bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 29
Exodus 29
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 30 →
1
“Pofuna kumpatula Aroni ndi ana ake, kuti akhale ansembe onditumikira, uchite izi: Utenge ng'ombe yamphongo ndi nkhosa zamphongo ziŵiri zopanda chilema.
2
Utengenso buledi wosafufumitsa, makeke osatupitsa, osakaniza ndi mafuta, ndiponso mitanda ya buledi yopsapsalala yopaka mafuta. Zimenezi uzipange ndi ufa wosalala watirigu.
3
Uziike m'lichero, ndipo ubwere nazo kwa Ine, pamene ukupereka nsembe ng'ombe yamphongo ija ndi nkhosa zija.
4
Ubwere naye Aroni ku khomo la chihema chamsonkhano, pamodzi ndi ana ake aamuna, ndipo onsewo uŵayeretse m'madzi.
5
Tsono utenge zovala zija ndi kumuveka Aroni mwinjiro ndi mkanjo wautali wovala pamwamba pa efodi, ndiponso chovala chapachifuwa. Ndipo umange lamba woluka mwaluso uja m'chiwuno mwake.
6
Umuveke nduŵira kumutu kwake, ndi duŵa lopatulika lija panduŵirapo.
7
Tsono utenge mafuta odzozera aja ndi kuŵatsanyulira kumutu kwake kuti umdzoze.
8
Kenaka ubwere ndi ana ake aamuna, ndipo uŵaveke miinjiro.
9
Uŵavekenso lamba m'chiwuno mwao ndi nduŵira. Motero iwoŵa adzakhala ansembe anga potsata lamulo langa losatha. Umu ndimo m'mene umdzozere Aroni ndi ana ake aamuna.
10
“Pambuyo pake ubwere ndi ng'ombe yamphongo pakhomo pa chihema chamsonkhano. Tsono Aroni ndi ana ake asanjike manja ao pamutu pa ng'ombeyo.
11
Kenaka muiphe ng'ombeyo pamaso pa Chauta, pa khomo la chihema chamsonkhano.
12
Utengeko magazi a ng'ombeyo, ndipo uŵapake ndi chala chako pa nyanga za guwa. Tsono magazi otsalawo uŵatsanyulire patsinde pa guwalo.
13
Pambuyo pake utenge mafuta onse okuta matumbo, mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ndiponso imso ziŵiri, pamodzi ndi mafuta ozikuta. Zonsezi uzipereke, ndipo uzitenthere pa guwalo.
14
Koma nyama yake, chikumba chake ndi ndoŵe zake, ukazitenthere kunja kwa mahema. Chopereka chimenechi ndicho cha nsembe yopepesera machimo.
15
“Utenge imodzi mwa nkhosa ziŵiri zamphongo zija, ndipo Aroni ndi ana ake aamuna asanjike manja ao pamutu pa nkhosayo.
16
Tsono uiphe ndipo utenge magazi ake ndi kuwaza pa mbali zonse za guwa.
17
Nkhosayo uiduledule, ndipo utatsuka matumbo ndi miyendo yake, uziike mosanjikiza pamwamba pa nthuli zake ndi mutu.
18
Ndipo upsereze nkhosa yonseyo paguwapo. Imeneyo idzakhala nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta. Idzakhala nsembe ya fungo lokoma yopereka pa moto kwa Chauta.
19
“Tsono utenge nkhosa yamphongo inayo. Aroni ndi ana ake aamuna asanjike manja ao pamutu pa nkhosayo.
20
Muiphe, ndipo mutengeko magazi ake ndi kupaka pa khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa khutu la ku dzanja lamanja la ana ake aamuna. Upakenso pa chala chao chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja. Magazi ena uwaze pa mbali zonse za guwa.
21
Utengeko magazi otsalira pa guwa ndiponso mafuta ena odzozera, uwaze Aroni ndi zovala zake. Uwazenso ana ake ndi zovala zao. Tsono iyeyo ndi ana ake adzakhala opatulika, pamodzi ndi zovala zomwezo.
22
“Nkhosa yamphongo ija utengeko mafuta ake, mchira wake wamafuta, mafuta okuta matumbo, mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, imso ziŵiri ndi mafuta ozikutawo, ndiponso ntchafu ya ku dzanja lamanja, chifukwa nkhosa imeneyi ndi nsembe ya pa mwambo wodzozera.
23
M'lichero limene lili m'Nyumba ya Chauta utengeko buledi mmodzi wosafufumitsa, keke imodzi yosakaniza ndi mafuta, ndiponso buledi mmodzi wopsapsalala.
24
Chakudya chonsechi uchiike m'manja mwa Aroni ndi mwa ana ake, ndipo iwowo achiweyule kuti chikhale chopereka choweyula kwa ine.
