bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 18
Exodus 18
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 19 →
1
Yetero, wansembe wa ku Midiyani, mpongozi wake wa Mose, adamva zonse zija zimene Mulungu adachitira Mose ndiponso anthu ake Aisraele. Adamvanso za m'mene Chauta adaŵatulutsira ku Ejipito.
2
Motero adabwera ndi Zipora, mkazi wa Mose, amene Moseyo anali atamsiya.
3
Yetero adabweranso ndi ana aamuna aŵiri aja a Zipora. Mwana woyamba Mose adaamutcha Geresomo (chifukwa adati, “Ndakhala mlendo m'dziko lachilendo.”)
4
Mwana wake wachiŵiri Mose adaamutcha Eliyezere, (chifukwa adati, “Mulungu wa atate anga ndiye thandizo langa, ndipo adandipulumutsa ku lupanga la Farao.”)
5
Yeteroyo adabwera ndi mkazi wa Mose ndi ana ake aamuna kuchipululu kuja, ku malo amene Mose adamangako mahema, pa phiri la Mulungu.
6
Munthu wina adakauza Mose kuti, “Mpongozi wanu Yetero akubwera ndi mkazi wanu ndi ana anu aŵiri aamuna.”
7
Tsono Mose adamchingamira nakakumana naye, ndipo adamgwadira ndi kumumpsompsona. Atalonjerana ndi kufunsana za moyo, adakaloŵa mu hema.
8
Ndipo Mose adamufotokozera zonse zimene Chauta adamchita Farao ndi Aejipito chifukwa cha Aisraelewo. Adamsimbiranso za mavuto omwe adaakumana nawo pa njira, ndi zonse zimene Chauta adaachita poŵapulumutsa.
9
Yetero adakondwa kwambiri ndi ntchito zabwino zimene Chauta adaachitira Aisraele pakuŵapulumutsa kwa Aejipito.
10
Tsono adati, “Mtamandeni Chauta amene adakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa Farao. Mtamandeni Chauta amene adapulumutsa anthu ake ku ukapolo wa Aejipito.
11
Tsopano ndikudziŵa kuti Chauta ndi wamkulu kupambana milungu ina yonse, chifukwa adapulumutsa Aisraele kwa Aejipito, pamene Aejipitowo ankaŵanyoza.”
12
Pamenepo Yetero adapereka kwa Mulungu nsembe yopsereza ndi nsembe zinanso. Kenaka Aroni ndi atsogoleri a Aisraele adabwera pamaso pa Mulungu kudzadya pamodzi ndi Yetero mpongozi wa Mose.
13
M'maŵa mwake Mose adayamba kuweruza milandu ya anthu. Ndipo anthuwo ankabwera ndi milandu yao kwa Moseyo kuyambira m'maŵa mpaka usiku.
14
Yetero mpongozi wake wa Mose ataona zonse zimene Moseyo ankachita, adafunsa kuti, “Kodi zonse zimene mukuchitira anthuzi nzotani? Chifukwa chiyani mukukhala nokha pano, pamene anthu akubwerabe kwa inu kuyambira m'maŵa mpaka usiku?”
15
Mose adayankha kuti, “Ndiyenera kuchita zimenezi chifukwa choti anthu amabwera kwa ine, kuti amve zimene Mulungu afuna.
16
Anthu aŵiri akamakangana, amabwera kwa ine, ndipo ndimaŵaweruza, ndi kuwona kuti wakhoza ndani. Ndipo ndimaŵauza mau a Mulungu ndi malamulo ake.”
17
Apo Yetero mpongozi wa Moseyo adati, “Simukuchita bwino ai.
18
Inu mudzafooka msanga, pamodzi ndi anthu muli nawoŵa. Ntchito imeneyi njaikulu kuposa mphamvu zanu, ndipo simungaithe nokha.
19
Tandimverani tsono, ndikulangizeni, ndipo Mulungu adzakhala nanu. Inu muyenera kuima m'malo mwa anthu pamaso pa Mulungu ndi kubwera ndi makangano ao kwa Iye.
20
Muyenera kuŵaphunzitsa mau ndi malamulo a Mulungu, ndi kuŵafotokozera m'mene azikhalira ndi m'mene azichitira.
21
Komanso sankhulani amuna anzeru, ndipo muŵaike kuti akhale atsogoleri a anthu, motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50, ena a anthu khumi chabe. Ayenera kukhala anthu oopa Mulungu, okhulupirika, ndiponso osakopeka ndi ziphuphu.
22
Iwo ndiwo aziweruza anthu nthaŵi zonse. Azibwera ndi milandu yovuta yokha kwa inu, koma timilandu ting'onoting'ono aziweruza okha. Adzakuchepetserani ntchito iwowo pakusenza katunduyo pamodzi nanu.
23
Mukachita zimenezi monga Mulungu akulamulira, simudzafooka, ndipo anthu onseŵa adzatha kumabwerera kwao, zao zonse zitakonzeka.”
24
Mose adamvera zonse zimene adanena Yetero zija.
25
Adasankha anthu anzeru pakati pa Aisraelewo ndi kuŵaika kuti akhale atsogoleri a anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50, ena a anthu khumi chabe,
26
ndipo iwowo ankaweruza anthu nthaŵi zonse. Milandu yovuta yokha ankabwera nayo kwa Mose, koma timilandu ting'onoting'ono ankangomaliza okha.
27
Tsono Yeteroyo atalaŵirana naye Mose, adabwerera kwao.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40