bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 16
Exodus 16
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 17 →
1
Pambuyo pake khamu lonse la Aisraele lidayamba ulendo kuchokera ku Elimu, ndipo pa tsiku la 15 la mwezi wachiŵiri atachoka ku Ejipito, adafika ku chipululu cha Sini, chimene chili pakati pa Elimu ndi Sinai.
2
Ndipo khamu lonse lidadandaulira Mose ndi Aroni m'chipululu muja kuti,
3
“Kukadakhala bwino Chauta akadatiphera ku Ejipito konkuja, kumene tinkakhala tikudya nyama ndi buledi, ndipo tinkakhuta. Koma inu mwatifikitsa kuchipululu kuno kuti mutiphe tonse ndi njala.”
4
Apo Chauta adauza Mose kuti, “Chabwino, ndikupatsani chakudya chimene chidzagwa ngati mvula kuchokera kumwamba. Anthu azituluka tsiku ndi tsiku kukatola chakudya chokwanira tsiku limodzi, kuti ndiŵayese ndipo ndiwone ngati adzayenda motsata malamulo anga kapena ai.
5
Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, pokonza chimene adatola adzapeza kuti nchokwanira masiku aŵiri.”
6
Tsono Mose ndi Aroni adauza Aisraele onse kuti, “Madzulo omwe ano mudzadziŵa kuti ndi Chauta amene adakutulutsani ku Ejipito,
7
m'maŵa mwake mudzaona ulemerero wa Chauta. Wamva madandaulo anu omuŵiringulira aja. Kodi ife ndife yani, kuti inu muzitiŵiringulira?”
8
Ndipo Mose adati, “Ndi Chauta amene adzakupatsani madzulo nyama yoti mudye, ndi m'maŵa buledi woti nkukhuta, chifukwa choti wamva madandaulo anu onse omuŵiringulira aja. Ife ndife yani? Madandaulo anu simudaŵiringulire ife ai, koma Chauta.”
9
Pamenepo Mose adauza Aroni kuti akauze anthuwo kuti, “Bwerani, mudzaime pamaso pa Chauta chifukwa wamva madandaulo anu onse.”
10
Tsono Aroni akulankhula ndi khamu lonse lija, khamulo lidatembenuka kupenya ku chipululu, ndipo ulemerero wa Chauta udaoneka mu mtambo mwadzidzidzi.
11
Chauta adauza Mose kuti,
12
“Ndamva madandaulo a Aisraele. Ndiye uŵauze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama, ndipo m'maŵa mudzadya buledi, choncho mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’ ”
13
Motero madzulo kudagwa zinziri, ndipo zidadzaza ponseponse pamahemapo. M'maŵa ndithu padagwa mame ponse pozungulira mahemawo.
14
Mamewo atangokamuka, panthakapo m'chipululu muja padapezeka tinthu tina topyapyala, tambee ngati chipale, ndiponso tonyata.
15
Aisraele ataona tinthuto sadatidziŵe kuti nchiyani, mwakuti adayamba kufunsana kuti “Kodi timeneti ntiyani?” Mose adaŵauza kuti, “Ameneyu ndi buledi yemwe Chauta wakupatsani kuti mudye.
16
Chauta walamula kuti aliyense mwa inu atole womukwanira kudya, ndiye kuti malita aŵiri pa munthu mmodzi, malinga ndi chiŵerengero cha anthu onse a m'hema mwake.”
17
Aisraele adachitadi zimenezo. Ena adatola tambiri, koma ena pang'ono.
18
Tsono atayesa ndi muyeso wa malita aŵiri, adaona kuti amene adaatola tambiri, sitidaŵatsalireko, amene adaatola pang'ono, sitidaŵathere. Aliyense adangotola tokwanira.
19
Pamenepo Mose adaŵauza kuti, “Munthu aliyense asasungeko mpaka m'maŵa.”
20
Komabe ena mwa iwowo sadamvere zimene adaanena Mosezo, adasungako mpaka m'maŵa mwake. Koma kutacha, adaona kuti tonseto tagwa mphutsi, ndipo tikununkha. Apo Mose adaŵapsera mtima anthuwo.
21
Ankatola m'maŵa mulimonse, ndipo aliyense ankatola monga m'mene ankasoŵera. Koma dzuŵa likatentha, tinthuto tinkasungunuka.
22
Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi ankatola chakudya cha masiku aŵiri, chokwanira malita anai ndi theka pa munthu mmodzi. Ndipo atsogoleri onse a Aisraele adabwera kwa Mose kudzamuuza zimenezo.
23
Tsono Mose adaŵauza kuti, “Chauta walamula kuti, ‘Maŵa ndi tsiku lopumula, tsiku la Sabata, loperekedwa kwa Chauta. Wotchani yense amene mufuna kuwotcha, ndipo muphike yense amene mufuna kuphika. Wotsalako mumsunge padera mpaka maŵa.’ ”
24
Mose atalamula zimenezi, anthuwo adasungadi totsalato mpaka m'maŵa mwake tosaonongeka, ndipo sitidagwe mphutsi.
25
Pambuyo pake Mose adauza anthuwo kuti, “Idyani ameneyu lero, chifukwa lero ndi tsiku la Sabata loperekedwa kwa Chauta. Lero simumpezatu kunjaku.
26
Mutole chakudya pa masiku asanu ndi limodzi. Koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, tsiku la Sabata, chakudyacho sichidzapezeka.”
27
Pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo anthu ena adaapita kuti akatole chakudya, koma sadachipeze.
28
Pamenepo Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi mudzakhalabe osamvera mau anga ndi malamulo anga mpaka liti?
29
Kumbukirani kuti ndine Chauta, amene ndidakupatsani tsiku la Sabata. Tsono chifukwa cha chimenechi ndimakupatsani chakudya chokwanira masiku aŵiri pa tsiku lachisanu ndi chimodzi. Aliyense azingokhala komwe aliriko pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Asachoke ndi mmodzi yemwe pakhomo pake.”
30
Motero anthu sankagwira ntchito pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri.
31
Aisraele chakudyacho adachitcha mana. Maonekedwe ake anali onga njere zamapira, ndiponso oyera. Pakudya, ankazuna ngati buledi wopangidwa ndi uchi.
32
Tsono Mose adati, “Chauta walamula kuti ‘Musungeko mana ena kuti zidzukulu zanu zidzaone chakudya chimene ndidakupatsani m'chipululu, nditakutulutsani ku Ejipito kuja.’ ”
33
Ndipo Mose adauza Aroni kuti, “Tenga mtsuko, uikemo mana wokwana malita aŵiri. Utatero uike pamaso pa Chauta kuti manayo asungike chifukwa cha zidzukulu zanu.”
34
Monga momwe Chauta adalamulira Mose, Aroni adaika mtsukowo patsogolo pa bokosi lachipangano, kuti manayo asungike.
35
Aisraelewo adakhala alikudya mana zaka makumi anai, mpaka adakafika kudziko kokhala anthu. Adadya mana mpaka adafika ku malire a dziko la Kanani.
36
Malita aŵiri alingana ndi gawo lachikhumi la efa.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→