bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 29
2 Chronicles 29
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 30 →
1
Hezekiya adamlonga ufumu ali wa zaka 25, ndipo adalamulira zaka 29 ku Yerusalemu. Mai wake anali Abiya, mwana wa Zekariya.
2
Adachita zolungama pamaso pa Chauta monga momwe ankachitira Davide kholo lake.
3
Pa chaka choyamba cha ufumu wake, pa mwezi woyamba, Hezekiya adatsekula zitseko za Nyumba ya Chauta, nazikonza.
4
Adaloŵa ndi ansembe ndi Alevi, naŵasonkhanitsa ku bwalo lakuvuma,
5
ndipo adaŵauza kuti, “Mverani inu Alevi. Mudziyeretse, muyeretsenso Nyumba ya Chauta Mulungu wa makolo anu, pakuchotsa zonyansa ku malo opatulika.
6
Makolo athu adakhala osakhulupirika ndipo adachita zoipa pamaso pa Chauta, Mulungu wathu. Iwo adasiya Chauta, adaloza nkhongo ku malo a Chauta, ndi kumfulatira.
7
Adatsekanso zitseko za khonde la poloŵera, nazima nyale. Sadafukize lubani kapena kupereka nsembe zopsereza ku malo opatulika kwa Mulungu wa Israele.
8
Nchifukwa chake Mulungu adaŵapsera mtima anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu. Adaŵasandutsa ochititsa anthu mantha, odabwitsa anthu ndiponso oti anthu aziŵatsonya monga m'mene mukuwoneramu.
9
Makolo athu adaphedwa ndi lupanga, ndipo ana athu aamuna, ana athu aakazi ndi akazi athu ali ku ukapolo chifukwa cha zimenezi.
10
Tsono ine ndikuganiza kuti ndichite chipangano ndi Chauta, Mulungu wa Israele, kuti mkwiyo wake woopsawo utichoke.
11
Ana anga, musachedwe, pakuti Chauta wakusankhani inu kuti muziima pamaso pake ndi kumamtumikira, ndipo kuti mukhale atumiki ake, ndi kumafukiza lubani kwa Iye.”
12
Tsono Alevi amene anali pomwepo ndi aŵa: a m'banja la Kohati: Mahati mwana wa Amasai, ndi Yowele mwana wa Azariya; a m'banja la Merari: Kisi mwana wa Abidi, ndi Azariya mwana wa Yehalelele; a m'banja la Geresoni: Yowa mwana wa Zima, ndi Edeni mwana wa Yowa;
13
a m'banja la Elizafani: Simiri ndi Yeuwele; a banja la Safu: Zekariya ndi Mataniya;
14
a m'banja la Hemani: Yehuwele ndi Simei; a m'banja la Yedutuni: Semaya ndi Uziyele.
15
Iwowo adasonkhanitsa abale ao, ndipo adadziyeretsa, naloŵa m'Nyumba ya Chauta kuti aiyeretse monga momwe mfumu idaalamulira, potsata mau a Chauta.
16
Ansembe ndiwo amene adaaloŵa m'katikati mwa Nyumba ya Mulungu kuti akayeretsemo. Adatulutsa zinthu zonse zonyansa zimene adazipeza m'Nyumbamo, m'bwalo la Nyumbayo. Alevi adazitenga zimenezo, nakazitaya ku mtsinje wa Kidroni.
17
Adayamba mwambo wa kuyeretsa pa tsiku loyamba la mwezi woyamba. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu la mweziwo, mpamene adafika m'khonde la poloŵera m'Nyumba ya Chauta. Tsono adachita mwambo wa kuyeretsa Nyumba ya Chauta ija pa masiku asanu ndi atatu, ndipo adaimaliza pa tsiku la 16 la mwezi woyambawo.
18
Atatha, adapita kwa mfumu Hezekiya nakamuuza kuti, “Tayeretsa Nyumba yonse ya Chauta ija, guwa la nsembe zopsereza, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndiponso tebulo la buledi wopereka pamaso pa Chauta, pamodzi ndi zipangizo zake zonse.
19
Zipangizo zonse zimene mfumu Ahazi adaazichotsa pamene anali mfumu yosakhulupirika, tazibwezera, ndipo taziyeretsa. Taziika ku guwa la Chauta.”
