bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 33
2 Chronicles 33
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 34 →
1
Manase anali wa zaka khumi ndi ziŵiri pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 55 ku Yerusalemu.
2
Iyeyu adachita zoipa pamaso pa Chauta potsata ntchito zonyansa za anthu a mitundu ina, amene Chauta adaaŵapirikitsa pofika Aisraele.
3
Adayambitsanso akachisi amene bambo wake Hezekiya adaaŵaononga. Adapanganso maguwa a Abaala ndiponso mafano, namapembedza zinthu zonse zamumlengalenga, ndi kumazitumikira.
4
Adamanga maguwa achikunja m'Nyumba ya Chauta imene Chauta mwini wake anali atanena kuti, “Dzina langa lidzakhala ku Yerusalemu mpaka muyaya.”
5
Adamanga maguwa m'mabwalo aŵiri a Nyumba ya Chauta, kumangira zolengedwa zonse zamumlengalenga.
6
Ndipo adapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza. Adachita zimenezi ku chigwa cha mwana wa Hinomu, ndipo ankachita zobwebwetetsa, namasamala zamalodza ndi zanyanga, nkumamvana ndi anthu olankhula ndi mizimu ndi anthu amatsenga. Adachita zoipa zambiri pamaso pa Chauta, naputa mkwiyo wake.
7
Tsono m'Nyumba ya Chauta adaikamo fano lopanga iyeyo, Nyumba imene Mulungu adaauza Davide ndi Solomoni mwana wake kuti, “M'nyumba imeneyi, mu Yerusalemu muno, malo amene ndaŵasankhula pakati pa mafuko onse a Aisraele, ndimo m'mene adzatamandira dzina langa mpaka muyaya.
8
Ndipo sindidzachotsa phazi la Israele m'dziko limene ndidapatsa makolo anu, pokhapokha akamasamala ndi kuchita zonse zimene ndidaŵauza pakumvera malamulo ndi malangizo onse amene ndidaŵapatsa kudzera mwa Mose.”
9
Manase adachimwitsa anthu a ku Yuda pamodzi ndi anthu okhala mu Yerusalemu. Ankachita zoipa zambiri kupambana anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵaononga pofika Aisraele.
10
Chauta adalankhula ndi Manase ndiponso ndi anthu ake, koma iwo sadasamaleko.
11
Nchifukwa chake Chautayo adaŵatumira atsogoleri ankhondo a mfumu ya ku Asiriya kudzamenyana naye Manase. Adamkoka ndi ngowe zachitsulo nammanga ndi maunyolo amkuŵa, nkupita naye ku Babiloni.
12
Ndiye pamene anali pa mavuto, adapempha kuti Chauta, Mulungu wake, amkomere mtima, ndipo adadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake.
13
Atapemphera kwa Iye, Mulungu adamva kupempha kwake ndi kupemba kwake, ndipo adambwezanso ku Yerusalemu mu ufumu wake. Motero Manase adadziŵa kuti Chauta ndi Mulungu.
14
Pambuyo pake adamanga khoma la kunja kwa mzinda wa Davide kuzambwe kwake kwa Gihoni, kuchokera ku chigwa mpaka poloŵera ku Chipata cha Nsomba. Ndipo adamanga khomalo kuzungulira Ofele nalikweza kwambiri. Adaikanso atsogoleri ankhondo ku mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda.
15
Adachotsa milungu yachilendo ndiponso fano m'Nyumba ya Mulungu. Adachotsa maguwa onse achikunja amene anali ataŵamanga pa phiri la Chauta ku Yerusalemu. Ndipo adaŵataya kunja kwa mzinda.
16
Adamanganso guwa la Chauta, namaperekerapo nsembe zachiyanjano ndiponso nsembe zothokozera. Tsono adalamula anthu a ku Yuda kuti azitumikira Chauta Mulungu wa Israele.
17
Anthuwo ankaperekabe nsembe ku akachisi, koma kwa Chauta, Mulungu wao yekha.
18
Tsono ntchito zina zonse za Manase, pamodzi ndi pemphero lake kwa Mulungu wake, ndiponso mau a aneneri amene adalankhula naye m'dzina la Chauta, Mulungu wa Israele, zidalembedwa m'buku la mbiri ya mafumu a ku Israele.
19
Ndipo pemphero lake ndi m'mene Mulungu adalilandirira pemphero lakelo, machimo ake onse, kusakhulupirika kwake, akachisi amene adayambitsa, m'mene adakhazikitsira mafano ndi zithunzi zina, asanadzichepetse paja, zonsezi zidalembedwa m'buku la mbiri ya aneneri.
20
Choncho Manase adamwalira, naikidwa m'nyumba mwake. Tsono Amoni mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
21
Amoni anali wa zaka 22 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka ziŵiri ku Yerusalemu.
22
Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta monga m'mene ankachitira Manase bambo wake. Amoniyo ankapereka nsembe kwa mafano onse amene bambo wake adaŵapanga, ndipo ankaŵatumikira.
23
Sadadzichepetse pamaso pa Chauta monga momwe Manase bambo wake adadzichepetsera. Koma Amoniyu ankadzipereka ku machimo kosalekeza.
24
Tsono anyamata ake adamchita chiwembu, namupha m'nyumba mwake.
25
Koma anthu am'dzikomo adapha onse aja amene adamchita chiwembu Amoniyo. Kenaka anthuwo adalonga Yosiya mwana wake kuti akhale mfumu m'malo mwake.
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 34 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36