25
Kenaka uchotse zonsezo m'manja mwao, ndipo uzipsereze pa guwa, pamwamba penipeni pa zopereka zija kuti zipereke fungo lokondweretsa Chauta. Imeneyi ndiyo nsembe yopsereza kwa Chauta.
26
“Utenge nganga ya nkhosa yamphongo imene adaipha podzoza Aroni, ndipo uiweyule kuti ikhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta. Imeneyi ndiyo idzakhala gawo lako.
27
Pambuyo pake upatule zigawo za nkhosa yopereka pa mwambo wodzozera Aroni ndi ana ake, ndiye kuti nganga yoperekedwa ngati chopereka choweyula ija, ndiponso ntchafu yoperekedwa ngati chopereka choweyula ija.
28
Pa zimene Aisraele azipereka, zimenezi zikhale za Aroni ndi ana ake nthaŵi zonse. Alandire ndiwo ansembe zonsezi zochokera pa zopereka zamtendere za Aisraele pakuti ndizo mphatso zao za Aisraele kwa Chauta.
29
“Zovala za Aroni zaunsembe zidzakhale za ana ake aamuna iyeyo atafa, kuti anawo azivala zimenezo pamene akudzozedwa ndi kulandira udindo wao.
30
Mwana wa Aroni womloŵera m'malo kuti akhale wansembe, azidzavala zimenezi masiku asanu ndi aŵiri, pamene akuloŵa m'chihema chamsonkhano kukatumikira m'malo oyera.
31
“Tsono utenge nkhosa yamphongo yophera mwambo woloŵera unsembe, uiphike m'malo oyera.
32
Ndipo Aroni ndi ana akewo adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, pamodzi ndi buledi wam'lichero uja pakhomo pa chihema chamsonkhano.
33
Adzadye zonse zimene adazipereka kwa Chauta pa mwambo wopepesera machimo poŵadzoza ndi kuŵapatula. Munthu wamba asadyeko, chifukwa nzoyera.
34
Nyama ikatsalako, kapena buledi akatsalako mpaka m'maŵa, utenthe. Asadye zimenezo chifukwa nzoyera.
35
“Zonse zimene ndakulamulazi umchitire Aroni ndi ana ake aamuna omwe. Udzachite mwambo wakuŵapatula pa masiku asanu ndi aŵiri.
36
Tsiku ndi tsiku uzipereka ng'ombe yamphongo yopepesera machimo, kuti machimowo akhululukidwe. Uyeretse guwalo pakuliperekera nsembe yopepesera machimo. Kenaka ulidzoze kuti likhale lopatulika.
37
Pa masiku asanu ndi aŵiri uzipereka nsembe zoyeretsera guwalo, ndipo uzilipatula. Pambuyo pake guwalo lidzakhala loyera kwathunthu, ndipo chilichonse chimene chidzakhudze guwalo chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake.
38
“Pa guwa lansembe uziperekapo izi: nthaŵi zonse tsiku ndi tsiku, uzipereka anaankhosa aŵiri a chaka chimodzi.
39
Mwanawankhosa wina uzimpereka m'maŵa, wina madzulo.
40
Pamodzi ndi mwanawankhosa woyambayo, uzipereka kilogaramu limodzi la ufa wosalala watirigu wosakaniza ndi lita limodzi la mafuta abwino, ndiponso lita limodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa.
41
Tsono uzipereka mwanawankhosa wachiŵiriyo madzulo ndithu. Pamodzi ndi mwanawankhosayo, uziperekanso chopereka chachakudya ndi cha chakumwa, monga zam'maŵa zija, kuti zipereke fungo lokoma ndipo zikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta.
42
Zopereka zopsereza zimenezi ziziperekedwa nthaŵi zonse pa mibadwo yonse. Muzizipereka pamaso pa Ine Chauta pa chipata choloŵera m'chihema chamsonkhano, kumene ndizidzakumana ndi anthu anga ndi kulankhula nawo.
43
Kumeneko ndiko ndizidzakumana ndi Aisraele, ndipo malo amenewo azidzakhala oyeretsedwa chifukwa cha ulemerero wanga.
44
Chihema chamsonkhanocho ndidzachisandutsa kuti chikhale chopatulika, pamodzi ndi guwa lomwe. Ndipo Aroni ndidzampatula pamodzi ndi ana ake aamuna, kuti akhale ansembe anga onditumikira.
45
Ndidzakhala pakati pa anthu anga Aisraele, ndipo ndidzakhala Mulungu wao.
46
Adzandidziŵa Ine Chauta amene ndidaŵatulutsa ku Ejipito kuti ndikhale pakati pao. Ine ndine Chauta, Mulungu wao.
← Chapter 28
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 30 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→