bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 9
Exodus 9
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 10 →
1
Pambuyo pake Chauta adalamula Mose kuti, “Pita kwa Farao ukamuuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, akunena kuti uŵalole anthu anga apite akandipembedze.
2
Koma ukakananso kuŵalola kuti apite, ndi kuŵaletsa ndithu,
3
dzanja la Chauta lidzakulanga ndi mliri woopsa pa zoŵeta zako monga akavalo, abulu, ngamira, ng'ombe, nkhosa ndi mbuzi zomwe.
4
Ndidzasiyanitsa pakati pa zoŵeta za Aisraele ndi za Aejipito. Motero palibe choŵeta nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidzafe.
5
Chauta waika nthaŵi, ndipo akunena kuti zimenezi azichita maŵa.’ ”
6
Tsono m'maŵa mwake Chauta adachitadi monga momwe adanenera, ndipo zoŵeta zonse za Aejipito zidafa. Koma panalibe choŵeta nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidafapo.
7
Ndipo Farao atafunsitsa zimene zidaachitikazo, adamva kuti palibe ndi chiŵeto nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidafapo. Komabe Farao adakhala wokanika ndithu, ndipo sadalole konse kuti anthuwo apite.
8
Pamenepo Chauta adalamula Mose ndi Aroni kuti, “Tapaniko phulusa lapamoto. Tsono Mose awaze phulusalo kumwamba pamaso pa Farao.
9
Phulusalo lidzaulukira m'dziko lonse la Ejipito ngati fumbi. Ndipo konse kumene lidzaulukireko, kudzabuka zithupsa zomaphulika ndi kusanduka zilonda pa anthu ndi pa nyama zomwe.”
10
Choncho Mose adatapa phulusalo pa moto ndipo adakaimirira pamaso pa Farao. Adawaza phulusalo kumwamba, ndipo padabuka zithupsa zimene zidaphulika ndi kusanduka zilonda pa anthu ndi pa nyama zomwe.
11
Amatsenga aja sadathenso kufika pamaso pa Mose chifukwa iwonso anali ndi zithupsa zokhazokha, monga Aejipito onse.
12
Koma Mulungu adamuumitsa mtima Farao, ndipo Faraoyo sadaŵalole anthuwo kuti apite monga momwe Chauta adaauzira Mose muja.
13
Apo Chauta adauza Mose kuti, “Maŵa m'mamaŵa upite ukakumane ndi Farao, ukamuuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, akunena kuti uŵalole anthu anga kuti apite, akandipembedze.
14
Tsopano ndikuti ndigwetsere miliri yanga yonse pa iwe, pa nduna zako, ndi pa anthu ako, ndipo udzadziŵa kuti palibe wina aliyense wofanafana ndi Ine pa dziko lonse lapansi.
15
Ndikadasamula dzanja langa kuti ndikumenye iwe pamodzi ndi anthu ako, bwenzi tsopano nonsenu mutatha.
16
Koma ndakusungani ndi moyo kuti muwone mphamvu zanga, kuti mbiri yanga iwande pa dziko lonse lapansi.
17
Koma ukunyozabe anthu anga, osafuna kuŵalola kuti apite.
18
Imvani tsono, nthaŵi yomwe ino maŵa, ndidzagwetsa matalala amphamvu amene sanagwepo nkale lonse mu Ejipito muno chiyambire cha dziko lino.
19
Tsopano lamula kuti zoŵeta zanu zonse zikhale m'khola pamodzi ndi zonse zimene muli nazo. Matalala adzagwa pa anthu ndi pa nyama zonse zongoyenda pa bwalo, chifukwa chosaziloŵetsa m'khola, ndipo zonsezo zidzafa.’ ”
20
Nduna zina za Farao zidachita mantha chifukwa cha mau amene adanena Chauta, ndipo zidatsekera akapolo ao m'nyumba pamodzi ndi zoŵeta zao zomwe.
21
Komabe ena sadasamaleko zimene Chauta adanenazo, ndipo adangosiya panja akapolo ao pamodzi ndi zoŵeta zomwe.
22
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Kweza dzanja lako kumwamba, ndipo matalala adzagwa pa anthu, pa nyama, ndi pa zomera zonse zam'minda, m'dziko lonse la Ejipito.”
23
Mose adakweza ndodo yake kumwamba. Pompo Chauta adatumiza mabingu ndi matalala, ndipo mphezi zidaomba pa nthaka. Chauta adagwetsa matalala pa dziko la Ejipito.
24
Ndipo panali mvula yamatalala ndi mphezi zong'anima kwambiri. Matalala ake anali oopsa kwambiri, kotero kuti chiyambire pamene Aejipito adasanduka mtundu wa anthu oima paokha, matalala otere sadagwepo.
25
Matalalawo adaononga zonse zokhala panja m'dziko lonse la Ejipito, anthu onse pamodzi ndi nyama zomwe. Adaononganso zomera zonse zam'minda ndi kukadzulanso mitengo yonse.
26
Dziko la Goseni lokha, kumene kunkakhala Aisraele, matalalawo sadagweko mpang'ono pomwe.
27
Pamenepo Farao adaitana Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Zoonadi, ndachimwa ndithu tsopano. Chauta ndi wolungama, koma ineyo pamodzi ndi anthu anga, tonse ndife ochimwa.
28
Pemphera kwa Chauta kuti aŵaletse mabingu ndi matalalaŵa ndipo ndidzakulolani kuti mupite. Simudzakhalanso kuno ai.”
29
Mose adamuuza kuti, “Ndikangotuluka mumzinda muno, ndikweza manja anga kwa Chauta. Tsono mabingu ndi matalala aleka, kuti inuyo mudziŵe kuti dziko lonse lapansi ndi la Chauta.
30
Komabe ndikudziŵa kuti inu ndi nduna zanu simukuwopa Chauta.”
31
Ndipo thonje lidaonongeka pamodzi ndi barele yemwe, chifukwa choti bareleyo anali atacha, ndipo thonjelo linali ndi nkhunje.
32
Koma tirigu ndi rayi sizidaonongeke, chifukwa zimenezi amabzala mochedwa.
33
Mose adachoka kwa Farao kuja, natuluka mumzindamo. Ndipo adakweza manja ake kumwamba, napemphera kwa Chauta. Tsono mabingu aja ndi matalala adaleka, ndipo mvula idakata.
34
Farao ataona kuti mvula, matalala ndi mabingu, zonsezo zaleka, adakhala wokanikabe, nauma ndithu mtima iyeyo ndi nduna zake zija.
35
Adakhala wokanika kwambiri, ndipo sadalole kuti Aisraele apite monga momwe Chauta adaauzira Mose muja.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
Recommended Reading
Commentary
Exodus Commentaries
→
Devotional
Exodus Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→