bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 6
Exodus 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 7 →
1
Chauta adauza Moseyo kuti, “Uwona tsopano zimene ndimchite Farao. Ndidzakakamiza Farao kuti atulutse anthu anga m'dziko lake. Ndithudi, adzaŵatulutsiratu m'dzikomo, chifukwa ndidzamkakamiza ndi dzanja langa lamphamvu. Zoonadi, dzanja langa lamphamvu lidzamuumiriza kuti aŵapirikitse.”
2
Mulungu adalankhula ndi Mose namuuza kuti, “Ine ndine Chauta.
3
Ndidaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobe ngati Mulungu Mphambe, koma sindidaŵadziŵitse dzina langa kuti ndine Chauta.
4
Ndidachita nawo chipangano ndi kuŵalonjeza kuti ndidzaŵapatsa dziko la Kanani, momwe adakhalamo kale ngati alendo.
5
Tsopano ndamva kudandaula kwa Aisraele, amene ali mu ukapolo wa Aejipito, ndipo ndakumbukira chipangano changa.
6
Tsono iwe ukaŵauze Aisraele mau anga oti, ‘Ine ndine Chauta. Ndidzakutulutsani mu ukapolo wa ntchito yakalavulagaga imene Aejipito akukukakamizani kuigwira. Ndidzakupulumutsani ndi dzanja langa lotambalitsa ndiponso pochita ntchito zamphamvu.
7
Inu mudzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Mudzazindikira kuti ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakupulumutsani ku ntchito yakalavulagaga imene Aejipito akukukakamizani kuigwira.
8
Ndipo ndidzakufikitsani ku dziko limene ndidalumbira kuti ndidzapatsa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Ndidzakupatsani dziko limenelo kuti likhale lanulanu. Ine ndine Chauta.’ ”
9
Mose adauza Aisraele zimenezi, koma iwo sadamvere, chifukwa choti anali atataya kale mtima, pomakhala mu ukapolo wao mwankhalwe chotere.
10
Tsono Chauta adauza Mose kuti,
11
“Pita kamuuze Farao, mfumu ya ku Ejipito, kuti aŵalole Aisraele kutuluka m'dziko mwake.”
12
Koma Mose adauza Chauta kuti, “Ngati Aisraele enieniwo sandimvera ine, nanji Farao angandimvere bwanji? Inetu paja sindikhoza kulankhula bwino.”
13
Koma Chauta adalamula Mose ndi Aroni kuti akauze Aisraele ndi Farao mfumu ya ku Ejipito, kuti Aisraelewo ayenera kutuluka m'dziko la Ejipito.
14
Naŵa atsogoleri a mabanja a makolo ao. Ana a Rubeni, mwana wachisamba wa Israele, anali aŵa: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Ameneŵa ndiwo a m'banja la Rubeni.
15
Ana a Simeoni naŵa: Yemuwele, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shaulo mwana wa kwa mkazi wa ku Kanani. Ameneŵa ndiwo a m'banja la Simeoni.
16
Maina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zao naŵa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Leviyo adakhala zaka 137 ali moyo.
17
Ana a Geresoni naŵa: Libini ndi Simeyi pamodzi ndi mabanja ao.
18
Ana a Kohati naŵa: Amuramu, Izihara, Hebroni ndi Uziyele. Kohati adakhala zaka 133 ali moyo.
19
Ana a Merari naŵa: Mali ndi Musi. Ameneŵa ndiwo mabanja a Levi pamodzi ndi zidzukulu zao.
20
Amuramu adakwatira mlongo wa bambo wake dzina lake Yokebede. Yokebedeyo adabala Aroni ndi Mose. Amuramu adakhala zaka 137 ali moyo.
21
Ana a Izihara naŵa: Kora, Nefegi ndi Zikiri.
22
Ana a Uziyele naŵa: Misaele, Elizafani ndi Sitiri.
23
Aroni adakwatira Eliseba mwana wa Aminadabu, ndipo mlongo wake anali Nasoni. Eliseba adabala Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.
24
Ana a Kora naŵa: Asiri, Elikana ndi Abiyasafu. Ameneŵa ndiwo mabanja a Kora.
25
Eleazara mwana wa Aroni adakwatira mmodzi mwa ana a Putiyele, amene adamubalira Finehasi. Ameneŵa ndiwo atsogoleri a mabanja a Alevi malinga ndi mafuko ao.
26
Mose ndi Aroni ndi omwe aja amene Chauta adaŵauza kuti, “Atulutseni Aisraele m'dziko la Ejipito mwa magulumagulu.”
27
Ameneŵa ndiwo ankauza Farao mfumu ya ku Ejipito kuti atulutse Aisraele ku Ejipito.
28
Pamene Chauta adalankhula ndi Mose ku dziko la Ejipito,
29
adati “Ine ndine Chauta. Ukamuuze Farao, mfumu ya ku Ejipito, zonse zimene ndikuuze.”
30
Koma Mose adauza Chauta kuti, “Inu mukudziŵa kuti paja ndine wosakhoza kulankhula, nanga Faraoyo adzandimvera bwanji?”
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→