bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 5
Exodus 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 6 →
1
Pambuyo pake Mose ndi Aroni adapita kwa Farao nakamuuza kuti, “Naŵa mau a Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Uŵalole anthu anga apite ku chipululu, kuti akachite mwambo wachipembedzo wondilemekeza Ine.’ ”
2
Farao adayankha kuti, “Kodi Chautayo ndani kuti ine nkumvera zimenezo ndi kuŵalola Aisraele kuti apite? Chautayo sindimdziŵa, ndipo sindidzalola konse kuti Aisraele apite.”
3
Koma iwo adamuuza kuti, “Mulungu wa Ahebri adalankhula nafe. Chonde tiloleni kuti tipite ku chipululu ulendo wa masiku atatu, kuti tikapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wathu. Tikapanda kupita adzatipha ndi matenda kapena nkhondo.”
4
Koma mfumu ya ku Ejipito ija idafunsa Mose ndi Aroni kuti, “Chifukwa chiyani mukuŵasiyitsa ntchito yao Aisraele? Chokani apa, bwererani ku ntchito yanu.”
5
Farao adapitirira kuŵauza kuti, “Anthu ameneŵa akuchulukana kwambiri tsopano. Bwanji inu mufuna kuŵaletsa kugwira ntchito yao?”
6
Motero pa tsiku limenelo Farao adalamula akuluakulu a thangata, pamodzi ndi akapitao achiisraele kuti,
7
“Musaŵapatsenso udzu wa njerwa anthu ameneŵa, monga muja munkachitiramu. Alekeni azikamweta okha udzuwo.
8
Koma chiŵerengero cha njerwa chikhale chonchija, monga momwe ankaumbira kale. Musaŵachepetsere ndi pang'ono pomwe, ngaulesi ameneŵa. Nchifukwa chake akulira nkumati, ‘Tiyeni tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’
9
Muŵagwiritse ntchito yakalavulagaga anthu ameneŵa, kuti azitanganidwa ndi ntchito m'malo momangomvera zabodza.”
10
Akuluakulu a thangata ndi akapitao Achiisraele adapita kukaŵauza anthu kuti, “Farao wanena kuti, ‘Sindidzakupatsaninso udzu.
11
Muzidzimwetera nokha kulikonse komwe mungaupeze. Koma chiŵerengero cha njerwa ndi chonchija.’ ”
12
Motero anthu aja adamwazikira m'dziko lonse la Ejipito kukafunafuna udzuwo.
13
Akulu a Farao aja ogwiritsa ntchito, adafulumizitsa Aisraele naŵauza kuti, “Muziwumba chiŵerengero chonchija cha njerwa pa tsiku, monga munkachitira pamene ankakupatsani udzu.”
14
Akuluakulu a thangata a Farao aja ankamenyanso akapitao Achiisraele amene adaŵaika kuti akhale omayang'anira ntchito, namaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani lero simudaumbe chiŵerengero chonchija cha njerwa monga munkachitira kale?”
15
Tsono akapitao achiisraele aja adapita kwa Farao kukadandaula kuti, “Pepani amfumu, kaya chifukwa chiyani mwatichita zotere ife atumiki anu?
16
Udzu satipatsanso ife, bwana, komabe akutilamula kuti, ‘Kaziwumbani njerwa!’ Ndiponso akungotimenya. Anthu anu akulakwa.”
17
Farao adaŵayankha anthuwo kuti, “Ndinu alesi inu, alesi zedi, nchifukwa chake mukuti, ‘Tiyeni tipite tikapereke nsembe kwa Chauta.’
18
Chokani apa, bwererani ku ntchito yanu. Udzu asakupatseni, koma chiŵerengero cha njerwa ndi chonchija ndithu basi.”
19
Akapitao achiisraele aja adaona kuti alidi pa mavuto, ataŵauza kuti, “Muziwumba chiŵerengero chonchija cha njerwa tsiku ndi tsiku.”
20
Tsono atachoka kwa Farao kuja, adakumana ndi Mose ndi Aroni amene ankaŵadikira,
21
ndipo adaŵauza kuti, “Chauta aone mwachitazi, ndipo akuweruzeni inu poti Farao ndi nduna zake mwaŵasandutsa adani athu. Inuyo ndinu amene mwaika lupanga m'manja mwao kuti atiphe ife.”
22
Choncho Mose adapemphera kwa Chauta nati, “Inu Chauta, chifukwa chiyani mukuzunza anthu anu? Nanga ine mudanditumiranji?
23
Chipitire changa chija kwa Farao kukamuuza mau anu aja, wakhala akuzunzabe anthu anu. Ndipo Inu simudachitepo kanthu konse kuti muŵaombole anthu anu.”
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40