bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 28
Exodus 28
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 29 →
1
“Aroni ndi ana ake aamuna apatulidwe pakati pa Aisraele ndipo abwere kwa iwe, kuti akhale ansembe onditumikira. Abwere Aroni pamodzi ndi ana ake Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.
2
Umsokere mkulu wako Aroni zovala zopatulika, kuti aziwoneka wolemerera ndi wolemekezeka.
3
Ulamule anthu onse aluso, onse amene ndaŵapatsa nzeru, kuti asoke zovala za Aroni zozivala pamene udzampatule kuti akhale wansembe wanga.
4
Zovala zimene udzasokezo ndi izi: chovala chapachifuwa, chovala cha efodi, mkanjo, mwinjiro wopetedwa bwino, nduŵira ndi lamba. Asoke zovala zopatulikazo za mbale wako Aroni ndi za ana ake, kuti akhale ansembe onditumikira.
5
Zovala zimenezi anthu alusowo azisoke ndi nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.
6
Efodi aisoke ndi nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso.
7
Idzakhale ndi tizikwewo tam'mapewa tiŵiri tosokerera ku nsonga zake ziŵiri, tomangira efodiyo.
8
Padzakhalenso lamba woluka mwaluso, womangira efodi, wolukira kumodzi ndi efodiyo. Lambayo nayenso adzakhale wa nsalu ya golide, ndi wa nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.
9
Utenge miyala iŵiri ya onikisi, ndipo ulembepo maina a ana a Israele.
10
Pa mwala umodzi ulembepo maina asanu ndi limodzi, ndipo pa mwala winawo uchitenso chimodzimodzi. Ulembe mainawo motsatana malinga nkubadwa kwa ana a Israelewo.
11
Maina aowo uŵalembe mozokota pa miyala iŵiriyo, potsata luso la mmisiri wozokota miyala. Ndipo miyalayo uiike m'zoikamo zake zagolide.
12
Uike miyala iŵiri imeneyi pa tizikwewo tam'mapewa ta efodi, ngati chikumbutso cha ana a Israele. Mwa njira imeneyi, Aroniyo azidzanyamula pa mapewa mainawo, ndipo Chauta azidzaŵakumbukira iwowo.
13
Upangenso zoikamo zonga maluŵa agolide,
14
ndiponso maunyolo aŵiri a golide wokoma, opotedwa ngati zingwe, amene udzaŵalumikize ku zoikamozo.
15
“Tsono usoke chovala chapachifuwa, chopetedwa mwaluso, chomavala poweruza. Mapangidwe ake akhale ngati a efodi, ndiye kuti a nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.
16
Kukula kwake kukhale kofanana mbali zonse, ndipo chikhale chopinda paŵiri. M'litali mwake chikhale masentimita 23, muufupi mwake chimodzimodzi.
17
Usokererepo mizere inai ya miyala. Pa mzere woyamba pakhale miyala ya rubi, topazi ndi garaneti.
18
Pa mzere wachiŵiri pakhale miyala ya emeradi, safiro ndi daimondi.
19
Pa mzere wachitatu pakhale miyala ya yasinti, agate ndi ametisiti.
20
Pa mzere wachinai pakhale miyala ya berili, onikisi ndi jasipere, ndipo zonsezo ziikidwe m'zoikamo zagolide.
21
Miyala imeneyi ikhalepo khumi ndi iŵiri, potsata maina a mafuko a Aisraele. Miyalayo izokotedwe ngati zidindo, uliwonse ukhale ndi dzina la fuko limodzi.
22
Upange timaunyolo ta golide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota mwaluso ngati maukufu.
23
Upangenso mphete ziŵiri, ndipo uzilumikize pa ngodya zam'mwamba za chovala chapachifuwa.
24
Umange zingwe zagolide ziŵiri ku mphete ziŵirizo.
25
Ndipo nsonga zake zina ziŵiri za zingwezo uzimange ku zoikamo zake zija.
