bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 20
2 Chronicles 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 21 →
1
Nthaŵi ina, Amowabu, Aamoni ndi Ameuni ena adabwera kudzamenyana nkhondo ndi Yehosafati.
2
Anthu ena adadzauza Yehosafati kuti “Chinamtindi cha anthu chikudzamenyana nanu nkhondo, kuchokera ku Edomu patsidya pa nyanja. Anthuwo ali ku Hazazoni-Tamara,” (ndiye kuti Engedi).
3
Pamenepo Yehosafati adachita mantha, ndipo adaganiza zopempha nzeru kwa Chauta, nalengeza kuti anthu onse a ku dziko la Yuda asale zakudya.
4
Ayuda onse adasonkhana kuti adzapemphe chithandizo kwa Chauta. Anthu onse a ku mizinda yonse ya ku Yuda adabwera kudzapempha chithandizo kwa Chauta.
5
Tsono Yehosafati adaimirira pakati pa msonkhano wa Ayuda ku Yerusalemu m'Nyumba ya Chauta pa bwalo latsopano.
6
Ndipo adati, “Chauta, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu Wakumwamba? Kodi suja mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu? M'manja mwanu muli mphamvu ndi nyonga, kotero kuti palibe ndi mmodzi yemwe woti nkulimbana nanu.
7
Kodi Inu, Mulungu wathu, suja mudapirikitsa nzika za dziko lino pamene ankafika Aisraele, anthu anu, ndi kulipereka kwa zidzukulu za Abrahamu, bwenzi lanu mpaka muyaya?
8
Mwakuti iwo atakhazikika m'dziko limenelo, adakumangirani Nyumba m'menemo, nkumati,
9
‘Choipa chikatigwera mwachilango, monga nkhondo, mlili kapena njala, tidzaima m'Nyumba ino ndiponso pamaso panu, popeza kuti dzina lanu lili m'Nyumba muno. Tsono tidzalira kwa Inu pa mavuto athu, Inuyo mudzamva, ndipo mudzatipulumutsa.’
10
Pajatu pamene Aisraele ankachoka ku Ejipito, simudalole kuti aŵathire nkhondo Aamoni, Amowabu ndi anthu a ku phiri la Seiri. Onsewo adaŵaleka osaŵaononga.
11
Koma tsopano chimene akutibwezera nkudzatipirikitsa m'dziko limene Inu mudatipatsa kuti likhale choloŵa chathu.
12
Inu Mulungu wathu, monga simuŵalanga iwoŵa? Ife tilibe mphamvu zoti nkulimbana nacho chinamtindi chikudzatithira nkhondocho. Tikusoŵa chochita, maso athu ali pa Inu.”
13
Nthaŵi imeneyo nkuti anthu onse a dziko la Yuda ataimirira pamaso pa Chauta, pamodzi ndi akazi ao ndi ana ao ndi ang'onoang'ono omwe.
14
Ndipo mumsonkhanomo mzimu wa Chauta udatsikira Yehaziele, mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyele, mwana wa Mataniya, mlevi, mmodzi mwa ana a Asafu.
15
Iyeyo adati, “Mverani Ayuda nonsenu, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu, ndi inunso mfumu Yehosafati. Chauta akukuuzani kuti, ‘Musaope, ndipo musataye nacho mtima chinamtindi cha anthuchi, pakuti nkhondo si yanu, nja Mulungu.
16
Maŵa mupite mukamenyane nawo nkhondo. Adzabwera ndipo adzadzera cha ku chikwera cha Zizi. Mudzaŵapeza pafupi ndi chigwa cha kuvuma kwa chipululu cha Yeruwele.
17
Sikudzafunika kuti mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale m'malo mwanu, mungoima, ndipo muwonerere Chauta akukumenyerani nkhondo, inu anthu a ku Yuda ndi inu anthu a mu Yerusalemu.’ Musaope ndipo musataye mtima, mutuluke maŵa mukalimbane nawo, Chauta adzakhala nanu.”
18
Apo Yehosafati adazyolikitsa nkhope yake pansi, ndipo anthu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yerusalemu adagwa pansi pamaso pa Chauta nampembedza.
