bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 18
2 Chronicles 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 19 →
1
Yehosafati anali ndi chuma chambiri ndi ulemerero waukulu. Tsono adachita chigwirizano chaukwati ndi banja la Ahabu.
2
Patapita zaka zina, Yehosafatiyo adapita kwa Ahabu ku Samariya. Ahabuyo adapha nkhosa ndi ng'ombe zambirimbiri kuphera Yehosafatiyo ndi anthu amene anali naye, pofuna kumkopa kuti akalimbane ndi Ramoti-Giliyadi.
3
Ndiye Ahabu mfumu ya ku Israele adafunsa Yehosafati mfumu ya ku Yuda kuti, “Kodi udzapita nane limodzi ku Ramoti-Giliyadi?” Iyeyo adayankha kuti, “Ine ndili nanu limodzi, anthu anga nganu. Ifeyo tidzakhala nanu pa nkhondo.”
4
Yehosafati adauza mfumu ya ku Israele kuti, “Poyamba upemphe nzeru kwa Chauta.”
5
Tsono mfumu ya ku Israele idasonkhanitsa aneneri ake 400, ndipo idaŵafunsa kuti, “Kodi ife tipite kukamenyana nkhondo ndi Ramoti-Giliyadi, kaya kapena ineyo ndileke?” Aneneriwo adamuuza kuti, “Pitani, pakuti Mulungu aupereka mzindawo kwa inu mfumu.”
6
Koma Yehosafati adafunsa kuti, “Kodi pano palibe mneneri wina wa Chauta woti tipempheko nzeru?”
7
Mfumu ya ku Israele idauza Yehosafati kuti, “Alipo wina amene angapemphe nzeru kwa Chauta, dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imila. Koma ine ndimadana naye ameneyo popeza kuti sandilosera zabwino, nthaŵi zonse amangondilosera zoipa.” Tsono Yehosafati adati, “Iyai mfumu, musatero.”
8
Apo mfumu ya ku Israele idaitana imodzi mwa nduna nkuiwuza kuti, “Takaitanani Mikaya, mwana wa Imila, abwere kuno msanga.”
9
Nthaŵi imeneyo mfumu ya ku Israele ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda adaakhala pa mipando yao yaufumu, atavala zovala zao zaufumu. Pamenepo panali pa bwalo lopererapo tirigu, pa khomo la chipata cha Samariya. Ndipo aneneri onse ankalosa pamaso pa mafumuwo.
10
Wina mwa iwo, Zedeki, mwana wa Kenana, adaadzisulira nyanga zachitsulo. Iyeyo adati, “Chauta akunena kuti, ‘Ndi nyangazi udzamegonjetsa Asiriya ndi kuŵaonongeratu.’ ”
11
Aneneri onsewo adalosa chimodzimodzi, adati, “Pitani ku Ramoti-Giliyadi, ndipo mukapambana. Chauta aupereka mzindawo kwa inu mfumu.”
12
Wamthenga uja amene adaapita kukaitana Mikaya, adamuuza Mikayayo kuti, “Onani, mau onse amene akunena aneneri, akulosera mfumu zabwino. Ndiye nanunso mau anu akhale ofanafana ndi mau awo. Muzilosa zabwino.”
13
Koma Mikaya adati, “Pali Chauta wamoyo, zimene Mulungu wanga andiuze, ndizo ndidzalankhule.”
14
Tsono atafika kwa Ahabu, mfumuyo idamufunsa kuti, “Kodi Mikaya, ife tipite kukamenya nkhondo ku Ramoti-Giliyadi, kapena ineyo ndileke?” Iye adayankha kuti, “Pitani, mukapambana, anthuwo akaperekedwa kwa inu.”
15
Koma mfumuyo idamufunsa kuti, “Kodi ndikulumbiritse kangati, kuti undiwuze zoona zokhazokha m'dzina la Chauta?”
16
Mikaya adati, “Ndidaona Aisraele onse atamwazikana pa mapiri ngati nkhosa zopanda mbusa. Tsono Chauta adati, ‘Ameneŵa alibe mbuyawo. Aliyense apite kwao mwamtendere.’ ”
17
Pamenepo mfumu ya ku Israele adauza Yehosafati kuti, “Suja ndidaakuuzani kuti ameneyu sadzandilosera zabwino koma zoipa zokha?”
