bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 17
Exodus 17
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 18 →
1
Khamu lonse la Aisraele lija lidachoka ku chipululu cha Sini kuja, ndipo linkangoyenda kuchoka pa chigono china mpaka pa chigono chinanso, monga momwe Chauta ankalamulira. Tsono adakamanga mahema ku Refidimu. Kumeneko kunalibe madzi akumwa.
2
Ndiye anthuwo adayamba kukangana ndi Mose, namanena kuti, “Tipatseni madzi akumwa.” Mose adaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Chifukwa chiyani mukuyesa Chauta?”
3
Koma anthu aja anali ndi ludzu loopsa, ndipo ankangoŵiringulira Mose, kuti “Chifukwa chiyani mudatitulutsa ku Ejipito kuti mutiphe ndi ludzu, ife pamodzi ndi ana athu ndi zoŵeta zathu?”
4
Apo Mose adapemphera mokweza mau kwa Chauta, adati, “Kodi anthu ameneŵa ndichite nawo chiyani? Iwowo ngokonzeka kundiponya miyala.”
5
Pamenepo Chauta adauza Mose kuti, “Tengako atsogoleri ena a Aisraele, mukakhale patsogolo pa anthuwo. Tsono utenge ndodo udamenya nayo madzi a mu mtsinje wa Nailo ija, ndipo upite.
6
Ine ndidzakhala patsogolo pako kumeneko pafupi ndi thanthwelo, pa phiri la Horebu. Ukamenye thanthwe, tsono mudzatuluka madzi m'thanthwemo, kuti anthuwo amwe.” Mose adachitadi zimenezo pamaso pa atsogoleri a Aisraele aja.
7
Malowo adaŵatcha Mayeso ndiponso Makangano, chifukwa Aisraele adakangana ndi Mose, ndipo adayesa Chauta pofunsa kuti, “Kodi Chauta ali nafe, kapena ai?”
8
Tsono kudabwera Aamaleke ku Refidimu kudzamenyana ndi Aisraele.
9
Mose adauza Yoswa kuti, “Tisankhulireko amuna ena, maŵa mupite kukamenyana nawo nkhondo Aamaleke. Ine ndidzaimirira pamwamba pa phiri, nditagwira ndodo adandipatsa Mulungu ija.”
10
Yoswa adachitadi monga momwe Mose adalamulira, adatuluka kukamenyana ndi Aamalekewo. Nthaŵi yomweyo Mose, Aroni ndi Huri adakwera pamwamba pa phiri.
11
Mose ankati akakweza manja ake, Aisraele ankapambana pa nkhondoyo, koma akatsitsa pansi manja, Aamaleke ankapambana.
12
Tsono manja a Mose atatopa, Aroni pamodzi ndi Huri uja adatenga mwala namkhazikira Mose kuti akhalepo. Aŵiriwo adakhala wina uku wina uku, atagwirira manja a Mose aja. Adaŵagwirira ndithu mpaka dzuŵa kuloŵa.
13
Ndipo Yoswa adagonjetseratu kwathunthu Aamalekewo.
14
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Zimenezi muzilembe m'buku kuti zidzakumbukike, ndipo munene pamaso pa Yoswa kuti Aamalekewo adzafafanizika kwathunthu.”
15
Ndipo Mose adamanga guwa nalitcha kuti, “Chauta ndiye mbendera yanga.”
16
Adati, “Kwezetsani mbendera ya Chauta! Chauta adzapitirirabe kumenya nkhondo ndi Aamaleke mpaka muyaya.”
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40