bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 26
2 Chronicles 26
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 27 →
1
Pambuyo pake anthu onse a ku Yuda adatenga Uziya, wa zaka 16, namlonga ufumu m'malo mwa Amaziya bambo wake.
2
Iyeyo adamanga mzinda wa Eloti naubwezera ku Yuda, mfumu itamwalira.
3
Uziyayo anali wa zaka 16 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 52 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yekoliya wa ku Yerusalemu.
4
Adachita zolungama pamaso pa Chauta, monga momwe ankachitira bambo wake Amaziya.
5
Adadzipereka kwa Mulungu pa nthaŵi ya Zekariya amene ankamphunzitsa Uziyayo kuti azilemekeza Mulungu. Ndipo nthaŵi zonse pamene ankadzipereka kwa Chauta, Mulungu ankamupezetsa bwino.
6
Nthaŵi ina Uziya adakamenyana nkhondo ndi Afilisti, nagwetsa linga la Gati ndi la Yabine ndiponso la Asidodi. Kenaka adamanga mizinda m'dziko la Asidodi ndi kwinanso m'dziko la Afilisti.
7
Mulungu adamthandiza pomenyana ndi Afilisti, ndi Arabu amene ankakhala ku Guribaala, ndiponso pomenyana ndi Ameuni.
8
Aamoni ankakhoma msonkho kwa Uziya, ndipo mbiri yake idamveka mpaka ku malire a Ejipito, poti anali wamphamvu kwambiri.
9
Kuwonjezera pamenepo, Uziya adamanga nsanja ku Yerusalemu ku Chipata cha ku Ndonyo, Chipata cha ku Chigwa ndi pa Mphindiko ya linga, ndipo adazilimbitsa.
10
Pambuyo pake adamanga nsanja ku chipululu ndi kukumba zitsime zambiri, poti anali ndi ziŵeto zambiri ku madambo ndi ku zigwa. Analinso ndi anthu olima minda ndi anthu omasamala mphesa ku mapiri, ndiponso ku maiko achonde, poti ankakonda kulima.
11
Komanso Uziyayo anali ndi gulu la asilikali odziŵa nkhondo. Anali m'magulumagulu potsata dongosolo limene adaalikonza mlembi Yeiyele ndi Maaseiya, mkulu wankhondo. Amene ankaŵalamulira asilikaliwo anali Hananiya, mmodzi mwa nduna za mfumu.
12
Chiŵerengero chonse cha atsogoleri amphamvu, olimba mtima, akulu a mabanja, chinali 2,600.
13
Atsogoleri ameneŵa ankalamulira gulu lankhondo lokwanira asilikali 307,500, amene ankatha kumenya nkhondo mwamphamvu, kuthandiza mfumu polimbana ndi adani.
14
Ndipo adapangira asilikaliwo zishango, mikondo, zisoti zankhondo, malaya ankhondo achitsulo, mauta, ndi miyala yoponyera.
15
Ku Yerusalemu anthu aluso adapanga makina amene ankaŵakweza pa nsanja ndi pa malo onse andonyo, kuti anthu aziponyera mivi ndiponso miyala ikuluikulu. Choncho mbiri ya Uziya idamveka nikafika kutali, chifukwa anali atathandizidwa kodabwitsa, mpaka adakhala wamphamvu.
16
Koma Uziyayo mphamvu zake zitachuluka, adayamba kunyada ndipo kunyada kwakeko kudamuwonongetsa. Anali wosakhulupirika kwa Chauta Mulungu wake, ndipo adaloŵa ku Nyumba ya Chauta kuti akafukize lubani pa guwa lofukizapo lubani.
17
Koma wansembe Azariya adaloŵa pambuyo pa iyeyo, pamodzi ndi ansembe a Chauta 80 olimba mtima.
18
Tsono ansembewo adamletsa mfumu Uziya namuuza kuti, “Pepani, mfumu Uziya, sindinu amene muyenera kufukiza lubani kwa Chauta, koma ansembe, ana a Aaroni, amene adaŵapatula kuti azifukiza lubani. Chokaniko ku malo opatulika kwambiriŵa. Kutereku mwalakwa, ndipo ulemerero wa Chauta wakuchokerani.”
19
Apo Uziya adapsa mtima. Tsono m'manja mwake munali chofukizira lubani. Ndipo atakwiyira ansembewo, khate lidatuluka pamphumi pake, ansembe aja akuwona, m'Nyumba ya Chauta, pafupi ndi guwa lofukizirapo lubani.
20
Azariya mkulu wa ansembe, pamodzi ndi ansembe onse atamuyang'ana, adangoona kuti wachita khate pa mphumi. Ansembewo adamkankhira kunja mwamsanga, ndipo iye mwini wake adatuluka msangamsanga, chifukwa chakuti Chauta adaamlanga.
21
Uziya adakhala wakhate mpaka pa tsiku la kufa kwake. Tsono popeza kuti anali wakhate, ankakhala m'nyumba ya yekha, chifukwa anali atachotsedwa ku Nyumba ya Chauta. Motero Yotamu mwana wake ndiye amene ankayang'anira za ku nyumba ya mfumu, namalamulira anthu am'dzikomo.
22
Ntchito zonse za Uziya kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, adazilemba mneneri Yesaya, mwana wa Amozi.
23
Tsono Uziya adalondola makoko ake ndipo adamuika pamodzi ndi makolo ake ku malo a manda a mafumu, osati m'manda mwaomo, poti anthu ankati, “Iyeyu ndi wakhate.” Ndipo Yotamu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
Recommended Reading
Commentary
2 Chronicles Commentaries
→
Devotional
2 Chronicles Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→