bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 2
2 Chronicles 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 3 →
1
Tsono Solomoni adatsimikiza zoti amange nyumba yopembedzeramo Chauta ndiponso nyumba yaufumu ya iye mwini.
2
Tsono adalemba anthu 70,000 osenza katundu, anthu 80,000 okakumba miyala ku dziko lamapiri, ndiponso akapitao 3,600, oyang'anira anthuwo.
3
Adatumiza mau kwa Hiramu mfumu ya ku Tiro, adati, “Monga momwe munkachitira ndi Davide bambo wanga, pomamtumizira mitengo ya mkungudza, kuti amangire nyumba yake yoti azikhalamo, muchitenso momwemo ndi ine.
4
Ineyo ndikufuna kuti ndimangire nyumba Chauta, Mulungu wanga, ndipo kuti ndiipereke kwa Iye, kuti ikhale yoperekeramo zofukiza za fungo lonunkhira bwino pamaso pa Mulungu, ndi yoperekeramo kosalekeza buledi wopatulika. M'nyumbamo aziperekeramonso nsembe zopsereza m'maŵa ndi madzulo, pa masiku a sabata, pa masiku okhala mwezi ndi pa masiku achikondwerero a Chauta, Mulungu wathu, potsata malamulo okhalira Aisraele mpaka muyaya.
5
Nyumba imene ndimangeyo idzakhala yaikulu, pakuti Mulungu wathu ndi wamkulu kupambana milungu yonse.
6
Koma ndani angathe kummangira nyumba, poti ku mlengalenga ngakhale kumwambamwamba sikungathe kumkwanira Iye? Kodi ine ndinenso yani kuti ndingammangire nyumba, osati kamalo chabe koti nkumafukizapo lubani pamaso pa Mulungu?
7
Tsono tumizireni munthu waluso pa ntchito za golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, nsalu yofiirira, yofiira ndi yobiriŵira, ndiponso wodziŵa kuzokota. Akhale pamodzi ndi anthu aluso amene ali ndi ine ku Yuda ndi ku Yerusalemu amene Davide bambo wanga adandipatsa.
8
Munditumizirenso mitengo ya mkungudza, mitengo ya mlombwa ndiponso matabwa ambaŵa a ku Lebanoni, poti ndikudziŵa kuti anyamata anu amadziŵa kudula mitengo ku Lebanoni. Ndipo anyamata anga adzakhala pamodzi ndi anyamata anu,
9
kuti andidulire mitengo yochuluka, popeza kuti nyumba imene ndimangeyo idzakhala yaikulu ndi yochititsa kaso.
10
Anyamata anu odzadula mitengowo ndidzaŵapatsa tirigu wopunthapuntha wokwanira matani 2,000, barele wokwanira matani 2,000, vinyo wa malitara 440,000, ndiponso mafuta a malitara 440,000.”
11
Tsono Hiramu, mfumu ya ku Tiro, adayankha Solomoni pomulembera kalata yonena kuti, “Chifukwa chakuti Chauta amakonda anthu ake, wakuika iweyo kuti ukhale mfumu yao.”
12
Adatinso, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, amene adapatsa mfumu Davide mwana wanzeru, waluntha, ndi womvetsa zinthu bwino, woti amange nyumba ya Chauta ndiponso nyumba yaufumu ya iye mwini wake.
13
“Ndatuma mmisiri wanzeru, womvetsa, dzina lake Huramuabi,
14
amene mai wake ndi wa ku Dani, ndipo bambo wake anali wa ku Tiro. Iyeyo ndi wodziŵa bwino ntchito za golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, miyala, ndi matabwa, ndiponso nsalu yofiirira, yofiira ndi yobiriŵira, ndiponso bafuta wosalala. Angathe kuchitanso ntchito zonse zozokota, ndi ntchito ina iliyonse imene mungampatse kuti achite pamodzi ndi anthu anu aluso, anthu aluso a mbuyanga Davide bambo wanu.
15
Nchifukwa chake tsono, tirigu, barele, mafuta ndi vinyo zimene mbuyanga wanena, azitumize kwa anyamata antchitowo.
16
Tsono ife tidzadula mtengo uliwonse wa ku Lebanoni umene mungaufune, ndipo tidzakutumizirani mitengoyo poimanga pamodzi ndi kuiyandamitsa pa nyanja mpaka ku Yopa, kuti inuyo muitenge ndi kupita nayo ku Yerusalemu.”
17
Choncho Solomoni adaŵerenga alendo onse amene anali m'dziko lonse la Israele, monga momwe bambo wake Davide adaaŵaŵerengera kale. Ndipo padapezeka anthu okwanira 153,600.
18
Adapatula anthu 70,000 kuti akhale amtengatenga, ndipo anthu 80,000 kuti akhale okumba miyala ku mapiri. Tsono anthu 3,600 adaŵaika kuti akhale akapitao ogwiritsa anthu ntchito.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36