bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 16
2 Chronicles 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 17 →
1
Pa chaka cha 36 cha ufumu wa Asa, Baasa mfumu ya ku Israele, adapita kukathira nkhondo dziko la Yuda. Adamangira linga mzinda wa Rama kuti aziletsa anthu kuloŵa kapena kutuluka m'dziko la Asa, mfumu ya ku Yuda.
2
Tsono Asa adatenga siliva ndi golide ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndiponso ku nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, amene ankakhala ku Damasiko. Mau a Asa anali akuti,
3
“Tiye tigwirizane ine ndi iwe, monga m'mene ankachitira bambo wanga ndi bambo wako. Ona ndikukutumizira mphatso za siliva ndi golide. Pita ukaphwanye chigwirizano chako ndi Baasa, mfumu ya ku Israele, kuti asadzanditherenso nkhondo.”
4
Benihadadi adamvera zimene adanena mfumu Asa zija, motero adatuma atsogoleri a magulu ake ankhondo kukathira nkhondo mizinda ya ku Israele. Adagonjetsa Iyoni, Dani, Abele-Maimu ndi mizinda yonse ya ku Nafutali yosungiramo zinthu.
5
Tsono Baasa atazimva zimenezi, adaleka kumangira Rama linga ndipo ntchito yonseyo adaisiya.
6
Apo mfumu Asa adabwera ndi Ayuda onse, ndipo adadzanyamula miyala ndi mitengo imene Baasa ankamangira linga la Rama. Zimenezi Asa adamangira linga la Geba ndi la Mizipa.
7
Nthaŵi imeneyo mneneri Hanani adadza kwa Asa mfumu ya ku Yuda, namuuza kuti, “Chifukwa chakuti mudakhulupirira mfumu ya ku Siriya, osakhulupirira Chauta, Mulungu wanu, gulu lankhondo la mfumu ya ku Siriya lakuthaŵirani.
8
Kodi Aetiopiya ndi Alibiya sanali gulu lalikulu lankhondo, lokhala ndi magaleta ochuluka ndiponso anthu ambirimbiri okwera pa akavalo? Komabe chifukwa chodalira Chauta, Chautayo adaŵapereka kwa inu.
9
Paja maso a Chauta amayang'ana uku ndi uku pa dziko lonse lapansi, kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wao uli wangwiro kwa Iyeyo. Inuyo mwachita zopusa pa zimenezi. Ndiye kuyambira tsopano lino, mpaka m'tsogolo muno, mudzakhala pa nkhondo.”
10
Apo Asa adapsera mtima mneneriyo, ndipo adammanga namuika m'ndende, popeza kuti adaakwiya naye kwambiri chifukwa cha zimenezi. Kenaka Asayo adayamba kuchita zankhalwe pa anthu enanso nthaŵi yomweyo.
11
Tsono ntchito za Asa, kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, zidalembedwa m'buku la Mafumu a ku Yuda ndi a ku Israele.
12
Pa chaka cha 39 cha ufumu wake, Asa adayamba kudwala nthenda ya mapazi, ndipo nthendayo idakula kwambiri. Komabe ngakhale ankadwala choncho, sadapemphe chithandizo kwa Chauta, koma kwa asing'anga.
13
Tsono adamwalira, pa chaka cha 41 cha ufumu wake.
14
Adamuika m'manda amene iyeyo adaadzisemera mu mzinda wa Davide. Adagoneka mtembo wake pa chithatha chimene adaikapo zonunkhira zamitundumitundu zimene anthu opanga zonunkhira adazikonza. Ndipo adasonkha chimoto chachikulu kwambiri chomchitira ulemu.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36