bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 22
Exodus 22
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 23 →
1
“Munthu akaba ng'ombe kapena nkhosa, nkuipha kapena kuigulitsa, alipire ng'ombe zisanu pa ng'ombe imodzi, kapena nkhosa zinai pa nkhosa imodzi.
2
“Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo ikanthidwa nkufa, asalipsire magazi chifukwa cha mbalayo.
3
Koma ikaphedwa dzuŵa litatuluka, apo padzakhala kulipsira magazi. Pajatu wakuba aliyense ayenera kulipira ndithu. Ngati mbala igwidwa, ndipo ilephera kulipira mlandu, aigulitse chifukwa cha kubako.
4
Ngati chinthu yabacho chipezeka chamoyo m'manja mwake, kaya ndi ng'ombe, kaya ndi bulu, kaya ndi nkhosa, mbalayo ilipire moŵirikiza.
5
“Munthu akamalekerera zoŵeta zake kuloŵa m'munda mwa munthu wina ndi kukadya mbeu za m'mundamo, mwini zoŵetayo alipire mbeu zabwino kwambiri za m'munda mwake, kapena mphesa zake zabwino kwambiri.
6
“Moto ukabuka mpaka kukafika ku thengo, ndipo ukatentha mulu wa tirigu kapena tirigu wosadula kapena munda umene uli ndi mbeu, amene adatenthayo alipire zoonongekazo.
7
“Munthu akasungiza mnzake ndalama kapena zina zamtengowapatali, ndipo zibedwa m'nyumba mwa munthumo, mbalayo ilipire moŵirikiza.
8
Mbalayo ikapanda kupezeka, mwini nyumba uja atengedwe ndi kufika naye pamaso pa Mulungu, kuti ziwoneke ngati katunduyo sadatenge ndi iyeyo.
9
“Pakakhala mkangano wina uliwonse pa za chinthu cha mwiniwake kaya ndi ng'ombe, bulu, nkhosa, zovala kapena china chilichonse chotayika, chimene wina akuti nchake, anthu aŵiriwo abwere nawo pamaso pa Mulungu. Amene Mulungu ampeze kuti ndiye wolakwa, adzalipira mnzakeyo moŵirikiza.
10
“Munthu akapereka ng'ombe, nkhosa kapena choŵeta chilichonse kwa munthu wina kuti amsungire, tsono choŵeta chija nkufa, kapena kupweteka kapena kutengedwa, wina osaona,
11
zitsimikizike pakulumbiritsa wosungayo pamaso pa Chauta kuti sadatenge chamwinicho. Ngati sichidabedwe, mwini wakeyo adzangoti zagwa zatha, ndipo wosungayo asalipire.
12
Koma ngati choŵetacho chidabedwa, mwiniwakeyo adzalipidwa.
13
Ngati chidajiwa ndi zilombo, atengeko zotsalira zake kuti zikhale mboni, koma asalipire chimene chidajiwa ndi zilombocho.
14
“Munthu akabwereka choŵeta kwa mnzake, tsono choŵeta chija nkupweteka mpaka kufa pamene sichili kwa mwiniwakeyo, wobwerekayo alipire ndithu choŵetacho.
15
Koma ngati chili kwa mwiniwakeyo, wobwereka uja asalipire. Choŵetacho akachibwereka, tsono nkuwonongeka, mtengo wolipira pobwereka ndiwo udzakonze mlanduwo.
16
“Munthu akanyenga namwali wosadziŵa mwamuna, yemwe sanatomeredwe, nagona naye, alipire chiwongo, ndipo amkwatire.
17
Koma ngati bambo wake wa namwaliyo akana kuti mwana wakeyo asakwatiwe, munthuyo adzangolipirabe ndalama za chiwongo cha namwali.
18
“Munthu wamkazi wochita zaufiti, musamlole kuti akhale moyo.
19
“Aliyense wogona ndi nyama aphedwe basi.
20
“Aliyense wopereka nsembe kwa milungu, osati kwa Chauta yekha, aphedwe ameneyo.
21
“Musazunze mlendo kapena kumkhalitsa m'phanthi, poti paja inunso munali alendo ku dziko la Ejipito.
22
Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye.
23
Mukamaŵazunza, Ine ndidzaŵamva iwowo akamalira kwa Ine.
24
Ndidzakukwiyirani, ndipo ndidzakuphani ku nkhondo. Akazi anu adzasanduka amasiye, ndipo ana anunso adzasanduka amasiye.
25
“Mukakongoza ndalama munthu wina aliyense waumphaŵi pakati panupo, musamachita monga momwe amachitira anthu okongoza, musamuumirize kupereka chiwongoladzanja.
26
Mukatenga mwinjiro wa munthu wina ngati chigwiriro kuti adzakulipireni, muubweze dzuŵa lisanaloŵe,
27
poti chofunda nchokhacho, ndicho chotetezera thupi lake. Nanga adzafunda chiyani? Akalira kwa Ine iyeyu kuti ndimthandize, ndidzamuyankha chifukwa ndine wachifundo.
28
“Musanyoze Mulungu, ndipo musatemberere mtsogoleri wa anthu anu.
29
“Musachedwe kundipatsa zopereka zotapa pa zokolola zanu zambiri ndiponso pa vinyo wanu wochuluka. “Mundipatse ana anu achisamba aamuna.
30
Mundipatsenso ana oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi nkhosa zanu. Mwana woyamba kubadwayo adzangokhala ndi mai wake masiku asanu ndi aŵiri, ndipo mudzampereka kwa Ine pa tsiku lachisanu ndi chitatu.
31
“Mudzakhale anthu operekedwa kwa Ine. Motero musadzadye nyama ya choŵeta chilichonse chojiwa ndi zilombo ku thengo. Nyama imeneyo mudzapatse agalu.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→