu pakati pa anthuwo. Ndipo adatumiza zofunkha zao zonse kwa mfumu ya ku Damasiko.
24
Ngakhale gulu lankhondo la ku Siriya lidadza ndi anthu ochepa, Chauta adapereka m'manja mwao gulu lalikulu kwambiri la ankhondo, chifukwa chakuti anthuwo anali atasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao. Umu ndimo m'mene anthu a ku Siriya adalangira Yowasi.
25
Asiriya aja atamsiya wovulazidwa kwambiri, anyamata ake adamchita chiwembu, chifukwa cha magazi a mwana wa Yehoyada wansembe uja, ndipo adamphera pabedi pake. Motero iyeyo adafa. Ndipo adamuika m'manda mu mzinda wa Davide, koma sadamuike m'manda a mafumu.
26
Anthu amene adamchita chiwembuwo ndi Zabadi mwana wa Simea Mwamoni, ndi Yehozabadi mwana wa Simeriti Mmowabu.
27
Za ana ake aamuna ndiponso za mau ambiri omtsutsa iyeyo, kudzanso za kumanganso Nyumba ya Chauta, izo zidalembedwa m'buku lofotokoza za mafumu. Ndipo Amaziya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36