bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 33
Exodus 33
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 34 →
1
Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Uchokeko kuno pamodzi ndi anthu amene udabwera nawo kuchokera ku Ejipito, ndipo upite ku dziko limene ndidalonjeza kuti ndidzapatsa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Pa nthaŵi imeneyo ndidaŵauza iwowo kuti, ‘Dziko limeneli ndidzalipatsa kwa zidzukulu zanu.’
2
Ndidzatuma mngelo patsogolo pako, ndipo ndidzapirikitsa Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.
3
Pitani ku dziko lamwanaalirenji. Koma Ine sindidzapita nanu chifukwa ndinu anthu okanika, ndipo ndingathe kukuwonongani panjira.”
4
Tsono anthu atamva mau oopsaŵa, adayamba kulira, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adavala zovala zokongola.
5
Ndiye kuti Chauta anali atauza Mose kuti, “Uza Aisraelewo kuti, ‘Ndinu anthu okanika. Ndikadapita nanu pamodzi, ngakhale kamphindi kakang'ono kokha, bwenzi nditakuwonongani kwathunthu. Tsopano vulani zokongoletsa zanu, ndipo ndidzadziŵa choti ndingathe kukuchitani.’ ”
6
Motero kuyambira ku phiri lija la Horebu, Aisraele sadavalenso zokongoletsa.
7
Mose ankatenga chihema chija ndi kukachimanga kunja kwake kwa mahema, chapatali ndithu. Tsono adachitcha chihemacho dzina loti, “Chihema chamsonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Chauta ankatuluka kumahemako, napita ku chihema chamsonkhanocho.
8
Nthaŵi zonse Mose akamapita kuchihemako, anthu onse ankaimirira. Tsono aliyense ankangoimirira pakhomo pa hema lake, namayang'ana Moseyo mpaka ataloŵa m'chihema chokumaniranako ndi Chauta chija.
9
Mose ataloŵa m'chihema muja, mtambo unkatsika nuphimba pakhomo pa chihemacho, ndipo Chauta ankalankhula ndi Mose kuchokera mumtambomo.
10
Ndipo anthu ankati akaona mtambowo pa khomo la chihemacho, ankaimirira ndi kupembedza, aliyense pa khomo la hema lake.
11
Choncho Chauta ankalankhula ndi Mose pamasompamaso, monga momwe munthu amalankhulira ndi bwenzi lake. Tsono pambuyo pake Mose ankabwerera kumahema komweko. Koma mnyamata wina, dzina lake Yoswa, mwana wa Nuni, amene anali mtumiki wa Mose, sankachoka kuchihemako.
12
Mose adauza Chauta kuti, “Mwakhala mukundiwuza kuti ndiŵatsogolere anthuŵa ku dzikolo, koma simudandiwuze amene mudzamtuma kuti apite nane. Komabe mwanena kale kuti, ‘Ndikukudziŵa bwino iwe, ndipo ndakondwa nawe.’
13
Nchifukwa chake tsono ndikukupemphani kuti ngati mwandikomera mtima, mundilangize njira zanu kuti ndikudziŵeni ndipo mupitirize kundikomera mtima. Kumbukiraninso kuti mtundu wa anthu uwu ndi wanu ndithu.”
14
Ndipo Mulungu adati, “Ine ndemwe ndidzapita nawe pamodzi, ndipo ndidzakupatsa mtendere.”
15
Apo Mose adauza Chauta kuti, “Mukapanda kupita nafe limodzi, musatilole kuti tichoke pano.
16
Nanga zidzadziŵika bwanji kuti mwandikomera mtima ine pamodzi ndi anthu anu? Kodi si chifukwa chakuti mumapita nafe, ine pamodzi ndi anthu anu, kuti tizikhala osiyana ndi anthu ena onse a pa dziko lapansi?”
17
Tsono Chauta adauza Moseyo kuti, “Ndidzachita monga wanena, chifukwa ndakukomera mtima, ndipo ndikukudziŵa bwino.”
18
Apo Mose adapempha Chauta kuti, “Chonde mundiwonetse ulemerero wanu.”
19
Pamenepo Chauta adayankha kuti, “Ndikudzakuwonetsa ulemerero wanga wonse, ndipo ndidzatchula dzina langa loti Chauta pamaso pako. Ndidzakomera mtima amene nditi ndimkomere mtima, ndipo ndidzachitira chifundo amene nditi ndimchitire chifundo.”
20
Chauta adaonjeza kuti, “Koma sungathe kuwona nkhope yanga, chifukwa palibe munthu angathe kundiwona Ine, nakhala moyo.”
21
Adapitirira kunenanso kuti, “Pafupi ndi Ine pano pali thanthwe, iwe uimirire pathanthwepo.
22
Tsono ulemerero wanga ukamapita, ndikuika mu mng'alu wa thanthwe, ndipo ndikuphimba ndi dzanja langa mpaka nditabzola.
23
Kenaka ndichotsa dzanja langa, ndipo undiwona kumsana, koma nkhope yanga suiwona ai.”
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 34 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→