20
Pambuyo pake mfumu Hezekiya adanyamuka m'mamaŵa, nasonkhanitsa akuluakulu amumzindamo, ndipo adakwera ku Nyumba ya Chauta.
21
Adabwera ndi ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndiponso atonde asanu ndi aŵiri kuti aperekere nsembe yopepesera uchimo, kuperekera banja la mfumu, Nyumba ya Chauta ndi Yuda. Ndipo iyeyo adalamula ansembe, ana a Aaroni, kuti azipereke pa guwa la Chauta.
22
Choncho anthuwo adapha ng'ombe zamphongo zija ndipo ansembe adatenga magazi, nawaza pa guwa. Adaphanso nkhosa zamphongo zija, nawaza magazi ake pa guwa.
23
Tsono atonde operekera nsembe yopepesera uchimo aja, adabwera nawo kwa mfumu ndi kwa msonkhano wonse. Ndipo adasanjika manja ao pa atondewo.
24
Kenaka ansembe adazipha, napereka magazi ake pa guwa, kuti akhale mwambo wofafanizira machimo a Aisraele onse, pakuti mfumu idaalamula kuti nsembe yopsereza ndi nsembe zopepesera uchimo zichitike chifukwa cha Aisraele onse.
25
Tsono adaika Alevi kuti azikhala ku Nyumba ya Chauta ndi kumaimba ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe, potsata lamulo la Davide ndi la Gadi mneneri wa mfumu, ndiponso la Natani mneneri. Pakuti lamulo limenelo nlochokera kwa Chauta kudzera mwa aneneri ake.
26
Alevi adaimirira atatenga zipangizo zoimbira zonga za Davide, ndipo ansembe adatenga malipenga.
27
Pamenepo Hezekiya adalamula kuti nsembe yopsereza iperekedwe pa guwa. Atayamba kupereka nsembe yopsereza, adayambanso kuimbira nyimbo Chauta. Ndipo adaliza malipenga ndi zipangizo zoimbira za Davide mfumu ya Israele.
28
Msonkhano wonse udagwada moŵeramitsa mitu pansi, anthu oimba nyimbo akuimba, ndipo oliza malipenga akuliza. Adakhala akuchita zimenezi mpaka nsembe yopsereza idatha.
29
Atatha kupereka nsembe, mfumu pamodzi ndi anthu onse amene anali nawo adagwada naŵeramitsa mitu pansi.
30
Kenaka mfumu Hezekiya, pamodzi ndi nduna zake, adalamula Alevi kuti aimbe nyimbo zotamanda Chauta potsata mau a Davide ndi a mneneri Asafu. Pomwepo adaimba mosangalala nyimbo zotamanda, ndipo adagwada naŵeramitsa mitu pansi.
31
Pamenepo Hezekiya adati, “Tsopano inu mwadzipereka kuti mugwire ntchito ya Chauta. Idzani pafupi, mubwere nazo nsembe ndi zopereka zothokozera ku Nyumba ya Chauta.” Msonkhanowo udabwera nazo nsembe ndi zopereka zothokozera. Anthu onse amene anali ndi mtima waufulu adabwera ndi nsembe zopsereza.
32
Chiŵerengero cha nsembe zopsereza zimene msonkhano udabwera nazo ndi ichi: ng'ombe zamphongo 70, nkhosa zamphongo 100, ndi anaankhosa 200. Zonsezi adazipereka ngati nsembe yopsereza kwa Chauta.
33
Tsono nsembe zina zopereka zinali izi: ng'ombe zamphongo 600 ndi nkhosa 300.
34
Koma ansembe anali pang'ono, choncho sadathe kusenda nsembe zonse zopserezazo. Motero poyembekeza kuti ansembe onse adziyeretse, Alevi adaŵathandiza mpaka ntchito yonseyo idatha. Aleviwo adaachita changu kupambana ansembe pakudziyeretsa kwao.
35
Kuwonjezera pa chiŵerengero cha nsembe zopsereza, panalinso mafuta a nsembe zamtendere, ndiponso zakumwa za pa nsembe zopsereza. Motero miyambo yonse ya ku Nyumba ya Chauta idakhazikikanso.
36
Choncho Hezekiya ndi anthu onse aja adakondwa chifukwa cha zimene Mulungu adaŵachitira, pakuti zimenezo zidaachitika mwadzidzidzi.
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 30 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36