bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 5
2 Chronicles 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 6 →
1
Motero Solomoni adatsiriza ntchito zonse za ku Nyumba ya Mulungu. Tsono adabwera ndi zinthu zonse zimene Davide bambo wake adaazipereka, ndipo adaika siliva, golide ndi ziŵiya zonse m'zipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Chauta.
2
Pambuyo pake Solomoni adasonkhanitsa akuluakulu onse a Aisraele, atsogoleri onse a mafuko ndi akuluakulu a mabanja a Aisraele. Onsewo adasonkhana ku Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta, kulichotsa ku Ziyoni, mzinda wa Davide.
3
Aisraele onse adasonkhana pamaso pa mfumu nthaŵi ya chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiŵiri.
4
Tsono atsogoleri onse a Aisraele atabwera, Alevi adanyamula Bokosi lachipangano lija.
5
Adabwera nalo Bokosilo pamodzi ndi chihema chamsonkhano ndiponso ziŵiya zonse zopatulika zimene zinali m'chihemamo. Ansembe ndi Alevi ndiwo amene adabwera nazo zimenezo.
6
Pamenepo mfumu Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la Aisraele amene adaasonkhana pamaso pake, ataima patsogolo pa Bokosi lachipanganolo, ankapereka nsembe za nkhosa ndi ng'ombe zosaŵerengeka.
7
Tsono ansembe adafika nalo Bokosi lachipangano la Chauta lija ku malo ake a m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, ku malo opatulika kopambana naliika kunsi kwa mapiko a akerubi.
8
Choncho akerubiwo ankatambasula mapiko ao pamwamba pa Bokosilo, kotero kuti ankaliphimba pamodzi ndi mphiko zake zonyamulira.
9
Mphikozo zinali zazitali kwambiri, kotero kuti nsonga zake zinkaonekera kukhalira ku malo opatulika kopambana patsogolo pa malo opatulika am'kati mwenimweni. Koma kunja sizinkaonekera. Ndipo zili komweko mpaka pano.
10
M'Bokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iŵiri yokha ija imene Mose adaaikamo ku Horebu, kumene Chauta adaachita chipangano ndi Aisraele, iwowo atatuluka ku Ejipito.
11
Tsono ansembe adatulukamo m'malo opatulikawo (poti ansembe onse amene analipo anali atadziyeretsa, osayang'aniranso magulu ao.)
12
Pamenepo Alevi onse amene ankaimba nyimbo, Asafu, Hemani ndi Yedutuni, ana ao pamodzi ndi abale ao, ovala nsalu za bafuta wambee, ali ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe, adaimirira cha kuvuma kwa guwa, pamodzi ndi ansembe okwanira 120 amene ankaimba malipenga.
13
Ndipo ntchito ya anthu oimba malipengawo ndi ya anthu oimba nyimbo aja, inali yakuti azimveketsa mau amodzi potamanda ndi kuthokoza Chauta, ndipo ankaimba nyimboyo ndi kuliza malipenga, ziwaya zamalipenga ndiponso zoimbira zina, kutamanda Chauta ndi mau akuti, “Ndithu Chauta ndi wabwino, pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.” Apo Nyumbayo, Nyumba ya Chauta, idadzaza ndi mtambo,
14
ndipo ansembe sankatha kuimirira kuti agwire ntchito yao yotumikira, chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Chauta unali utadzaza m'Nyumba ya Chautayo.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36