18
Apo Mikaya adati, “Mverani tsono mau a Chauta. Ine ndidapenya Chauta atakhala pa mpando wake waufumu, gulu lonse lakumwamba litaima ku dzanja lake lamanja ndi ku dzanja lake lamanzere.
19
Tsono Chauta adati, ‘Kodi ndani amene akamnyengerere Ahabu mfumu ya ku Israele, kuti akafe ku Ramoti-Giliyadi?’ Wina ankanena zina, winanso nkumanena zina.
20
Apo mzimu wina udadzaima pamaso pa Chauta, nunena kuti, ‘Ndikamnyengerera ndine.’ Tsono Chauta adaufunsa kuti, ‘Ukamnyengerera bwanji?’
21
Udati, ‘Ndidzapita, nkumakanena zabodza kudzera mwa aneneri ake onse.’ Pamenepo Chauta adati, ‘Ukakatero, ukakhozadi. Pita ukamnyengerere.’
22
Tsonotu ngati Chauta waika mzimu wabodza m'kamwa mwa aneneri anuŵa, ndiye kuti Iye yemwe waneneratu kuti mukaona tsoka.”
23
Tsono Zedeki uja, mwana wa Kenana, adadza pafupi namenya Mikaya pa tsaya, namufunsa kuti, “Kodi mzimu wa Chauta udadzera njira iti kuti uchoke mwa ine, uzikalankhula ndi iwe?”
24
Mikaya adati, “Udzadziŵa pa tsiku limene uzikaloŵa m'chipinda china ndi china cham'kati kuti ukabisale.”
25
Pamenepo Ahabu, mfumu ya ku Israele, adati, “Mgwireni Mikayayu, mupite naye kwa Amoni, mkulu wa mzinda, ndiponso kwa Yowasi mwana wa mfumu.
26
Mukaŵauze mau angaŵa akuti, ‘Munthu uyu muikeni m'ndende, ndipo muzimpatsa chakudya pang'ono ndi madzi pang'ono, mpaka ine nditabwerera mwamtendere.’ ”
27
Mikaya adati, “Mukabwerera mwamtendere, ndiye kuti Chauta sadalankhule kudzera mwa ine.” Ndipo adaonjeza kuti, “Anthu nonsenu, mumve zimene ndanenazi.”
28
Zitatero Ahabu, mfumu ya ku Israele, ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda, adapita ku Ramoti-Giliyadi.
29
Mfumu ya ku Israele idauza Yehosafati kuti, “Ine ndidzizimbayitsa, ndipo ndipita kunkhondoko, koma iwe uvale malaya ako aufumu.” Choncho mfumu ya ku Israele idadzizimbayitsa, onsewo nkupita ku nkhondo.
30
Mfumu ya ku Siriya nkuti italamula oyendetsa magaleta kuti asamenye nkhondo ndi wina aliyense, wamng'ono kapena wamkulu, koma mfumu ya ku Israele basi.
31
Tsono pamene oyendetsa magaletawo adaona Yehosafati, adati, “Ndithudi ameneyo ndiye mfumu ya ku Israele.” Choncho adabwerera kudzalimbana naye. Koma Yehosafati adayamba kufuula, ndipo Chauta adamthandiza. Mulungu adaŵabweza m'mbuyo.
32
Ndiye kuti oyendetsa magaleta aja ataona kuti ameneyu si mfumu ya ku Israele, adabwerera osamtsatanso.
33
Koma munthu wina adakoka uta wake mwachiponyeponye, ndipo adalasa mfumu ya ku Israele pa maluma a malaya ake achitsulo. Pamenepo mfumuyo idauza woyendetsa galeta lake kuti, “Bwerera, undichotse pankhondo pano chifukwa ndavulazidwa.”
34
Nkhondo idakula kwambiri tsiku limenelo, mwakuti mfumu ya ku Israeleyo idangokhala tsonga m'galeta lake itayang'anana ndi Asiriya mpaka madzulo. Motero pamene dzuŵa linkaloŵa, idafa.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36