bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 12
Exodus 12
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 13 →
1
Chauta adalankhula kwa Mose ndi Aroni m'dziko lija la Ejipito kuti,
2
“Mwezi uno udzakhala mwezi wanu woyambira chaka.
3
Mulengeze kwa khamu lonse la Aisraele kuti pa tsiku lakhumi la mwezi uno, munthu aliyense adzasankhulire banja lake mwanawankhosa mmodzi. Banja lililonse lidzatenge mwanawankhosa mmodzi.
4
Banja likachepa, kuti silingathe kudya nyama yonseyo, mabanja aŵiri oyandikana aphatikizane pamodzi, monga momwe aliri anthu, tsono onsewo adyere limodzi. Mulinganiziretu chiŵerengero cha anthu odya nyamayo, modziŵa m'mene munthu mmodzi angadyere.
5
Mwanawankhosa wake adzakhale wopanda chilema, wamphongo, wa chaka chimodzi. Mungathe kusankhulanso mwanawambuzi.
6
Mumsunge mpaka tsiku la 14 la mwezi, pamene khamu lonse la Aisraele lidzaphe nyama zaozo madzulo ndithu.
7
Tsono adzatengeko magazi a nyamayo ndi kuwaza pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo, ndi pamwamba pa chitseko cha nyumba m'mene akadyeremo nyamayo.
8
Nyamayo adzaiwotche usiku womwewo, ndipo adzaidye ndi buledi wosafufumitsa ndiponso ndi ndiwo zoŵaŵa zamasamba.
9
Musaidye yaiŵisi kapena yophika, koma muwotche yonse pamodzi ndi mutu wake womwe, miyendo ndi zonse zam'kati.
10
Musasiyeko nyama ina mpaka m'maŵa, motero ina ikatsalako, muitenthe.
11
Kudya kwake, muzikadya motere: Mudzavale zaulendo, nsapato zanu zili kuphazi, ndodo zili kumanja. Mudzadye mofulumira. Limeneli ndilo tsiku la Paska ya Chauta.
12
Usiku umenewo, Ine ndidzapita m'dziko la Ejipito ndipo m'dziko lonselo ndidzapha ana onse oyamba kubadwa, a anthu ndi a nyama omwe. Ndidzalanga milungu yonse ya Ejipito. Ine ndine Chauta.
13
Magaziwo adzakhala chizindikiro pa nyumba zimene mumakhalamo. Ndikadzangoona magaziwo, ndidzakupitirirani inuyo, ndipo mliri wosakaza sudzakugwerani, pamene ndidzakanthe dziko la Ejipito.
14
“Tsiku limeneli muzidzalisunga. Tsiku limeneli muzidzalikumbukira, ndipo muzidzachita chikondwerero, kupembedza Chauta. Mibadwo yonse izidzakumbukira tsikuli, kuti likhale lamulo lamuyaya, lakuti muzidzachita chikondwerero pa tsiku limenelo.”
15
Tsono Chauta adati, “Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku loyamba muzidzachotsa zotupitsira buledi m'nyumba zanu zonse, chifukwa pa masiku asanu ndi aŵiri aliyense wodya buledi wofufumitsa adzachotsedwa pakati pa Aisraele.
16
Pa tsiku loyamba, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, muzidzachita msonkhano wachipembedzo. Musadzagwire ntchito pa masiku amenewo, koma chakudya chokha choti aliyense adye, mudzatha kukonza.
17
Chikondwerero chimenechi cha buledi wosafufumitsa, mudzachisunge ndithu, chifukwa pa tsiku limeneli mpamene ndidzatulutse magulu anu onse kuchoka m'dziko la Ejipito. Tsono muzidzasunga tsiku limeneli pa mibadwo yanu yonse, ngati lamulo lamuyaya.
18
Muzidzadya buledi wosafufumitsa kuyambira madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba, mpaka madzulo a tsiku la 21 mwezi womwewo.
19
Pa masiku asanu ndi aŵiri onsewo, m'nyumba mwanu musadzapezeke chofufumitsira buledi, chifukwa wina aliyense akadzadya chakudya chofufumitsa, adzachotsedwa pa mtundu wa Aisraele, mlendo ngakhale mbadwa yomwe.
20
Musadye chilichonse chofufumitsa, ndipo ku nyumba zanu zonse muzidzangodya buledi wosafufumitsa.”
21
Ndipo Mose adaitana atsogoleri onse a Aisraele, naŵauza kuti, “Pitani kasankhuleni mwanawankhosa woyenera pa banja lililonse, ndipo muphe nyama ya Paskayo.
22
Mutenge nthambi ya kachitsamba ka hisope, muiviike m'magazi amene mwaŵathira m'mbale. Tsono muwaze magaziwo pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo ndi pamwamba pa chitseko. Wina aliyense asatuluke m'nyumba mwake mpaka m'maŵa.
23
Chauta adzapita m'dziko lonse la Ejipito, ndi kumapha Aejipito. Azidzati akaona magaziwo pamwamba pa chitseko ndi pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo, azidzapitirira khomolo ndipo sadzamulola mngelo wake woononga kuti aloŵe m'nyumba mwanu kuti akupheni.
