bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 3
2 Chronicles 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 4 →
1
Tsono Solomoni adayambapo kumanga Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu pa phiri la Moriya, pamene Chauta adaaonekera Davide bambo wake, pa malo omwe Davide adaaloza, pa bwalo lopunthira tirigu la Orinani Myebusi.
2
Solomoniyo adayamba kumanga pa mwezi wachiŵiri wa chaka chachinai cha ufumu wake.
3
Nyumba ya Chautayo, miyeso yake imene Solomoni adaapereka inali iyi: Potsata miyeso yakale, m'litali mwake inali ya mamita 27, ndipo m'mimba mwake inali ya mamita asanu ndi anai.
4
Chipinda chapoloŵera, m'litali mwake chinali cha mamita asanu ndi anai, kulingana ndi m'mimba mwake mwa nyumbayo. Msinkhu wake unali wa mamita 54. Nyumbayo m'kati mwake adaikuta ndi golide weniweni.
5
Chipinda chachikulucho adachichinga ndi matabwa amlombwa, nachikuta ndi golide wosalala, ndipo pamakoma adalochapo zithunzi za kanjedza ndi za maunyolo.
6
Adaikometsa nyumbayo ndi miyala yamtengowapatali. Golide wake anali wa ku Paravaimu.
7
Motero adaikuta nyumba yonseyo ndi golide, ndiye kuti mitanda yake, ziwundo zake, makoma ake ndi zitseko zake zomwe. Ndipo adazokota zithunzi za akerubi pa makoma.
8
Kenaka adapanga malo opatulika kwambiri. M'litali mwake anali a mamita asanu ndi anai, kulingana ndi m'mimba mwa nyumbayo. M'mimba mwake analinso a mamita asanu ndi anai. Adakuta malo opatulikawo ndi golide wosalala wokwanira matani makumi aŵiri.
9
Magaramu 570 a golide adaŵagwiritsa ntchito kupanga misomali. Ndipo zipinda zapamwamba adazikutanso ndi golide.
10
Ku malo opatulika kwambiriko adapangako akerubi aŵiri achitsulo, ndipo adaŵakuta ndi golide.
11
Mapiko a akerubiwo akaŵatambasula, pamodzi ankakwanira mamita asanu ndi anai. Phiko limodzi la kerubi mmodzi, la mamita aŵiri nkanthu, linkakhudza ku khoma la nyumba. Phiko lake lina, nalonso la mamita aŵiri nkanthu, linkakhudzana ndi phiko la kerubi mnzake.
12
Ndipo Kerubi ameneyu phiko lake limodzi, la mamita aŵiri nkanthu, linkakhudza ku khoma la nyumba, phiko lake lina, nalonso la mamita aŵiri nkanthu, lidalumikizana ndi phiko la kerubi woyamba uja.
13
Mapiko a akerubi amenewo onse pamodzi akaŵatambasula ankakwanira mamita asanu ndi anai. Akerubiwo adaaimirira pa mapazi ao, kuyang'ana m'kati mwa nyumbayo.
14
Ndipo Solomoni adatenga nsalu yobiriŵira, ina yofiira, ina yofiirira, ndi bafuta wosalala, napangira nsalu yochingira, kenaka adapetapo zithunzi za akerubi.
15
Kumaso kwake kwa nyumbayo adamangako nsanamira ziŵiri za msinkhu wa mamita 15 ndi theka. Nsanamira iliyonse inali ndi mutu wa mamita aŵiri nkanthu pamwamba pake.
16
Adapanga maunyolo okometsera, ofanafana ndi aja a m'kati mwa Nyumba ya Chauta, naŵaika pamwamba pa nsanamirazo. Adapanganso zinthu zonga makangaza zokwanira 100, ndipo adaziika ku maunyolowo.
17
Adamanga nsanamirazo kumaso kwa Nyumba ya Chauta, ina chakumwera, ina chakumpoto. Yakumwerayo adaitchula kuti Yakini, yakumpotoyo Bowazi.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36