bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Exodus 24
Exodus 24
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 25 →
1
Mulungu adauza Mose kuti, “Bwera kwa Ine kuno ku phiri pamodzi ndi Aroni, Nadabu, Abihu ndiponso atsogoleri a Aisraele 70. Tsono mundipembedze Ine muli chapatali ndithu.
2
Mose yekha ndiye andiyandikire, koma enawo asafike pafupi. Anthu ena onse nawonso asabwere ndi Moseyo.”
3
Mose adapita kukauza anthu mau ndi malangizo onse amene Chauta adamuuza. Ndipo anthu onse adayankha kuti, “Tidzachita zonse zimene Chauta wanena.”
4
Apo Mose adalemba mau onse a Chauta. Ndipo adadzuka m'maŵa ndithu nayamba kumanga guwa patsinde pa phiri. Kenaka adaimiritsa miyala khumi ndi iŵiri ya mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele.
5
Tsono adatuma Aisraele achinyamata kuti iwoŵa apereke nsembe zopsereza, ndi kupha ng'ombe kuti apereke nsembe zamtendere kwa Chauta.
6
Mose adatengako theka la magazi, naŵathira m'mbale, ndipo magazi otsala adawaza pa guwa.
7
Pambuyo pake adatenga buku lachipangano, naŵaŵerengera momveka anthuwo. Tsono anthuwo adati, “Tidzachita zonse zimene Chauta walamula. Tidzamumvera Iyeyo.”
8
Apo Mose adatenga magazi am'mbale aja, nawaza anthuwo, ndipo adati, “Magazi ameneŵa ndiwo amene akutsimikiza chipangano chimene Chauta wapangana nanu pakukupatsani mau onseŵa.”
9
Tsono Mose, Aroni, Nadabu ndi Abihu ndiponso anthu 70 mwa atsogoleri aja a Aisraele, adakwera phiri,
10
ndipo adaonana ndi Mulungu wa Aisraele. Pansi pa mapazi ake panali china chooneka ngati mseu wopangidwa ndi mwala wa safiro woyalidwa bwino, wa maonekedwe onga thambo.
11
Mulungu sadaŵaononge atsogoleri a Aisraelewo. Iwowo adampenyadi Mulungu, kenaka adadya ndi kumwa.
12
Chauta adauza Mose kuti, “Bwera kwa Ine kuphiri kuno, ndipo udikire konkuno. Ndidzakupatsa miyala imene ndalembapo malamulo, kuti ndiphunzitse anthu.”
13
Apo Mose adanyamuka pamodzi ndi mtumiki wake Yoswa, ndipo Moseyo adakwera phiri la Mulungu.
14
Iyeyo anali atauza atsogoleri aja kuti, “Batiyembekezani pano, mpaka tidzakupezeni. Aroni ndi Huri muli nawo pompano. Amene akhale ndi milandu, apite kwa iwowo.”
15
Tsono Mose adakwera phiri, ndipo phirilo lidaphimbidwa ndi mtambo.
16
Ulemerero wa Chauta udatsikira pa phiri la Sinai, ndipo lidaphimbidwa ndi mtambo masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri Chauta adaitana Mose m'kati mwa mtambomo.
17
Kwa Aisraele aja, ulemerero wa Chauta uja unkaoneka ngati malaŵi a moto pa phiri.
18
Mose adakaloŵa mumtambomo mpaka kukafika pamwamba pa phiri. Adakhala kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40