bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 2
Exodus 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 3 →
1
Munthu wina wa fuko la Levi adakwatira mkazi wa fuko lomwelo.
2
Mkaziyo adatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo ndi wokongola, adamubisa miyezi itatu.
3
Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sangathe kumubisanso, maiyo adatenga kadengu kabango, nakamata phula. Tsono mwanayo adamuika m'menemo, nakabisa kadenguko pakati pa bango lalitali m'madzi, pafupi ndi chibumi cha mtsinjewo.
4
Ndipo mlongo wake wa mwanayo adaimirira pafupi namangopenyetsetsa, kuti aone zimene zimchitikire mwanayo.
5
Nthaŵi ina mwana wamkazi wa Farao adapita kumtsinje komweko kukasamba. Iyeyo anali ndi adzakazi ake, ndipo onsewo ankangoyenda m'mbali mwa mtsinje muja. Tsono mwana wa Farao uja adakaona kadengu kaja m'bangomo, natuma mdzakazi wake kuti akakatenge.
6
Atakatsekula kadengu kaja, adapezamo kamwana kakamuna kakungolira. Mtsikanayo adachita nako chifundo kamwanako, ndipo adati, “Kameneka ndi kamwana kachihebri.”
7
Apo mlongo wake wa mwanayo adafunsa kuti, “Bwanji ndikakuitanireni mai wachihebri woti akakulerereni mwanayu?” Mwana wa Farao uja adayankha kuti,
8
“Chabwino, pita.” Mlongo wakeyo adapita nakaitana amai ake a mwanayo.
9
Tsono mwana wa Farao uja adauza maiyo kuti, “Mtengeni mwanayu, mukandilerere, ine ndidzakulipirani.” Motero mai uja adamtenga mwanayo, nakamlera.
10
Mwana uja atakula adakampereka kwa mwana wa Farao, ndipo adasanduka mwana wake ndithu. Mwana wa Faraoyo adamutcha Mose, chifukwa adati, “Ndidamuvuula m'madzi.”
11
Tsiku lina Mose, atakula ndithu, adapita kukacheza kwa anthu a mtundu wake uja, ndipo adaona m'mene ankaŵagwiritsira ntchito moŵazunza kwambiri. Adaona Mwejipito wina akumenya Muhebri, mmodzi mwa anthu a mtundu wake.
12
Pamenepo Mose atayang'ana uku ndi uku, naona kuti kulibe anthu, adamupha Mwejipitoyo, nafotsera mtembo wake mu mchenga.
13
M'maŵa mwake atabweranso, adaona kuti Ahebri aŵiri akumenyana. Mose adafunsa wolakwayo kuti, “Chifukwa chiyani ukumumenya mnzako?”
14
Iye uja adafunsa Mose kuti, “Kodi ndani adakuika kuti uzitilamula ndi kumatiweruza? Kodi ukufuna kundipha monga muja udaphera Mwejipito uja?” Pamenepo Mose adachita mantha kwambiri naganiza mumtima mwake kuti, “Ha, anthu akudziŵa zimene ndidachita zija!”
15
Tsono Farao atamva, adayesetsa kuti aphe Mose, koma Mose adathaŵa nakakhala ku dziko la Midiyani. Ali kumeneko, tsiku lina adakhala pansi pafupi ndi chitsime.
16
Amene anali wansembe ku Midiyaniko anali ndi ana aakazi asanu ndi aŵiri. Ana aakaziwo adabwera kudzatunga madzi, kuti adzaze m'chomwera nkhosa ndi mbuzi za bambo wao.
17
Koma kudabwera abusa ena naŵapirikitsa atsikanawo. Apo Mose uja adaimirira naŵathandiza atsikana aja, ndipo adamwetsa zoŵeta zao zonse zija.
18
Atsikana atabwerera kwa bambo wao Reuele, bambo waoyo adaŵafunsa kuti, “Bwanji mwabwerako msanga chotere lero?”
19
Iwo aja adayankha kuti, “Mwejipito wina ndiye amene watitchinjiriza kwa abusa, ndipo watitungira madzi omwetsa zoŵeta zonsezi.”
20
Tsono bambo waoyo adaŵafunsa kuti, “Nanga iyeyo ali kuti? Chifukwa chiyani mwamsiya komweko munthu ameneyo? Pitani mukamuitane, adzadye nao kuno.”
21
Choncho Mose adavomera kukhala nao komweko, ndipo Reuele adapatsa Moseyo mwana wake Zipora kuti akhale mkazi wake.
22
Zipora adabala mwana wamwamuna. Pamenepo Mose adati, “Ndine mlendo m'dziko lachilendo.” Motero adamutcha mwanayo Geresomo.
23
Patapita nthaŵi yaitali ndithu, mfumu ya ku Ejipito ija idamwalira. Monsemo Aisraele ankangolira nawo ukapolo wao uja, namapempha chithandizo, ndipo kulira kwao kudamveka kwa Mulungu.
24
Mulungu adamva kudandaula kwaoko, nakumbukira chipangano chake chija chimene adachita ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
25
Mulungu ataŵapenya Aisraelewo, adaŵamvera chifundo.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40