bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 11
2 Chronicles 11
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 12 →
1
Rehobowamu atafika ku Yerusalemu, adasonkhanitsa ankhondo osankhidwa okwanira 180,000, afuko la Yuda ndi la Benjamini, ndi cholinga akamenyane nkhondo ndi anthu a ku Israele, kuti choncho ambwezere Rehobowamu ufumu wake.
2
Koma Chauta adadza kwa Semaya, m'meneri wake, namlamula kuti,
3
“Ukauze Rehobowamu, mwana wa Solomoni, mfumu ya ku Yuda, ndi Aisraele onse a ku Yuda ndi a ku Benjamini kuti,
4
‘Ine Chauta ndikuti, Musapite kukamenyana ndi abale anu. Aliyense abwerere kwao, poti zimene zachitikazi zachokera kwa Ine.’ ” Anthuwo adamvera mau a Chauta, nadabwerera osapita kukamenyana ndi Yerobowamu.
5
Rehobowamu ankakhala ku Yerusalemu, ndipo adamanga mizinda yamalinga ku Yuda.
6
Adamanga Betelehemu, Etamu, Tekowa,
7
Betezuri, Soko, Adulamu,
8
Gati, Maresa, Zifi,
9
Adoraimu, Lakisi, Azeka,
10
Zora, Aiyaloni ndi Hebroni. Mizinda yamalinga yonseyo inali ku Yuda ndi ku Benjamini.
11
Malinga ake adamanga olimba, ndipo adaikamo atsogoleri a nkhondo. Adaikamonso chakudya, mafuta ndi vinyo.
12
Adaikamo zishango ndi mikondo, ndipo adaitchinjiriza kwambiri mizindayo. Choncho ankalamulira anthu a ku Yuda ndi a ku Benjamini.
13
Ansembe pamodzi ndi Alevi amene anali m'dziko lonse la Israele adatsata Rehobowamu, kuchoka konse kumene ankakhala.
14
Alevi adasiya mabusa ao ndi maiko ao, ndipo adapita ku Yuda ndi ku Yerusalemu, chifukwa chakuti Yerobowamu ndi ana ake anali ataŵachotsa pa ntchito zao zaunsembe zomatumikira Chauta.
15
Yerobowamu adaadzisankhira ansembe ake, kuti azitumikira ku kachisi ku zitunda, kupembedza mizimu yoipa ndi mafano a atonde ndi a anaang'ombe amene adaŵapanga.
16
Tsono anthu amene adatsimikiza mumtima mwao kuti azitumikira Chauta, Mulungu wa Israele, ankatsatira ansembe ndi Alevi aja, kuchoka ku mafuko a ku Israele, kupita ku Yerusalemu kukapereka nsembe kwa Chauta, Mulungu wa makolo ao.
17
Iwowo adalimbitsa ufumu wa Yuda, ndipo adamsunga Rehobowamu mwana wa Solomoni zaka zitatu, chifukwa chakuti pa zaka zitatuzo ankatsata chitsanzo cha Davide ndi cha Solomoni.
18
Rehobowamu adakwatira Mahalati, amene bambo wake anali Yerimoti, mwana wa Davide, ndipo mai wake anali Abihaili mwana wa Eliyabu mwana wa Yese.
19
Mkaziyo adambalira ana aŵa: Yeusi, Semariya ndi Zahamu.
20
Adakwatiranso Maaka mwana wa Abisalomu, ndipo adambalira Abiya, Atai, Ziza ndi Selomiti.
21
Rehobowamu ankakonda Maaka mwana wa Abisalomu kupambana akazi ake onse, kupambananso azikazi ake. (Adakwatira akazi 18, ndipo anali ndi azikazi okwanira 60, ndipo anali ndi ana aamuna 28, ana aakazi 60.)
22
Rehobowamu adasankha Abiya, mwana wa Maaka, kuti akhale mtsogoleri pakati pa abale ake, poti ankafuna kuti amlonge ufumu iyeyo.
23
Tsono mwanzeru adaika ena mwa ana ake aamuna m'zigawo zonse za ku Yuda ndi za ku Benjamini, ku mizinda yonse yamalinga. Ankaŵapatsa chakudya chambiri ndi kuŵafunira akazi ochuluka.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36