bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 14
2 Chronicles 14
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 15 →
1
Tsono Abiya adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide. Pambuyo pake Asa mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Pa masiku a Asa, dziko lidakhala pa mtendere zaka khumi.
2
Asa adachita zokoma ndi zolungama pamaso pa Chauta, Mulungu wake.
3
Adagwetsa maguwa achilendo, nkuwononga akachisi ku zitunda, nagumula zipilala zamiyala zachipembedzo, nkugwetsa mafano a Asera.
4
Ndipo adalamula anthu a ku Yuda kuti azitembenukira kwa Chauta, Mulungu wa makolo ao, ndi kumamvera malangizo ndi malamulo ake.
5
M'mizinda yonse ya ku Yuda adaononga akachisi opembedzeramo mafano nagumula maguwa ofukizirapo lubani. Ndipo dzikolo lidakhala pa mtendere nthaŵi imene Asa ankalamulira.
6
Adamanga mizinda yamalinga ku Yuda, chifukwa dzikolo linali pa mtendere. Sadamenye nkhondo masiku amenewo, popeza kuti Chauta adampatsa mtendere.
7
Adauza anthu a ku Yuda kuti, “Tiyeni timange mizinda imeneyi, ndipo timange makoma ndi nsanja, zitseko ndi mipiringidzo yake. Dzikoli lidakali lathu, chifukwa chakuti tachita kufuna kwa Chauta, Mulungu wathu. Tachita kufuna kwake, ndipo Iye watipatsa mtendere pa mbali iliyonse.” Choncho adamangadi zimenezo, ndipo adapeza bwino ndithu.
8
Tsono Asa anali nalo gulu lankhondo la anthu 300,000 a ku Yuda. Iwoŵa anali ndi zishango ndi mikondo. Anthu a ku Benjamini analipo 280,000. Iwowo anali ndi zishango ndi mauta. Anthu onsewo anali amphamvu ndi olimba mtima.
9
Zera wa ku Etiopiya adanyamuka kukamenyana ndi Ayuda atatenga gulu lake lankhondo la anthu 1,000,000, ndi magaleta 300, ndipo adakafika mpaka ku Maresa.
10
Tsono Asa adanyamuka kuti akakomane naye, ndipo onsewo adandanditsa magulu ao ankhondo ku chigwa cha Zefati ku Maresa.
11
Pamenepo Asa adafuula kwa Chauta, Mulungu wake, kuti, “Inu Chauta, palibe wina wofanafana nanu woti angathandize pakati pa anthu amphamvu ndi ofooka. Tithandizeni, Inu Chauta, Mulungu wathu, popeza kuti timakhulupirira Inu, ndipo tabwera kudzamenyana ndi chinamtindi cha anthu chimenechi m'dzina lanu. Inu Chauta, ndinu Mulungu wathu. Munthu asakupambaneni ai.”
12
Motero Chauta adagonjetsa anthu a ku Etiopiya pamaso pa Asa ndi pa anthu a ku Yuda, ndipo anthu a ku Etiopiyawo adathaŵa.
13
Asa pamodzi ndi anthu ake aja adaŵathamangitsa mpaka ku Gerari, ndipo anthu a ku Etiopiyawo adaphedwa onse, osatsalapo ndi mmodzi yemwe wamoyo. Zidatero chifukwa anali ndi mantha aakulu pamaso pa Chauta ndi gulu lake lankhondo. Ndipo Ayuda adatenga zofunkha zambirimbiri.
14
Tsono adakantha mizinda yonse yozungulira Gerari pakuti anthu ake adaagwidwa ndi mantha oopa Chauta. Adalanda katundu m'mizinda yonse, poti munali chuma chambiri m'mizindamo.
15
Ndipo adagwetsa makola a ziŵeto, ndi kutenga nkhosa zochuluka, pamodzi ndi ngamira. Kenaka adabwerera ku Yerusalemu.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36