bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 15
2 Chronicles 15
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 16 →
1
Mzimu wa Mulungu udamtsikira Azariya mwana wa Odedi.
2
Tsono iye adatuluka mu mzinda wake kukakomana ndi Asa, ndipo adamuuza kuti, “Ndimvereni inu Asa, Ayuda nonsenu ndi inu Abenjamini. Chauta ali nanu nthaŵi yonse imene inu muli ndi Iye. Mukamfunafuna mudzampeza. Koma mukamsiya, nayenso adzakusiyani.
3
Pa nthaŵi yaitali Aisraele adakhala opanda Mulungu woona, ndiponso opanda wansembe woŵaphunzitsa, ndipo analibe malamulo.
4
Koma pamene anali pa mavuto, namabwera kudzafunafuna Chauta, Mulungu wa Israele, ankamupeza.
5
Pa masiku amenewo panalibe mtendere kwa munthu amene ankatuluka kapena kuloŵa, pakuti mavuto adaaŵagwera onse amene ankakhala m'makomo.
6
Anthuwo adagalukirana, mtundu wina unkamenyana ndi mtundu wina, mzinda unkamenyana ndi mzinda wina, pakuti Mulungu adaaŵavuta ndi mazunzo osiyanasiyana.
7
Koma inu limbani mtima, manja anu asafooke chifukwa mudzalandira mphotho ya ntchito yanu.”
8
Tsono Asa atamva mau ameneŵa, mau aulosi a Azariya mwana wa Odedi, adalimba mtima. Adachotsa mafano onyansa ku dziko lonse la Yuda ndi la Benjamini. Adachotsanso mafano ku mizinda imene adailanda ku dziko lamapiri la Efuremu. Ndipo adakonza guwa la Chauta limene linali patsogolo pa khonde la Nyumba ya Chauta.
9
Adasonkhanitsa Ayuda onse ndi Abenjamini ndiponso anthu a ku Efuremu, Manase ndi Simeoni amene ankangokhala nao, pakuti anthu ambiri anali atathaŵira kwa mfumu Asa, kuchoka ku Israele, ataona kuti Chauta Mulungu wake anali naye Asayo.
10
Anthuwo adasonkhana ku Yerusalemu pa mwezi wachitatu chaka cha 15 cha ufumu wa Asa.
11
Tsiku limenelo adapereka nsembe kwa Chauta zotapako pa za zofunkha zimene adaabwera nazo, ndiye kuti ng'ombe 700, ndi nkhosa 7,000.
12
Tsono adapangana zoti azifunafuna Chauta, Mulungu wa makolo ao, ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse.
13
Adaamvana kuti aliyense wosafunafuna Chauta, Mulungu wa Israele, aziphedwa, kaya ndi wamng'ono kaya wamkulu, wamwamuna kapena wamkazi.
14
Zimenezi adalumbira kwa Chauta mokweza mau ndi mofuula, alikuliza malipenga ndi mbetete.
15
Ndipo anthu onse a ku Yuda adakondwa pa mwambo wolumbirirawo, pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse. Ankafunafuna Chauta kwambiri, ndipo adampezadi. Motero Chauta adaŵapatsa mtendere ponse poŵazungulira.
16
Mfumu Asa adachotsa ngakhale ufumu wa Maaka, gogo wake, chifukwa choti Maakayo anali atachita chinthu choipa kwambiri popanga fano. Asa adagwetsa fanolo, nalitswanya, ndipo adakalitentha ku mtsinje wa Kidroni.
17
Koma akachisi sadaŵaononge ku Israele. Ngakhale zinali choncho, mtima wa Asa udakhala wangwiro masiku onse a moyo wake.
18
Ndipo adabwera ku Nyumba ya Chauta ndi mphatso zimene bambo wake adaapereka, ndiponso zopereka iye mwini, monga siliva, golide ndi ziŵiya.
19
Tsono panalibenso nkhondo mpaka chaka cha 35 cha ufumu wa Asa.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36