bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 20
Exodus 20
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 21 →
1
Tsono Mulungu adalankhula mau onseŵa, adati,
2
“Ine ndine Chauta Mulungu wako, amene ndidakutulutsa mu ukapolo ku dziko la Ejipito.
3
“Usakhale ndi milungu ina, koma Ine ndekha.
4
“Usadzipangire fano kapena chithunzi chilichonse chofanizira kanthu kena kalikonse kakumwamba kapena ka pa dziko lapansi, kapenanso ka m'madzi a pansi pa dziko.
5
Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
6
Komatu anthu ambirimbiri a mibadwo yosaŵerengeka amene amandikonda, namatsata malamulo anga, ndimaŵakonda ndi chikondi chosasinthika.
7
“Usatchule pachabe dzina la Chauta, Mulungu wako, chifukwa Mulunguyo sadzamleka aliyense wotchula pachabe dzina lakelo.
8
“Uzikumbukira tsiku la Sabata, uzilisunga loyera.
9
Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito zako zonse.
10
Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata loperekedwa kwa Chauta, Mulungu wako. Usamagwira ntchito pa tsiku limenelo iweyo, kapena ana ako, kapena antchito ako, kapena zoŵeta zako, kapena mlendo amene amakhala m'mudzi mwako.
11
Paja pa masiku asanu ndi limodzi Chauta adalenga zonse zakumwamba, za pa dziko lapansi, nyanja ndi zinthu zonse zam'menemo, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adapumula. Nchifukwa chake Chauta adadalitsa tsiku la Sabata, nalisandutsa loyera.
12
“Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.
13
“Usaphe.”
14
“Usachite chigololo.”
15
“Usabe.”
16
“Usachite umboni womnamizira mnzako.”
17
“Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.”
18
Anthu onse ankamva mabingu ndi kulira kwa lipenga, namaona mphezi ndi utsi paphiripo, ndipo ankaopa ndi kunjenjemera, ataima kutali.
19
Adauza Mose kuti, “Muzilankhula ndi ife ndinu, ndipo tidzamva. Mulungu asalankhule nafe, kuti tingafe.”
20
Apo Mose adaŵayankha kuti, “Musaope, Mulungu wafika kuti akuyeseni, kuti muzimuwopa m'mitima mwanu, ndiponso kuti musachimwe.”
21
Koma anthu ankaima kutali, Mose yekha ndiye adayandikira mtambo wamdima m'mene munali Mulungu.
22
Ndipo Chauta adalamula Mose kuti, “Kauze Aisraele kuti, ‘Mwapenyatu kuti Ine Mulungu ndalankhula nanu ndili kumwamba.
23
Musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide, kuti muziipembedzera kumodzi ndi Ine.
24
Mundimangire guwa ladothi, ndipo pamenepo muziperekapo nsembe zanu zopsereza, ndi zopereka zanu zamtendere, nkhosa ndi ng'ombe zanu. Pa malo onse amene ndikuuzani kuti muzindipembedzerapo, Ine ndidzabwera kudzakudalitsani.
25
Mukadzandimangira guwa lamiyala, miyala yake musadzaseme, chifukwa mukadzaisema ndi chitsulo chosemera, mudzaipitsa guwalo.
26
Popita ku guwa langa, musadzaponde pa makwerero, kuti maliseche anu angaonekere.’ ”
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40