bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Chronicles 17
2 Chronicles 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 18 →
1
Yehosafati, mwana wa Asa, adaloŵa ufumu m'malo mwa bambo wake, ndipo adadzilimbitsa pofuna kulimbana ndi Aisraele.
2
Adaika magulu ankhondo ku mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda, ndipo adamanga maboma ankhondo ku dziko la Yuda ndi ku mizinda ya ku Efuremu, imene Asa bambo wake adailanda.
3
Chauta anali naye Yehosafati, chifukwa chakuti ankatsata makhalidwe oyambayamba aja a Asa bambo wake. Sadatsate Abaala,
4
koma ankatsata Mulungu wa atate ake, ndipo ankasunga malamulo ake, osatsata makhalidwe a Aisraele.
5
Nchifukwa chake Chauta adaukhazikitsa ufumuwo m'manja mwake. Anthu onse a ku Yuda ankakhoma msonkho kwa iyeyo. Choncho anali nacho chuma chambiri ndiponso ulemu.
6
Iyeyo adalimba mtima pa zinthu za Chauta. Kuwonjezera pamenepo, adathetsa akachisi ndiponso mafano a Aserimu ku Yuda.
7
Pa chaka chachitatu cha ufumu wake, Yehosafati adatuma nduna zake, Benihali, Obadiya, Zekariya, Netanele ndi Mikaya, kuti akaphunzitse ku mizinda ya ku Yuda.
8
Adapita ndi Alevi aŵa: Semaya, Netaniya, Zebadiya, Asahele, Semiramoti, Yohonatani, Adoniya, Tobiya ndi Tobadoniya. Alevi ameneŵa anali pamodzi ndi ansembe aŵa: Elisama ndi Yehoramu.
9
Ankaphunzitsa ku Yuda, ali ndi buku la malamulo a Chauta. Ndipo adayendera mizinda yonse ya ku Yuda, namaphunzitsa pakati pa anthu.
10
Maufumu onse a m'maiko ozungulira Yuda ankaopa Chauta, ndipo sadachitenso nkhondo ndi Yehosafati.
11
Afilisti ena adabwera ndi mphatso kwa Yehosafatiyo, pamodzi ndi siliva wa msonkho. Arabu nawonso adabwera ndi nkhosa zamphongo 7,700 ndi atonde 7,700.
12
Ndipo mphamvu za Yehosafati zidanka zikulirakulira. Ku Yuda adamanga malinga ndi mizinda yosungirako zinthu.
13
Choncho anali ndi nyumba zikuluzikulu zosungiramo zinthu ku mizinda ya ku Yuda. Ku Yerusalemu anali ndi ankhondo, anthu amphamvu ndi olimba mtima.
14
Chiŵerengero chao potsata mabanja ao chinali chotere: Ku Yuda, atsogoleri a zikwi anali aŵa: Adina amene anali ndi anthu amphamvu ndi olimba mtima 300,000.
15
Yehohanani, mtsogoleri wotsatana ndi iyeyo, anali ndi anthu 280,000.
16
Amasiya mwana wa Zikiri, mtsogoleri wotsatana naye, amene adaadzipereka mwaufulu ku ntchito ya Chauta, anali ndi anthu amphamvu ndi olimba mtima 200,000. (Amasiya adadzipereka kutumikira Ambuye.)
17
Ku Benjamini, Eliyada munthu wolimba mtima, anali ndi anthu 200,000 amauta ndi azishango.
18
Yehozabadi anali mtsogoleri wotsatana ndi iyeyo, ndipo anali ndi anthu okonzekera nkhondo 180,000.
19
Ameneŵa ndiwo ankatumikira mfumu, pamodzi ndi ena amene mfumu idaŵaika ku mizinda yamalinga ku dziko lonse la Yuda.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36