bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 13
2 Chronicles 13
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 14 →
1
Pa chaka cha 18 cha ufumu wa Yerobowamu, Abiya adaloŵa ufumu wa ku Yuda.
2
Adakhala mfumu mu Yerusalemu zaka zitatu. Mai wake anali Maaka, mwana wa Uriyele wa ku Gibea. Tsono panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu.
3
Abiya adanyamuka kupita ku nkhondo atatenga gulu lake la ankhondo olimba mtima okwanira 400,000 osankhidwa. Yerobowamu adandanditsa ankhondo ake oti amenyane ndi Abiya, anthu okwanira 800,000, amphamvu ndi osankhidwa.
4
Tsono Abiya adaima pa phiri la Zemaraimu, limene lili ku dziko lamapiri la Efuremu, ndipo adati, “Iwe Yerobowamu, pamodzi ndi Aisraele onse, imvani zimene ndikunenazi.
5
Kodi simukudziŵa kuti Chauta, Mulungu wa Israele, adapereka ufumu wa Israele kwa Davide ndi kwa ana ake mpaka muyaya, pochita chipangano chosaphwanyika?
6
Komabe Yerobowamu mwana wa Nebati, mtumiki wa Solomoni mwana wa Davide, adanyamuka naukira mbuyakeyo.
7
Ndipo anthu ena achabechabe adasonkhana kwa iye nachita chipongwe Rehobowamu mwana wa Solomoni pa nthaŵi imene Rehonowamu anali wamng'ono ndi wosalimba mtima, ndipo sankatha kulimbana nawo.
8
“Tsopano inu mukuganiza zolimbana ndi ufumu wa Chauta ndi kuulanda m'manja mwa ana a Davide, poti inuyo ndinu ambirimbiri. Ndipo muli nawo mafano agolide, a anaang'ombe amene Yerobowamu adakupangirani, kuti akhale milungu yanu.
9
Kodi inu simudapirikitsa ansembe a Chauta, ana a Aaroni, ndiponso Alevi, ndipo mudadzisankhira ansembe anuanu, monga amachitira anthu a mitundu ina am'maikomo? Munthu aliyense amene amabwera kuti adzipereke atatenga mwanawang'ombe wamphongo kapena nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, amasanduka wansembe wa zinthu zimene sizili milungu konse.
10
Koma kunena za ife, Chauta ndiye Mulungu wathu, ndipo sitidamsiye ai. Tili nawo ansembe, ana a Aaroni, otumikira Chauta, tilinso ndi Alevi amene amatumikira ansembewo.
11
Iwowo amapereka kwa Chauta nsembe zopsereza m'maŵa mulimonse ndi madzulo aliwonse. Amafukiza lubani wonunkhira bwino, amaikanso buledi wopereka pa tebulo la golide weniweni, namasamala zoikapo nyale zagolide, kuti nyale zake ziziyaka madzulo aliwonse. Ife timasunga zimene Chauta Mulungu wathu amatilamula, koma inuyo mudamsiya.
12
Onani, Mulungu ali nafe, akutitsogolera, ansembe ake atatenga malipenga ao ankhondo otiitanira ku nkhondo yokamenyana ndi inu. Inu ana a Israele, musati mulimbane ndi Chauta, Mulungu wa makolo anu, chifukwa simungathe kupambana.”
13
Yerobowamu anali atatumiza anthu obisalira, kuti alimbane nawo moŵadzera kumbuyo. Motero magulu ankhondowo anali kutsogolo kwa anthu a ku Yuda, ndipo obisalirawo anali kumbuyo kwao.
14
Anthu a ku Yuda aja poyang'ana, adangoona kuli nkhondo kutsogolo kwao ndi kumbuyo komwe. Tsono adafuula kwa Chauta, ndipo ansembe adayamba kuliza malipenga.
15
Apo anthu a ku Yuda adafuula, kufuula kwake kwankhondo. Ndipo anthu a ku Yudawo atafuula, Mulungu adagonjetsa Yerobowamu pamodzi ndi anthu a ku Israele onse, pamaso pa Abiya ndi pa anthu a ku Yuda.
16
Aisraele adathaŵa Ayuda, ndipo Mulungu adapereka Aisraelewo kwa Ayuda.
17
Abiya pamodzi ndi anthu ake adapha Aisraelewo, kupha kwake kwakukulu. Adaphedwa Aisraele okwanira 500,000, anthu ndithu osankhidwa.
18
Motero Aisraele adagonjetsedwa nthaŵi imeneyo, ndipo Ayuda adapambana chifukwa chakuti adakhulupirira Chauta, Mulungu wa makolo ao.
19
Tsono Abiya uja adapirikitsa Yerobowamu, namlanda mizinda iyi: Betele ndi midzi yake, Yasana ndi midzi yake, ndiponso Efuroni ndi midzi yake.
20
Yerobowamu sadapezenso mphamvu nthaŵi ya Abiya. Ndipo Chauta adamkantha Yerobowamu, naafa.
21
Koma Abiya mphamvu zake zidakula. Ndipo adakwatira akazi khumi ndi anai, nabala ana aamuna 22 ndi ana aakazi 16.
22
Ntchito zonse za Abiya, makhalidwe ake ndi zimene ankalankhula zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Ido.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36