24
Muziŵamvera malamulo ameneŵa inuyo ndi ana anu mpaka muyaya.
25
Ndipo mukadzaloŵa m'dziko limene Chauta akukupatsanilo, monga momwe adalonjezera, muzidzasunga mwambo umenewu.
26
Ana anu azidzakufunsani kuti, ‘Kodi mwambo umenewu umatanthauza chiyani?’
27
Pamenepo inu muzidzayankha kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Chauta, chifukwa chakuti adapitirira nyumba za Aisraele ku Ejipito; pamene ankapha Aejipito, nyumba zathu adazisiya.’ ” Atamva zimenezi, anthu adaŵerama pansi, napembedza.
28
Aisraele adapita, ndipo adamvera zimenezo. Adachitadi zonse zimene Chauta adalamula Mose ndi Aroni.
29
Pakati pa usiku, Chauta adapha ana onse achisamba m'dziko la Ejipito. Adayambira mwana wachisamba wa Farao amene ankayembekezeka kuloŵa ufumu wake, mpaka ana a akaidi a m'nyumba zamdima za m'ndende. Ana onse oyamba kubadwa a nyama adaphedwanso ndithu.
30
Farao ndi nduna zake zonse, pamodzi ndi Aejipito onse, adadzuka pakati pa usiku, ndipo m'dziko lonse la Ejipito munali maliro okhaokha, chifukwa panalibe banja lopanda mwana wakufa.
31
Usiku womwewo Farao adaitana Mose ndi Aroni, ndipo adaŵalamula kuti, “Inu pamodzi ndi Aisraele onse, fulumirani, mutuluke. Asiyeni anthu anga, pitani mukapembedze Chauta monga momwe mudanenera.
32
Mutenge nkhosa zanu, mbuzi zanu ndi ng'ombe zanu zomwe, monga momwe mudanenera, ndipo muchoke. Mukapemphere kuti nanenso andidalitseko.”
33
Aejipito adafulumizitsa anthu kuti achoke m'dzikomo, namanena kuti, “Tifatu tonsefe.”
34
Motero anthuwo adanyamula pa mapewa ao ufa wa buledi wokandiratu asanathire chofufumitsira, pamodzi ndi mbale zokandiramo buledi zili zokulunga m'nsalu.
35
Ndiponso Aisraele anali atachita monga momwe Mose adaaŵauzira. Adaapempha kwa Aejipitowo zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide, ndiponso zovala.
36
Chauta adasandutsa Aejipito aja kuti akhale okoma mtima, ndipo anthuwo adapatsa Aisraele zonse zimene ankapempha. Motero Aisraele adalandako chuma cha Aejipito aja.
37
Tsono Aisraele adanyamuka ulendo kuchoka ku Ramsesi kupita ku Sukoti. Anthu aamuna analipo zikwi 600, osaŵerenga akazi ndi ana.
38
Panalinso gulu lalikulu la anthu ena, ndiponso nkhosa, mbuzi pamodzi ndi ng'ombe zomwe.
39
Adaphika mitanda ya buledi wosafufumitsa wa ufa wokandiratu, yomwe adachoka nayo ku Ejipito kuja. Ufa wabuledi wokandiratuwo unali wosathira chofufumitsira chifukwa anali atapirikitsidwa mwadzidzidzi ku Ejipito kuja. Panalibe nthaŵi yophikira chakudya chao cha kamba.
40
Aisraele adakhalako zaka 430 ku Ejipito kuja.
41
Pa tsiku lomwe zaka 430 zinkatha, magulu onse a Chauta adachokako ku Ejipito.
42
Usiku wonse Chauta adachezera kutulutsa Aisraelewo m'dziko lija la Ejipito. Nchifukwa chake usiku umenewu ndi wopatulikira Chauta pa mibadwo yonse, kuti ukhale usiku womwe Aisraele onse ayenera kuchezera.
43
Tsono Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Malamulo ake a Paska ndi aŵa: Mlendo aliyense asadyeko.
44
Kapolo aliyense wochita kugulidwa angadyeko, koma atayamba waumbalidwa.
45
Mlendo kapena wantchito wanu aliyense asadyeko.
46
Muzidyera m'nyumba imodzi, musatuluke nayo panja nyamayo, ndipo musaphwanye mafupa ake.
47
Mtundu wonse wa Aisraele uzichita mwambo umenewu.
48
Mlendo akakhala pakati panu, namafuna kuti achite nao mwambo wa Paska ya Chauta, muziyamba mwaumbala amuna onse am'banjamo. Pambuyo pake angathe kuloŵa ndi kumachita nao mwambowo. Iyeyo muzimuyesa ngati mbadwa yeniyeni ya Israele. Koma wosaumbalidwa asadyeko.
49
Lamulo limeneli ndi la mbadwa yeniyeni ya Israele, ndiponso la mlendo woumbalidwa amene ali pakati panu.”
50
Aisraele onse adamveradi zimenezi, ndipo ankachitadi zimene Chauta adalamula Mose ndi Aroni.
51
Pa tsiku lomwelo ndi pamene Chauta adatulutsa Aisraele ku Ejipito mwa magulumagulu ao.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40