bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 32
Exodus 32
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 33 →
1
Anthu ataona kuti Mose wakhalitsako kuphiri osatsikako, adasonkhana kwa Aroni, ndipo adamuuza kuti, “Tiyeni mutipangire milungu yotitsogolera ife, chifukwa sitikudziŵa chomwe chamugwera Moseyo, amene adatitsogolera potitulutsa ku Ejipito kuja.”
2
Tsono Aroni adauza anthuwo kuti, “Vulani nsapule zagolide kukhutu kwa akazi anu, kwa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi omwe, ndipo mubwere nazo kwa ine.”
3
Anthuwo adavuladi nsapule zao, ndipo adabwera nazo kwa Aroni.
4
Tsono Aroni adalandira golideyo kumanja kwa anthuwo, ndipo adamsungunula, napanga fano la mwanawang'ombe m'chikombole. Ndipo anthu adayamba kufuula kuti, “Inu Aisraele, nayi milungu yanu imene idakutulutsani ku Ejipito.”
5
Aroniyo ataona zimenezi, adapanga guwa patsogolo pa mwanawang'ombe wagolideyo. Tsono adalengeza kuti, “Maŵa padzakhala chikondwerero cholemekeza Chauta.”
6
Choncho m'maŵa mwake, m'mamaŵa ndithu, adapereka nsembe zopsereza, nabweranso ndi nsembe zamtendere. Ndipo anthuwo adakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa, kenaka adayambanso kuvina.
7
Pamenepo Chauta adauza Mose kuti, “Fulumira, tsika phiri, chifukwa anthu ako amene udaŵatsogolera poŵatulutsa ku Ejipito aja, adziipitsa kwambiri.
8
Asiya mwamsanga zonse zija zimene ndidaŵalamula kuti azichita. Adzipangira fano la mwanawang'ombe wa golide wosungunula, ndipo alipembedza ndi kuliphera nsembe, namanena kuti, ‘Inu Aisraele, nayi milungu yanu imene idakutulutsani ku Ejipito.’ ”
9
Ndipo Chauta adaonjeza kuti, “Anthu ameneŵa ndikuŵadziŵa, ngokanika kwambiri.
10
Nchifukwa chake tsono, undileke kuti ndiŵaononge chifukwa ndili wokwiya kwambiri, koma iweyo ndidzakusandutsa mtundu waukulu wa anthu.”
11
Koma Mose adapepesa Chauta wake, nati, “Inu Chauta, chifukwa chiyani mukukwiyira anthu anu chotere, anthu amene mudaŵatulutsa mu ukapolo ku Ejipito kuja ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lamphamvu?
12
Kodi mukufuna kuti Aejipitowo azidzanena kuti, ‘Adaŵatulutsa ku Ejipito ndi cholinga choipa choti akaŵaphere ku mapiri ndi kuŵaonongeratu pa dziko lapansi?’ Ukali wanu woyaka ngati motowo ubwezeni, ndipo musaŵaononge anthu anu.
13
Kumbukirani atumiki anu aja Abrahamu, Isaki ndi Israele ndiponso zija mudaŵalonjezazi molumbira pa dzina lanu, pamene mudaŵauza kuti, ‘Ndidzakupatsani zidzukulu zambiri, zochuluka ngati nyenyezi zakuthambo. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonse limene ndidalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lao mpaka muyaya.’ ”
14
Choncho Chauta adaleka chilango choopsa chimene adaati agwetsere anthu akewo.
15
Mose adabwerera natsika phiri atanyamula miyala iŵiri ija yaumboni, yolembedwa mbali zonse ziŵiri.
16
Imeneyi inali ntchito ya Mulungu, ndipo zolembedwazo adaalemba ndi Mulungu mwini mozizokota pamiyalapo.
17
Tsono Yoswa adamva anthu akufuula, nauza Mose kuti, “Ndikumva phokoso lankhondo kumahemako.”
18
Koma Mose adati, “Phokoso limenelo silikumveka ngati phokoso la opambana pa nkhondo, kapenanso kulira kwa ogonjetsedwa. Ndikumva phokoso la kuimba.”
19
Mose atafika pafupi ndi mahema aja, ndi kuwona mwanawang'ombe uja ndi anthu ovina, adakalipa kwambiri. Adaponya pansi miyala inali m'manja mwake ija, naiphwanya patsinde pa phiri paja.
20
Pomwepo adakatenga mwanawang'ombe amene Aroni adapanga, namperapera ngati ufa, ndipo adakamtaya m'madzi. Tsono Aisraele aja adaŵamwetsa madziwo.
21
Kenaka Mose adafunsa Aroni uja kuti, “Kodi anthu ameneŵa adakuchita zotani iwe, kuti uŵachimwitse koopsa chotere?”
22
Aroni adayankha kuti, “Musakwiyire ine mbuyanga. Mumaŵadziŵa anthu ameneŵa kuti ngovuta.
23
Iwoŵa adandiwuza kuti, ‘Tipangireni milungu yoti ititsogolere ife, chifukwa sitikudziŵa chomwe chamgwera Mose, amene adatitsogolera potitulutsa ku Ejipito.’
24
Tsono ine ndidaŵauza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi golide abwere naye.’ Ndipo amene anali nazo zinthu zopangidwa ndi golide adandipatsa. Ndidaziponya pa moto, ndipo ndidapanga fano la mwanawang'ombe lija.”
25
Mose adaonadi kuti anthuwo ngosokonezeka, (chifukwa Aroni adaaŵalekerera, mpaka iwo kusanduka anthu oŵanyodola pakati pa adani ao).
26
Moseyo adaimirira pa chipata cha mahema aja ndipo adafuula mokweza nafunsa kuti, “Kodi ndani akufuna Chauta? Bwerani kuno.” Pompo Alevi onse adadzasonkhana kwa iye,
27
ndipo Mose adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Aliyense mwa inu atenge lupanga, ndipo mupite ku mahema ndi kuloŵa m'zipata zonse. Aliyense mwa inu akaphe mbale wake kapena bwenzi lake kapena mnansi.’ ”
28
Aleviwo adachitadi monga momwe Mose adaŵalamulira, ndipo amuna 3,000 adaphedwa pa tsiku limenelo.
29
Apo Mose adauza Aleviwo kuti, “Lero lino mwadzipatula nokha kuti mukhale ansembe otumikira Chauta, pakupha ana anu ndi abale anu omwe. Motero Chauta akudalitsani lero.”
30
M'maŵa mwake Mose adauza anthu kuti, “Inu mudachimwa koopsa. Koma tsopano ndidzapita kwa Chauta ku phiri, ndipo nditakupemphererani, kapena angathe kukukhululukirani machimo anu.”
31
Tsono Mose adabwerera kwa Chauta nakanena kuti, “Anthu aŵa adachimwa koopsa. Adadzipangira milungu yagolide.
32
Koma tsopano, chonde muŵakhululukire machimo ao. Mukapanda kuŵakhululukira, chonde mufafanize dzina langa m'buku m'mene mudalemba.”
33
Apo Chauta adauza Mose kuti, “Yekhayo amene wandilakwira Ine, ndiye amene ndidzachotse dzina lake m'buku langa.
34
Tsopano pita uŵatsogolere anthuwo ku malo amene ndidakuuza. Kumbukira kuti mngelo wanga adzakutsogolera, koma tsiku likubwera limene ndidzaŵalange iwowo chifukwa cha machimo ao.”
35
Motero Chauta adatumiza nthenda pa anthuwo, chifukwa choti adakakamiza Aroni kuti aŵapangire fano la mwanawang'ombe.
← Chapter 31
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 33 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→