19
Kenaka Alevi, ana a Kohati ndi ana a Kora, adaimirira kuti atamande Chauta, Mulungu wa Aisraele, mokweza kwambiri.
20
Tsono anthuwo adadzuka m'mamaŵa nakaloŵa m'chipululu cha ku Tekowa. Pamene ankatuluka, Yehosafati adaima nati, “Tamverani inu anthu a ku Yuda ndi inu okhala mu Yerusalemu. Khulupirirani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalimbika, khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzapambana.”
21
Tsono ataŵafunsa anthuwo, adasankha ena oti aziimbira Chauta ndi kumtamanda, oimbawo atavala zovala zoyera, akutsogolera gulu lankhondo namanena kuti, “Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.”
22
Iwo aja atayamba kuimba ndi kutamanda, Chauta adaŵatchera msampha Aamoni, Amowabu ndiponso anthu a ku phiri la Seiri, amene adaadzalimbana ndi anthu a ku Yuda, kotero kuti adaŵagonjetsa onse.
23
Aamoni ndi Amowabu adaukira anthu okhala ku phiri la Seiri, naŵaononga kotheratu. Ndipo ataononga anthu onse a ku Seiri aja, adayamba kumaphana okhaokha.
24
Pambuyo pake anthu a ku Yuda atafika ku nsanja yakuchipululu, adapenya kumene kunali chinamtindi cha anthu chija. Adangoona mitembo yokhayokha ili pansi ngundangunda. Panalibe ndi mmodzi yemwe wopulumuka.
25
Tsono Yehosafati ndi anthu ake atadzafunkha za anthuwo, adapeza ng'ombe zambirimbiri, katundu, zovala ndiponso zinthu zamtengowapatali. Adatenga zinthu zochuluka, mpaka kuzilephera. Adafunkha zinthuzo masiku atatu, chifukwa zinali zambirimbiri.
26
Pa tsiku lachinai lake, adasonkhana ku chigwa cha Beraka, ndipo kumeneko adatamanda Chauta. Nchifukwa chake malowo amatchedwa chigwa cha Beraka mpaka lero lino.
27
Tsono onsewo a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu adabwerera mokondwa ku Yerusalemu, Yehosafati akuŵatsogolera, pakuti Chauta adaŵakondweretsa poŵagonjetsera adani ao.
28
Anthuwo adafika ku Yerusalemu, ku Nyumba ya Chauta, akuimba azeze, apangwe ndiponso malipenga.
29
Ndipo maufumu onse a m'maiko achilendowo adachita mantha kwambiri, atamva kuti Chauta ndiye adathira nkhondo pa adani a Aisraele.
30
Motero mudakhala bata mu ufumu wonse wa Yehosafati, pakuti Mulungu adampatsa mtendere ku maiko onse omzungulira.
31
Choncho Yehosafati adayamba kulamulira Yuda. Anali wa zaka 35 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 25 ku Yerusalemu. Mai wake anali Azuba, mwana wa Sili.
32
Yehosafati ankayenda motsata chitsanzo chabwino cha Asa atate ake. Sadapatuke pa zimenezo. Ankachita zolungama pamaso pa Chauta.
33
Komabe akachisi opembedzerako mafano sadaŵaononge. Anthu anali asanapereke mitima yao kwa Mulungu wa makolo ao.
34
Tsono ntchito zonse zimene adachita Yehosafati kuyambira poyamba mpaka potsiriza, zidalembedwa m'buku la mbiri ya Yehu, mwana wa Hanani, limene lili chigawo cha buku lokamba za mafumu a Aisraele.
35
Zitapita zimenezi, Yehosafati mfumu ya ku Yuda, adagwirizana ndi Ahaziya mfumu ya ku Israele, amene ankachita zoipa kwambiri.
36
Adagwirizana naye pomanga zombo zomapita ku Tarisisi ndipo zombozo ankazimangira ku Eziyoni-Gebere.
37
Tsono Eliyezere mwana wa Dodavahu wa ku Maresa, adalosa zoipira Yehosafati adati, “Chifukwa chakuti mwagwirizana ndi Ahaziya, Chauta adzaononga zimene mwapangazo.” Ndipo zombozo zidaonongekadi zosakafika ku Tarisisi.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36