bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 34
Exodus 34
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 35 →
1
Chauta adauzanso Mose kuti, “Sema ina miyala ngati iŵiri yakale ija, kuti ndilembepo mau omwe anali pa miyala yoyamba udaphwanya ija.
2
Ukonzeke m'mamaŵa, ndipo nthaŵi yam'maŵa, ukwere phiri la Sinai kuti udzakumane nane pamwamba pa phiripo.
3
Usabwere ndi wina aliyense, ndipo wina asaoneke pa mbali iliyonse ya phirilo. Nkhosa kapena ng'ombe zisadzadye pa tsinde la phirilo.”
4
Motero Mose adasema ina miyala iŵiri ngati yakale ija, ndipo kutacha m'maŵa, adakwera phiri la Sinai monga momwe Chauta adamlamulira. Anali atanyamula miyala iŵiri ija.
5
Tsono Chauta adatsika mu mtambo, naimirira pomwe panali iyepo, ndipo adatchula dzina lake loti Chauta.
6
Adayenda pamaso pa Mose nanena mokweza kuti, “Chauta, Chauta, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndiponso wokhulupirika kwa anthu ake.
7
Amaonetsa chikondi chake kwa anthu zikwi zambirimbiri, ndipo amaŵakhululukira mphulupulu zao, zoipa zao, ndi machimo ao. Koma sadzalekerera ochimwa, ndipo adzalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha zoipa za atate ao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.”
8
Pamenepo Mose adagwada pansi napembedza.
9
Kenaka adati, “Ngati mwandikomera mtima, Inu Chauta, ndikukupemphani kuti mupite nafe. Anthuŵa ngokanika, koma Inu mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu, ndipo mutilandire ife, kuti tikhale anthu anu.”
10
Pambuyo pake Chauta adati, “Ndidzachita nanu chipangano. Ndidzachita zozizwitsa zazikulu pamaso pa anthu ako onseŵa, zimene sizidachitikepo ndi kale lonse pa dziko lonse lapansi, pakati pa mitundu ina yonse. Anthu onse amene ali ndi iweŵa adzaona zimene Ine Chauta ndingathe kuchita, chifukwa zimene ndidzachita kudzera mwa iwe nzoopsa zedi.
11
“Muzimvera malamulo amene ndakulamulani leroŵa. Ndidzapirikitsa Aamori, Akanani, Ahiti, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.
12
Musamale kuti musachite chipangano ndi anthu a ku dziko limene mukupitakolo, kuwopa kuti chingadzakhale msampha wokuchimwitsani.
13
Muzigwetsa maguwa ao, muwononge miyala yao yopatulika imene adaimiritsa, ndipo mugwetse mitengo yao yopatulika yopembedzerapo.
14
Musadzapembedze mulungu wina aliyense, chifukwa Chauta amene dzina lake ndi Kansanje, ndi Mulungu wansanjedi.
15
Anthu a ku dziko limenelo, musadzachite nawo chipangano, chifukwa akamadziipitsa popembedza milungu yao nkumaiphera nsembe, kapena adzakuitanani kuti mudye nao chakudya cha nsembe zaozo.
16
Mwina ana anu aamuna angathenso kumadzakwatira ana ao aakazi. Tsono akazi ameneŵa akamadziipitsa potumikira milungu yao, adzakopa ana anu aamuna kuti azidzatumikiranso milungu yaoyo.
17
“Musadzipangire milungu yosungunula.
18
“Muzichita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa monga ndidakulamulirani. Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, chifukwa ndi mwezi umenewu pamene inu mudachokako ku Ejipito kuja.
19
Mwana wamphongo aliyense woyamba kubadwa ndi wanga, pamodzi ndi wa zoŵeta yemwe, ndiye kuti ng'ombe ndi nkhosa zanu zomwe.
20
Koma muzidzaombola mwana woyamba kubadwa wa bulu, pakupereka nkhosa m'malo mwake. Mukapanda kumuwombola, muzidzamthyola khosi. Mwana aliyense wachisamba wamwamuna, muzidzachita choombola. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaonekere pamaso panga opanda kanthu kumanja kodzapereka.
21
“Muzigwira ntchito pa masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, musagwire ntchito iliyonse, ngakhale pa nthaŵi yolima kapena yokolola.
22
Muzichita chikondwerero cha masabata, ndi chikondwerero cha kukolola tirigu woyambirira, ndi chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pake pa chaka.
23
Amuna onse azibwera pamaso pa Ine Chauta, Mulungu wa Aisraele, katatu pa chaka.
24
Ndidzapirikitsa mitundu inayo pamene inu mukufika, ndi kukuziriza malire a dziko lanu. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzafune kulanda dziko lanulo nthaŵi zitatuzo za pa chaka, pamene mudzadziwonetse pamaso pa Ine Chauta, Mulungu wanu.
25
“Musapereke buledi wofufumitsa pamene mukupereka kwa Ine magazi a nsembe yanga. Nyama iliyonse yophera nsembe ya Paska, musaisunge mpaka m'maŵa.
26
Muzibwera ndi zokolola zoyamba ndi zabwino kwambiri ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu. Musaphike kamwanakanyama mu mkaka wa make.”
27
Chauta adauzanso Mose kuti, “Lemba mauŵa, chifukwa potsata mau ameneŵa, ndikuchita chipangano ndi iwe ndi Aisraele onse.”
28
Tsono Mose adakhala pamodzi ndi Chauta kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku, osadya kanthu. Ndipo Chautayo adalemba pa miyala iŵiri ija mau onse a chipanganocho, ndiye kuti Malamulo Khumi aja.
29
Pamene Mose adatsika phiri la Sinai atanyamula miyala iŵiri yaumboni ija, sadadziŵe kuti nkhope yake njoŵala chifukwa cholankhula ndi Chauta.
30
Aroni ndi anthu onse aja atayang'ana Mose, adaona kuti nkhope yake njoŵala. Ndipo adachita mantha osafuna kumuyandikira.
31
Koma Mose adaŵaitana, ndipo Aroni pamodzi ndi atsogoleri a Aisraele aja atabwera kwa iye, Moseyo adayamba kulankhula nawo.
32
Pambuyo pake Aisraele onse adasendera pafupi, ndipo Mose adaŵapatsa malamulo onse amene Chauta adaamuuza ku phiri la Sinai lija.
33
Mose atamaliza kulankhula nawo, adadziphimba kumaso.
34
Nthaŵi zonse Moseyo ankati akaloŵa m'chihema kukalankhula ndi Chauta, ankachotsa nsalu yophimba kumaso ija mpaka atatuluka. Tsono atatuluka, ankauza Aisraele aja zonse zimene Chauta wamulamula kuti anene.
35
Ndipo anthuwo ankaona kuti nkhope yake njoŵala, koma Moseyo ankadziphimbanso kumaso mpaka nthaŵi ina yakuti apitenso kukalankhula ndi Chauta.
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 35 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→