bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 36
2 Chronicles 36
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
1
Anthu am'dzikomo adatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya, namlonga ufumu m'malo mwa atate ake ku Yerusalemu.
2
Yehowahazi anali wa zaka 23 pamene ankaloŵa ufumu. Ndipo adalamulira miyezi itatu ku Yerusalemu.
3
Pambuyo pake mfumu ya ku Ejipito idamchotsa Yehowahaziyo ku Yerusalemu, ndipo idakhometsa dziko msonkho wokwanira makilogramu 3,400 a siliva ndi 34 a golide.
4
Tsono mfumu ya ku Ejipito idakhazika Eliyakimu, mbale wake wa Yehowahazi, kuti akhale mfumu yolamulira ku Yuda ndi ku Yerusalemu. Ndipo adasintha dzina lake kuti akhale Yehoyakimu. Koma Yehowahazi uja Neko adamtenga kupita naye ku Ejipito.
5
Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu. Iyeyo ankachita zoipa pamaso pa Chauta, Mulungu wake.
6
Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adabwera kudzamenyana naye nkhondo. Adammanga maunyolo kunka naye ku Babiloni.
7
Nebukadinezara adatenganso ziŵiya za ku Nyumba ya Mulungu kunka nazo ku Babiloni. Ndipo adakaziika ku nyumba yake yaufumu ku Babiloniko.
8
Tsono ntchito zina zonse za Yehoyakimu ndi zoipa zimene ankachita zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Israele ndi a ku Yuda. Ndipo Yehoyakini mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
9
Yehoyakini anali wa zaka 18 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira miyezi itatu ndi masiku khumi ku Yerusalemu. Iyeyo ankachita zoipa pamaso pa Chauta.
10
Pomatha chaka, mfumu Nebukadinezara adatuma anthu kukamtenga, ndipo adabwera naye ku Babiloni, pamodzi ndi ziŵiya zamtengowapatali za ku Nyumba ya Chauta. Tsono adakhazika Zedekiya mbale wake kuti akhale mfumu ya ku Yuda ndi Yerusalemu.
11
Zedekiya anali wa zaka 21 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu.
12
Ankachita zoipa pamaso pa Chauta, Mulungu wake. Iyeyo sadadzichepetse pamaso pa mneneri Yeremiya, amene ankalankhula mau ochoka m'kamwa mwa Chauta.
13
Adapandukiranso mfumu Nebukadinezara amene anali atamlumbiritsa kwa Mulungu kuti adzamumvera. Koma Zedekiyayo adangoti nkhongo gwa, nkuumitsanso mtima wake, kuti asabwerere kwa Chauta, Mulungu wa Israele.
14
Atsogoleri onse a ansembe, pamodzi ndi anthu omwe, adachita zosakhulupirika zambirimbiri potsata zoipa za mitundu ina ya anthu. Adaipitsa Nyumba ya Chauta imene Chautayo anali ataipatula kuti ikhale yake ku Yerusalemu.
15
Chauta, Mulungu wa makolo ao, ankaŵatumira amithenga kaŵirikaŵiri, chifukwa chakuti ankaŵamvera chifundo anthu ake ndi malo ake amene Iye ankakhala.
16
Koma anthuwo ankapeputsabe amithengawo, namanyoza mau a Mulungu. Ndipo ankaŵaseka aneneri ake, mpaka Chauta adakwiyira anthu ake, ndipo panalibenso mankhwala ochiritsa.
17
Nchifukwa chake adaŵautsira mfumu ya Ababiloni. Iwowo adapha anyamata ao ndi lupanga ku Nyumba ya Chauta wao. Ndipo sadachitire chifundo anyamata kapena anamwali, ndoda kapena nkhalamba. Chauta adaŵapereka onsewo kwa mfumu ya Ababiloni.
18
Adaperekanso ziŵiya zonse za ku Nyumba ya Chauta, zazikulu nzazing'ono zomwe, pamodzi ndi chuma chonse cha ku Nyumba ya Mulungu ndiponso chuma cha ku nyumba ya mfumu, pamodzi ndi chuma cha nduna zake. Zonsezo adapita nazo ku Babiloni.
19
Kenaka adatentha Nyumba ya Chauta, nagwetsa linga lonse la Yerusalemu. Adatenthanso nyumba zonse zaufumu, naononga ziŵiya zonse zamtengowapatali.
20
Anthu amene adapulumuka ku lupanga, adaŵatenga ukapolo kupita nawo ku Babiloni. Kumeneko adasanduka anthu oitumikira mfumuyo ndi ana ake, mpaka ufumu wa Persiya utakhazikitsidwa,
21
kuti zipherezere zimene Chauta adaalankhula kudzera mwa Yeremiya, zakuti, “Dzikoli lidzakhala lopasuka kwa zaka 70, kuti masabata opuma amene sanachitike, akwaniritsidwe.”
22
Tsono chaka choyamba cha ufumu wa Kirusi, mfumu ya ku Persiya, Chauta adautsa mtima wa Kirusiyo, kuti alengeze ku maiko onse a ufumu wake mpaka kulemba kumene. Adachita choncho kuti zimene Chauta adaalankhula kudzera mwa Yeremiya zipherezere. Adati,
23
“Kirusi, mfumu ya ku Persiya, akunena kuti, ‘Chauta, Mulungu wakumwamba, wandipatsa ine maufumu onse pa dziko lapansi. Ndipo wandilamula kuti ndimmangire Nyumba ku Yerusalemu, ku Yuda. Aliyense mwa inu nonse amene ali munthu wa Chauta, Chauta Mulungu wakeyo akhale naye. Ndipo apite.’ ”
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36