26
Upangenso mphete ziŵiri zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zam'munsi za chovala chapachifuwa, ku nsonga yake yam'kati, pafupi ndi chovala cha efodi chija.
27
Upangenso mphete zina ziŵiri zagolide, ndipo uzilumikize cham'munsi, kutsogolo kwake kwa malamba aŵiri a pa mapewa a efodi, pafupi ndi misoko, pa lamba wolukidwa mwaluso uja.
28
Tsono ulumikize mphete za chovala chapachifuwacho ku mphete za chovala cha efodi chija ndi kamkuzi kobiriŵira, kuti chovala chapachifuwacho chikhale pamwamba pa lamba wolukidwa mwaluso uja, ndipo chovala chapachifuwa chilumikizike bwino ku chovala cha efodi.
29
Ndipo Aroni akamaloŵa m'malo opatulika, azivala chovala chapachifuwa cholembedwa maina onse a ana a Israele, kuti Chauta azidzaŵakumbukira.
30
M'chovala chapachifuwacho uziikamo zinthu zoyera za Chauta zotchedwa Urimu ndi Tumimu, kuti zimenezo zikhale pa chifuwa cha Aroni akamapita kwa Chauta. Motero Aroni akakhala pamaso pa Chauta, nthaŵi zonse adzakhala ndi zomthandiza kuweruza bwino mpingo wa Israele.
31
“Upange mkanjo wa nsalu yobiriŵira, wophimba chovala cha efodi chija.
32
Pakati pake pa mkanjowo usiye chiboo chopisapo mutu. Chiboo chimenechi chikhale chosokerera mwamphamvu mozungulira monse, ngati khosi la malaya, kuti mkanjowu usang'ambike.
33
Pa mpendero wapansi wa mkanjowo, upange zinthu zonga makangaza. Zikhale za thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, kuzungulira mkanjo wonsewo. Pakati pa makangazawo pakhale timabelu tagolide.
34
Choncho pakhale khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, kuzungulira mpendero wonse wam'munsiwo.
35
Tsono Aroni azivala mkanjowo pamene akutumikira zaunsembe. Akamaloŵa m'malo opatulika pamaso pa Chauta kapena pochoka kumeneko, liwu la timabeluto lizidzamveka, kuti asafe.
36
“Upangenso duŵa la golide wabwino kwambiri, ulembepo mozokota mau akuti, ‘Choperekedwa kwa Chauta.’
37
Ulimange ndi kamkuzi kobiriŵira pa nduŵira ya Aroni, ndipo likhale cha kutsogolo kwa nduŵirayo.
38
Likhaledi pamphumi pake pa Aroni, motero asenze iye yemwe cholakwa chilichonse cha pa zopereka zimene Aisraele amazipatulira Chauta. Kuti Chauta alandire zopereka za anthuzo, Aroni azivala duŵali pa nduŵira yake nthaŵi zonse.
39
“Umsokerenso Aroni mwinjiro wa bafuta wokoma, ndipo umpangire nduŵira ya bafuta wokoma, ndiponso lamba wopetedwa mokongola.
40
“Ana a Aroni, uŵasokere miinjiro, malamba ndi nduŵira, kuti azisiyana ndi anthu ena, ndipo iwowo aziwoneka olemerera ndi olemekezeka.
41
Zovala zimenezi uveke mbale wako Aroni ndi ana ake. Tsono uŵadzoze, uŵapatse udindo ndi kuŵapatula, kuti akhale ansembe onditumikira.
42
Uŵasokere akabudula ofika m'ntchafu, kuti asamaonetse maliseche.
43
Aroni ndi ana ake azivala zimenezi nthaŵi zonse akamapita ku chihema chamsonkhano kapena ku guwa, kukanditumikira ku malo opatulika aja, kuwopa kuti angachimwe ndipo angafe. Lamulo limeneli, lonena za Aroni ndi zidzukulu zake, ndi lokhazikika mpaka muyaya.
← Chapter 27
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 29 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→