bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 12
2 Chronicles 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 13 →
1
Rehobowamu atangokhazikitsa ulamuliro wake ndi kuulimbitsa, iyeyo pamodzi ndi Aisraele onse adayamba kusiya malamulo a Chauta.
2
Chaka chachisanu cha ufumu wa Rehobowamu, Sisake mfumu ya ku Ejipito adathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu chifukwa chakuti Aisraele adaakhala osakhulupirika kwa Chauta.
3
Sisakeyo adabwera ndi magaleta ankhondo okwanira 1,200 ndi anthu okwera pa akavalo 60,000. Anthu ake anali osaŵerengeka amene adadza nawo kuchokera ku Ejipito, Libiya, Sukimu ndi Etiopiya.
4
Adalanda mizinda yamalinga ya ku Yuda, nakafika mpaka ku Yerusalemu.
5
Tsono mneneri Semaya adadza kwa Rehobowamu ndi kwa atsogoleri a ku Yuda, amene anali atasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisake, ndipo adaŵauza kuti, “Chauta akunena kuti, ‘Inu mwandisiya Ine, ndiye nanenso ndakusiyani ndi kukuperekani kwa Sisake.’ ”
6
Apo atsogoleri a Aisraele pamodzi ndi mfumu yomwe adadzichepetsa, nati, “Chauta ndi wolungama.”
7
Tsono Chauta ataona kuti anthuwo adzichepetsa, adauzanso Semaya kuti, “Anthuŵa adzichepetsa, sindidzaŵaononga ai, koma ndidzaŵapulumutsa. Sindidzaukwiyira mzinda wa Yerusalemu, motero Sisake sadzauwononga konse.
8
Komabe adzakhala akapolo a Sisakeyo, kuti anthuwo adziŵe kusiyanitsa pakati pa kutumikira Ine ndi kutumikira mafumu a maiko achilendo.”
9
Tsono Sisake, mfumu ya ku Ejipito, adabwera kudzathira Yerusalemu nkhondo. Adalanda chuma cha ku Nyumba ya Chauta pamodzi ndi chuma cha ku nyumba ya mfumu. Adatenga zonse, ngakhalenso zishango zomwe zagolide zimene Solomoni adaapanga.
10
Pambuyo pake mfumu Rehobowamu adapanga zishango zamkuŵa m'malo mwake, nazipereka kwa m'manja mwa akapitao a alonda amene ankalonda pakhomo pa nyumba ya mfumu.
11
Tsono nthaŵi zonse mfumu ikamaloŵa m'Nyumba ya Chauta, alondawo ankatenga zishango, kenaka nkumazibwezera ku chipinda cha alonda.
12
Tsono mfumuyo itadzichepetsa, Chauta adaleka kufuna kuŵaononga kwathunthu. Motero zinthu zinkayenda bwino ku Yuda.
13
Mfumu Rehobowamu adakhazikitsa ufumu wake ku Yerusalemu. Anali wa zaka 41 nthaŵi imene ankayamba kulamulira. Adalamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Chauta adausankha pakati pa mafuko onse a Israele kuti azimpembedza kumeneko. Mai wake anali Naama, Mwamoni.
14
Koma Rehobowamuyo adachita zoipa, popeza kuti mtima wake sudafunitsitse Chauta.
15
Tsono ntchito za Rehobowamu kuyambira poyamba mpaka pomaliza, paja zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Semaya ndiponso m'buku la mbiri ya mneneri Ido. Panali nkhondo zosakata pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu.
16
Rehobowamu adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide. Tsono Abiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36