bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 21
2 Chronicles 21
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 22 →
1
Yehosafati adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide. Tsono Yehoramu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
2
Abale ake, ana a Yehosafati, anali aŵa: Azariya, Yehiyele, Zekariya, Azariyahu, Mikaele ndi Sefatiya. Onseŵa anali ana a Yehosafati, mfumu ya ku Yuda.
3
Atate ao adaaŵapatsa mphatso zambiri za siliva, golide, ndi zinthu zamtengowapatali, pamodzi ndi mizinda yamalinga ya ku Yuda. Koma ufumu adapatsa Yehoramu, chifukwa chakuti anali mwana wachisamba.
4
Yehoramu ataloŵa ufumu, nakhazikika pa mpando waufumu wa atate akewo, adapha abale ake onse ndi lupanga, ngakhalenso atsogoleri ena a ku Israele.
5
Yehoramu anali wa zaka 32 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu.
6
Ankatsata makhalidwe a mafumu a ku Israele, monga m'mene linkachitira banja la Ahabu, pakuti adaakwatira mwana wa Ahabu. Tsono ankachita zoipa zilizonse pamaso pa Chauta.
7
Komabe Chauta sadafune kuononga banja la Davide, chifukwa cha chipangano chimene adaachita ndi Davide, ndiponso poti adaalonjeza kuti adzampatsa nyale Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.
8
Pa nthaŵi yakeyo anthu a ku Edomu adaukira ulamuliro wa Yuda, ndipo adadzisankhira mfumu yao.
9
Tsono Yehoramu adapita pamodzi ndi atsogoleri ake ankhondo ndi magaleta ake onse. Adanyamuka usiku nakaŵakantha Aedomu amene adaamzinga iyeyo pamodzi ndi atsogoleri a magaleta ake.
10
Choncho Aedomu ngoukira ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Pa nthaŵi imeneyo, mzinda wa Libina nawonso udaukira ulamuliro wa Yehoramuyo, chifukwa chakuti adaasiya Chauta, Mulungu wa makolo ake.
11
Kubzolera pamenepo adayambitsa akachisi opembedzerako mafano ku dziko lamapiri la ku Yuda, ndipo adatsogolera anthu a ku Yerusalemu kuti akhale osakhulupirika, nasokeza anthu a ku Yuda.
12
Tsono adalandira kalata kwa mneneri Eliya, yonena kuti, “Chauta, Mulungu wa Davide, kholo lanu, akunena kuti, ‘Sudatsate chitsanzo cha Yehosafati bambo wako, kapenanso cha Asa, mfumu ya ku Yuda,
13
koma watsata chitsanzo cha mafumu aku Israele. Watsogolera anthu a ku Yuda pamodzi ndi anthu a mu Yerusalemu kuti akhale osakhulupirika, monga m'mene linkachitira banja la Ahabu pochimwitsa anthu a ku Israele. Wapha abale ako a pa banja la atate ako, amene anali abwino kupambana iwe.
14
Chifukwa cha zonsezi Chauta adzaŵagwetsera mliri anthu ako, ana ako, akazi ako, ndi zinthu zako zonse.
15
Ndipo iweyo udzadwala nthenda yoopsa ya m'mimba imene izidzakulirakulira tsiku ndi tsiku mpaka matumbo ako adzasololoka.’ ”
16
Tsono Chauta adamuutsira Yehoramuyo mkwiyo wa Afilisti ndi mkwiyo wa Arabu amene ali pafupi ndi Aetiopiya.
17
Motero iwowo adadzalimbana ndi anthu a ku Yuda naŵathira nkhondo. Ndipo adalanda zinthu zonse zimene adazipeza ku nyumba ya mfumu, pamodzinso ndi ana ake aamuna ndi akazi ake, kotero kuti panalibe mwana ndi mmodzi yemwe wamwamuna amene adatsala, kupatula Ahaziya mzime wake.
18
Pambuyo pake Chauta adamkantha ndi nthenda ya m'mimba yosachizika.
19
Patapita nthaŵi ndithu, pomatha chaka chachiŵiri, matumbo ake adayamba kusololoka chifukwa cha nthendayo, ndipo adafa imfa yopweteka kwambiri. Anthu sadasonkhe moto kuti amchitire ulemu monga m'mene ankachitira ndi makolo ake.
20
Iyeyo anali wa zaka 32 pamene ankayamba ufumu wake, ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu. Adafa popanda munthu womumvera chisoni. Adamuika mu mzinda wa Davide, koma osati m'manda a mafumu.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36