bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 1
Exodus 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 2 →
1
Naŵa ana a Yakobe amene adapita ku Ejipito pamodzi ndi Yakobeyo ndi mabanja ao omwe:
2
Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda,
3
Isakara, Zebuloni, Benjamini,
4
Dani, Nafutali, Gadi ndi Asere.
5
Chiŵerengero chenicheni cha anthu obadwa mwa Yakobe chinali makumi asanu ndi aŵiri. Yosefe anali atakhazikika kale ku Ejipito.
6
Tsono Yosefe adamwalira, abale ake ndi mbadwo wao wonse uja adamwaliranso.
7
Koma adzukulu a Aisraele adabala ana ambirimbiri. Adachulukana nakhala amphamvu kwambiri nkudzaza dzikolo.
8
Pambuyo pake padaloŵa mfumu ina imene sidadziŵe za Yosefe.
9
Mfumuyo idauza anthu ake kuti, “Aisraeleŵa akuchuluka kwambiri, ndipo ndi amphamvu kupambana ife.
10
Mvetsani tsono, ife tichite nawo mwanzeru anthu ameneŵa. Tiŵachenjerere, kuti asachuluke, chifukwatu pa nthaŵi ya nkhondo, iwoŵa angathe kudzaphatikizana ndi adani athu, nadzalimbana nafe, kenaka nkudzachoka m'dziko mwathu muno.”
11
Tsono adaika akapitao ao oŵagwiritsa mwankhanza ntchito yolimba Aisraelewo, kuti pakutero aŵafooketse. Aisraele adamangira Faraoyo mizinda ya Pitomu ndi Ramsesi, kumene Aejipito ankasunga chakudya chao.
12
Koma Aisraele ankati akamaŵazunza kwambiri, ndi pamene iwo tsono ankachulukirachulukira, mpaka adabalalikira m'dziko lonselo. Motero Aejipito ankaŵaopa Aisraele,
13
ndipo ankaŵakakamiza mwankhalwe kugwira ntchito yaukapolo.
14
Moyo wa Aisraele unali woŵaŵa chifukwa cha ntchito yakalavulagaga youmba njerwa, ndiponso ntchito zosiyanasiyana zam'minda. Ankaŵakakamiza mwankhanza kugwira ntchito zonse zolemetsa.
15
Tsono mfumu ya ku Ejipito ija idaitana azamba amene ankathandiza azimai achihebri pochira. Wina mwa azamba ameneŵa anali Sifira, wina anali Puwa. Mfumuyo idauza azambawo kuti,
16
“Mukamathandiza azimai achihebri pochira, akabadwa mwana wamwamuna, mupheni, akakhala wamkazi, mlekeni.”
17
Koma azambawo ankaopa Mulungu, kotero kuti mau a mfumu aja sadaŵasamale konse, ana aamunawo ankangoŵaleka amoyo.
18
Tsono mfumu ija idaŵaitana azamba aja niŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwaŵaleka ana aamuna osaŵapha?”
19
Azamba aja adayankha kuti “Azimai achihebri safanafana ndi azimai achiejipito. Iwo ngamphamvu, amati mzamba asanafike, mwana amakhala atabadwa kale.”
20
Choncho Mulungu adaŵakomera mtima azambawo, mwakuti Aisraele adapitirirabe kuchulukana, nakhala amphamvu kwambiri.
21
Tsono chifukwa choti azambawo ankaopa Mulungu, Mulungu adaŵapatsa mabanja.
22
Pamenepo Farao adalamula anthu ake kuti, “Mwana aliyense wamwamuna wobadwa mwa Ahebri azimponya mu mtsinje wa Nailo, koma ana onse aakazi aziŵaleka, azikhala moyo.”
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40