bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 28
2 Chronicles 28
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 29 →
1
Ahazi anali wa zaka 20 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Iyeyo sadachite zolungama pamaso pa Chauta, monga m'mene ankachitira Davide kholo lake.
2
Koma adatsata zitsanzo za mafumu a ku Israele. Adapanga zifanizo zosungunula za Abaala.
3
Adafukiza lubani ku chigwa cha mwana wa Hinomu, ndipo adapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza, potsata miyambo yonyansa ya anthu a mitundu ina imene Chauta adaaipirikitsa m'dzikomo pamene ankafika Aisraele.
4
Ndipo adapereka nsembe, namafukiza lubani ku akachisi opembedzerako mafano, pa mapiri ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira.
5
Nchifukwa chake Chauta, Mulungu wake, adapereka Ahazi kwa mfumu ya ku Siriya, imene idamgonjetsa. Ndipo anthu ambiri adatengedwa ukapolo kupita ku Damasiko. Chauta adamperekanso Ahaziyo kwa mfumu ya ku Israele, imene idamgonjetsa kotheratu pakupha anthu ambiri.
6
Peka mwana wa Remaliya adaphako anthu okwanira 120,000 a ku Yuda pa tsiku limodzi, chifukwa iwowo adaasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao. Onsewo anali anthu olimba mtima.
7
Ndipo Zikiri, munthu wamphamvu wa ku Efuremu, adapha Maaseiya mwana wa mfumu, ndi Azirikamu, nduna ya ku nyumba ya mfumu, ndiponso Elikana, wachiŵiri mu ulamuliro wa mfumu.
8
Anthu a ku Israele adagwira ukapolo abale ao a ku Yuda okwanira 200,000, akazi, ana aamuna, ndi ana aakazi. A ku Israelewo adatenganso zofunkha zambiri kubwera nazo ku Samariya.
9
Koma kumeneko kunali mneneri wina wa Chauta dzina lake Odedi. Iye adapita kuti akakumane ndi gulu lankhondo limene lidadza ku Samariya. Adauza anthuwo kuti, “Popeza kuti Chauta, Mulungu wa makolo anu, adaakwiyira anthu a ku Yuda, adapereka Ayudawo kwa inu. Koma inu mwaŵapha mwaukali, ukali wake wofika mpaka kumwamba.
10
Tsono mukufuna kuti mupondereze anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu, amuna ndi akazi omwe, kuti akhale akapolo anu. Kodi inuyo mulibe anu machimo pamaso pa Chauta, Mulungu wanu?
11
Mverani tsono, ndipo muŵabweze akapolo amene mudaŵatenga pakati pa abale anuwo, kuti apite kwao, poti Chauta wakwiya nanu koopsa.”
12
Atsogoleri enanso a anthu a ku Efuremu, monga Azariya mwana wa Yohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilai, adaimirira kuti amenyane ndi anthu amene ankachoka ku nkhondo.
13
Adaŵauza kuti, “Musati mubwere nawo kuno akapolowo, poti inuyo mukufuna kuti ife tichimwire Chauta kuwonjezera pa machimo athu amene tili nawo, ndiponso kuwonjezera pa zolakwa zathu. Ndithu kulakwa kwathu nkwakukulu ndipo mkwiyo woopsa uli pa Israele.”
14
Motero anthu ankhondo aja adaŵasiya akapolowo, pamodzi ndi zofunkhazo, pamaso pa atsogoleriwo ndi pamaso pa msonkhano wonse.
15
Kenaka anthu amene taŵatchula maina aja, adanyamuka natenga akapolowo. Amene anali maliseche adaŵaveka zovala zimene adaafunkha. Adaŵaveka, naŵapatsa nsapato. Adaŵapatsa zakudya ndi zakumwa. Tsono atanyamula anthu onse ofooka pa abulu, adabwera nawo kwa abale ao ku Yeriko, mzinda wamigwalangwa. Kenaka adabwerera ku Samariya.
16
Pa nthaŵi imeneyo Mfumu Ahazi adatumiza mau kwa mfumu ya ku Asiriya, kupempha chithandizo.
17
Paja Aedomu anali atathiranso nkhondo ku Yuda, ndipo adaagonjetsa Yudayo, natenga anthu kuti akhale akapolo.
18
Afilisti nawonso anali atathira nkhondo mizinda yakuchigwa ndiponso Megebu wa ku Yuda. Ndipo adalanda Betesemesi, Aiyaloni, Gederoti ndiponso Soko pamodzi ndi midzi yake yomwe, Timna pamodzi ndi midzi yake yomwe, ndi Gimizo pamodzi ndi midzi yake yomwe, nakhazikika komweko.
19
Zoonadi Chauta adalitsitsa dziko la Yuda chifukwa cha mfumu Ahazi, popeza kuti adaaipitsa ku Yuda, ndipo anali wosakhulupirika kwa Chauta.
20
Motero Tiligati-Pilinesere, mfumu ya ku Asiriya, adadzamenyana naye nkhondo, ndipo adamvutitsa m'malo momlimbikitsa.
21
Ahazi ankatenga katundu ku Nyumba ya Chauta, ku nyumba ya mfumu ndi ku nyumba za nduna, namakampereka kuti akakhomere msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya. Koma zonsezo sizidamthandize.
22
Pa nthaŵi yake yamavutoyo, Ahazi adapitirirabe kukhala wosakhulupirika kwa Chauta.
23
Ankapereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko imene idamgonjetsayo, ndipo ankati, “Chifukwa chakuti milungu ya mafumu a ku Siriya yaŵathandiza iwowo, ine ndidzapereka nsembe kwa milunguyo kuti indithandizenso ine.” Koma milunguyo idamuwononga pamodzi ndi anthu ake onse.
24
Tsono Ahazi adasonkhanitsa ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta, naziphwanyaphwanya. Kenaka adatseka zitseko za Nyumba ya Mulungu, nadzimangira maguwa pa malo ambirimbiri mu Yerusalemu.
25
Adamanga akachisi opembedzerako ku mzinda uliwonse wa Yuda, kuti azifukizako lubani kwa milungu ina, kuputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa makolo ake.
26
Tsono ntchito zonse ndi makhalidwe ake kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Yuda ndi mafumu a ku Israele.
27
Ahazi adamwalira, naikidwa mu mzinda wa Yerusalemu, koma sadamuike m'manda enieni a mafumu. Ndipo Hezekiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 29 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36